yesu, ndiye njira · 2017-02-28 · yesu amalamulira mu mpingo umodzi wowona, ngakhale kuti njira...

74
YESU, NDIYE NJIRA Kuyenda mu njirayo ya chipulumutso osakhotera ku dzanja la manja kapena la manzere. Wolemba I.A. Sadler

Upload: others

Post on 19-Jan-2020

7 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

YESU,

NDIYE NJIRA

Kuyenda mu njirayo ya

chipulumutso osakhotera ku

dzanja la manja kapena la

manzere.

Wolemba

I.A. Sadler

YESU,

NDIYE NJIRA

Wolemba

I.A. Sadler

Lachingerezi linasindikizidwa ndi Wolemba:

1 Payne Close, Chippenham,

Wiltshire, SN15 3FX, England.

Copyright, I.A. Sadler 2004.

Kusindikiza Koyamba 2002 Linasindikizidwanso 2004 Linasindikizidwa ndi Cromwell Press, Trowbridge, Wiltshire. Linatanthauzidwa ndi: Pastor Elwyn E. E. Maliwa PO Box 502, Balaka, Malawi. Cell. +265 888332761. E-mail. [email protected]. Omwe anayika ndemanga za kutathawuzira kwa Bikhuli: Pastor Norman Kalilombe.

Lotanthawuzidwa mu chi Spanish la “Yesu ndiye Njira”

“Yesu ndiye Njira” linasindikidwa mu chi Spanish ndi Gospel Mission, P.O. Box 318, Choteau, MT 59422, USA. (Tel/Fax: 406 466: e-mail: [email protected]) Copies can also be obtained in the UK from Dr Ian Sadler.

ZOLEMBEDWA MKATIMU.

Mawu Otsogolera……………………………………..……………………………….………………………. 1 Mavesi omwe agwiritsidwa ntchito. Mutu 1. Njira Yopapatiza koma Yodatsidwayo ………………………..………………………. 3 Khristu Njirayo – Kupapatizika kwa njirayo – Osati ku Dzanja La Manja kapena La Kumanzere – Kumaliza. Mutu 2. Mlengi wamphamvu Yonse………………………………………………………………… 10 Chidziwitso – Mlengi – Uphungu Wokhazikika wa Mulungu – Wamphamvu Yonse mu Chipulumutso – Luther ndi Erasmus pa ufulu wa chifuniro. Mutu 3. Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Kudziwidwa………………………………… 21 Chidziwitso – Chiyero cha Mulungu ndi Wochimwa Wolapa – Kubwera kwa Yesu – Chivomerezo chopanda Chipulumutso Chowona – Zisomo za Wopulumutsidwa Kwatsopano – Khristu Yesu Ambuyeyo – Umodzi wa Mawu Olembedwa ndi Osandulika Thupi. Mutu 4. Umboni wa Mpingo…………………………………………………………………………….… 37 Umodzi wa Okhulupirira – Mipingo yotsogozedwa ndi Mawu – Chikondi ndi Chiyanjano mwa Yesu – Kulalikidwa kwa Uthenga Wabwino – Mbiri Yokondweretsa ya Uthenga Wabwino – Mkwatibwi wa Khristu. Mutu 5. Chitsimikizo Mkati mwa Mayesero ……………………………………………………. 52 Njira za Mulungu ndi za mngwiro – Chipatso cha Uchimo – Dzanja lopereka Chilango la Ambuye – Kuyanjana ndi Khristu mu Zivutiko zake – Kulakwa kwa kuchoka pa Chowonadi – Chitsimikizo mwa Yesu - Kumbukirani Njirayo. Mutu 6. Mathero Abwino Ochokera ku Kumwamba ……………………………………..… 63 Mtima wanu Usavutike – Yerusalemu wa Kumwamba – Khalani Wosaledzera ndi Watcheru – UMulungu Wathunthu mwa Yesu.

MAWU OTSOGOLERA. Mu tsiku la lero la kukakamizidwa ndi kulemera kwa dziko lapansi pakati pa mipingo yolalikira ku Britain, pali vesi limodzi la Mawu a Mulungu lomwe likufotokoza bwino za zomwe zikuchitika. “Tawonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva Mawu a Yehova.” (Amosi 8:11). Mawu a Mulungu amawerengedwa ndipo ma ulaliki amalalikidwa kuchokera momwemo, komatu nanga kumvetsera kwa uzimu kuli kuti? Timawona mwa apo ndi apo kuti anthu akuyika Mawu a Mulunguwo mu mitima. Mawuwa ndi omwe amagwira ntchito kusintha miyoyo. Kawirikawiri timamva, koma osawazindikira; timawona koma osazindikira chomwe tikuwona. Palibe kupindula kwa uzimu komwe kunalipo masiku akale.

Mkatikati mwa izi, timapeza mzimu wa kusowa mpumulo. Ambiri a akhristu eni eni amawoneka monga Israel mu masiku a Oweruza; “ Panalibe mfumu m’Israeli masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake,” (Oweruza 21:25). Komabe, Mfumu Yesu amalamulira mu mpingo umodzi wowona, ngakhale kuti njira yake ndiyoposa kumvetsetsa kwa ife.

Chifukwa cha zinthu izi m’malingaliro athu tikufunafuna kamodzinso kuti tilembe, modalira kwathunthu pa Ambuye, ndi kupempheranso kuti bukhu ili lipangidwe kukhala dalitso kwa ochepa a anthu okondedwa ake. Mu bukhu lathu la m’mbuyomo “Chinsinsicho, Babulo Wamkulu” tinayesayesa kuchenjeza za Babulo wa uzimu mkatikati mwa mayiko ndi mipingo yolalikira chowonadi. Tsopano tikumva mtolo kuti tisakhazikitse chowonadi cha mtengo wapatali cha Uthenga Wabwino chowonjezerapo. Kudziwa za kulakwa ndinso uchimo kokha sikungathe kutipulumutsa ife pa tsiku la chiweruzo. Tiyenera kudziwa ndi kumva mphamvu ya mwazi wa mtengo wapatali ya Muwomboli, Ambuye Yesu Khristu. Ndi mwa Yesu yekha momwe padzakhale chitsitsimutso m’mipingo yathu.

Tiri ndi udindo wakuti bukhu ili lisalembedwe mu ndondomeko ya (chiphunzitso cha) mpingo wina uli wonse. Pali Mpingo wa uzimu umodzi, Mbusa wa uMulungu m’modzi, ngakhale kuti pali makola osiyana a nkhosa. Ngakhale pali kusiyana mu zinthu zina, Mpingo wowona wa Khristu, wolumikizika pamodzi ku Mpesa wamoyo, udzagwirizana pa maziko ndi zotetezera za chikhulupiriro. Tidzayenera potero kufunafuna kuti tipeze njira yoyendamo ya mkhristu ndi zokongola za Muwomboli, ndi kupempheranso kuti pakhoza kukhala dalitso lina, chenjezo, malangizo ndi chilimbikitso chomwe chi

khoza kukhala cha phindu kwa owerenga. Tikumudandawulira owerenga kuti aganizire pa zomwe zakhazikitsidwa, kuti pakhale chipatso china cha uzimu cha ku ulemerero wa Ambuye.

1

Mawu Otsogolera

Pamene tikulowa mu phunziro ili, ndakatulo iyi yakhazikitsidwa pa malingaliro athu.

Yesu, zanga Zonse, Kumwamba wapita, Iye yemwe, Ndikhazikitsapo ziyembekezo zanga; Njira yake Ndipenya, ndipo Ndiyilondola, Njira yopapatizayo, mpaka Iye Ndiona. Njira yomwe oyera aneneri anapita, Njira yotsogolera ku kusachotsedwa, Khwalala loyera la Mfumu, Ndidzapita, chifukwa njira zake zonse ndi mtendere. Iyi ndi njira yomwe ndayikhumba kwa nthawi yayitali, Ndinalira pomwe sindinaipeza iyo; Chisoni changa, Mtolo wanga zakhala izi kwa ine kwa nthawi, Chifukwa sindikadakhoza kuleka chimo. Pomwe ndinalimbana nayo mphamvu yake kwambiri, Ndinachimwa ndikuphunthwa komatu kwambirinso; Kufikira mochedwa momwe Mpulumutsi wanga ananena, “Bwera kuno, moyo, Ine ndine Njira.” Inde! Mokondwa ndidza, ndinu Mwanawankhosa wodala, Mudzanditengera kwa inu monga ndiri; China palibe koma chimo ndilo ndipereka, China palibe koma chikondi ndicho ndilandira. Apo ndidzanena kwa ochimwa ondizinga, Mpulumutsi wokonda wotani yemwe ndapeza, Ndidzaloza ku mwazi wanu wowombola, Ndi kuti, “Tawonani njira ya kwa Mulungu.” (Cennick)

Mavesi a Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito.

Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito atengedwa mu Baibulo la Chichewa lotchedwa “BUKU LOPATULIKA NDILO MAWU A MULUNGU” lomwe linasindikizidwa mu chaka cha 1997. Izi sizinachokere mu kumva kwa mtundu wina uli wonse wa

2

Mawu Otsogolera

miyambo kapena malingaliro. Wolemba bukhu anagwiritsa ntchito mamasulidwe ena a Baibulo pomwe anali mnyamata. Komatu, palibe lomwe linali ndi mamasulidwe alondola, uzimu weniweni ndi zotsatira zoyenera za uMulungu womwe uli mu chingerezi la “Authorized Version” la “king James Version” losindikizidwa mu chaka cha 1611, lomwe linagwiritsidwa ntchito polemba bukhu la chingerezi.

MUTU 1. NJIRA YOPAPATIZA KOMA YODALITSIKA

Khristu Njirayo

Patsogolo pa wina ali yense wa ife pali chosamvetsetseka chomwe chili imfa ndi umuyaya. Pali njira ziwiri; imodzi yomwe imatsogolera kwa Mulungu ndi moyo wosatha, ndi imodzi yomwe imatsogolera ku Gahena ndi chilango chosatha. Tisowatu chisomo cha Mulungu kuti tidziwe kusiyana pakati pa njira ziwiri izi! Tiyenera kupatsidwa mzimu wapemphero kuti tifunefune njira yomwe imatsogolera ku chipulumutso cha muyaya! Tisowa kuti maso atsegulidwe ndi Mulungu kuti tidziwe njira zokondweretsa thupi zomwe zimatichotsa pa chowonadi! “Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoyipa nthawi; nawerenga thonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:24-26)

Pali chikhalidwe chokhazikika ndi chofunika chimodzi cha njira ya ku moyo wosatha, ndicho, kuti tiyenera kupezeka mwa Ambuye Yesu Khristu yekha. Timawerenga kuti wophunzira wa Yesu, Tomasi ananena kwa Yesu; “Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:5-6). Pokhapokha titalumikizidwa kwa Yesu Khristu mwa Mzimu Woyera, sitiri mu njira yamoyo wosatha. Baibulo limatsindika za Ambuye Yesu: Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pathambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12).

3

Njira Yopapatiza Koma Yodalitsika

Kotero kuti, Ambuye mwini adalankhula za njira yopapatiza. “Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka iri yatakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo ku moyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.” (Mateyu 7:13-14). Njira yopapatiza ndiyo yomwe tidzakhala ochepa onyozedwa. Ndi njira yomwe zisoni zambiri zimabukamo, yomwe ndi imodzi yomwe ili ndi masawutso ndi chizunzo komanso kulekanitsidwa ndi dziko la pansi. Koma, kodi izi zitidabwitse ife? Ambuye Yesu mwini, pomwe anali pa dziko la pansi, ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zawo; ndipo ife sitinamlemekeza.” (Yesaya 53:3). Yesu ananenanso kuti, “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mawu anga, adzasunga anunso.” (Yohane 15:20). Komabe, Ambuye anapitirira kunena mawu awa a chilimbikitso; “M’dziko la pansi mudzakhala nacho chivuto koma limbikani mtima; ndalilaka dziko la pansi Ine.“ (Yohane 16:33).

Onse omwe ali osankhidwiratu kwa muyaya mwa Khristu Yesu, “lisanakhazikike dziko la pansi,” (Aefeso 1:4) adzayenda mu njira yopapatizayi. Akhristu owona mtima, omwe anafika pa chidziwitso cha chipulumutso ndi kuti ndi olumikizidwa mwa uzimu kwa Khristu, adzasungidwa mu njira iyi; chifukwa Khristu anati, “Ine ndine njira”. Ngakhale kuti nthawi zina angathe kumva ngati si ali mwa Khristu, ndi kuti akuponderezedwa pansi mpaka pafupifupi kuwonongedwa ndi mayesero, chipulumutso chawo chimakhalabe chotetezedwa.

Zimakhala monga ngati tsiku lomwe ladzala ndi mitambo ndipo ndi la mdima; dzuwa limakhala liripo, ngakhale kwa ka nthawi limaphimbika ku maso athu. Kotero kuti, Davide akadakhoza kunena mwa chikhulupuriro kuti; “Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, Sindidzawopa choyipa; pakuti Inu muli ndi ine: Chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.” Masalmo 23:4).

Kupapatiza kwa Njirayo.

Talankhula za njira yopapatizayo; koma nanga “kupapatiza kwake ndi kotani”? Funso ili likhoza kuwoneka ngati lachilendo kulifunsa. Komabe, ili ndi funso lofunika, pakuti mipingo ina ndi okhulupirira ena amagwa m’mayesero pamenepa. Pali ngozi yakuti titha kupitirira muyeso kapena kubwerera kutali, m’malo motsatira momwe Mawu a Mulungu akunenera zokhudza nkhani iyi. Tilingalirapo pang’ono tsopano pa za nkhani iyi, koma tidzabwereranso pa phunziro ili mu mitu yotsatira.

4

Njira Yopapatiza Koma Yodalitsika

Poyamba, tiyeni tifufuze mitima yathu mokhudzana ndi chiyeso chofuna kukulitsa njira yopapatizayi. Zifukwa zambiri zikhoza kupezeka chifukwa cha ichi. Kapena timamva mkati mwathu kuti mipingo isachotseko ena a omwe angakhale ndi chidwi ndi Chikhiristu, pakuwoneka ochita zinthu mokhwimitsa kwambiri. Mu njira ina, pali mantha akuti tikhoza kutchulidwa “osamva za ena” kapena “oganiza moperewera” komabe, timawopa nthawi zonse pafupi pafupi chifukwa chomwe chili pansi pa mitima yathu kuti ndi chikondi cha dziko la pansi ndi zokondweretsa zake. Kwa ichi tiyenera kuyankha motsindika kuti ufumu wa Khristu si wa dziko lino, koma uli ufumu wa uzimu. (Yohane 18:36). Mawu a Ambuye Yesu Khristu ali omveka bwino, kuti sitingathe kugwira za dziko nthawi yomweyo ndi kumakhala moyo wakuvomereza za uMulungu. “Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Luka 16:13). Pali mavesi ena ambiri omwe angakhoze kuwonjezeredwa, koma zomwe analemba Yakobo ndi zolondola koposa pa nkhaniyi; “kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko la pansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko la pansi adziyika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4).

Ngati timamva kulasa kwa chikumbu mtima mokhudzana ndi nkhani iyi (ndipo ndi ndani amene asanalakwitsapo apa?), tiyeni mwa pemphero tilingalire chilimbikitso chokoma cha Uthenga Wabwino cha Ambuye Yesu, “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.” (Yohane 14:15). Mtumwi Yohane akuwonjeza ndi mawu akuti: “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3).

Ichi ndi chowonadi chokhazikika kuti Mulugu amalemekeza iwo omwe amalamekeza Iye (1 Samueli 2:30). Kodi nanga dzina lake lingalemekezedwe bwanji ngati tivomereza Khristu ndi milomo yathu, koma osamvera malamulo ake, zomwe zimatipangitsa kuwoneka osasiyana ndi osakhulupirira? Mtumwi Paulo adawulimbikitsa mpingo wa ku Korinto omwe udagwa mu zolakwa zambiri, “Chifukwa cha ichi, Turukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu, ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana amuna ndi akazi, anena Ambuye Wamphamvu yonse.” (2 Akorinto 6:17-18). Ambuye atithandize potipatsa mtima wolapa weniweni ndi chikhulupiriro chakuti tikhulupirire malonjezano akulu ndi a mtengo wapatali, ndipo kuti kenaka tingathe kukhala “akuchita mawu, osati akumva okha”. (Yakobo 1:2).

5

Njira Yopapatiza Koma Yodalitsika

Kufunafuna kukulitsa njira yopapatiza sikungangokhala kwakuti kungathe kuvulaza miyoyo yathu yomwe, komanso pakhoza kukhala zotsatira zosawoneka ndi maso athu zomwe zingathe kukhudza mipingo. Satana nthawi zonse ndiwokonzekera kubzyala mbewu za chisokonezo, kotero kuti amapezerapo mwayi pa kusakhwimitsa ndi kelekerera kwa chikhalidwe cha anthu. Kuti ayese iwo amene akhumudwitsidwa ndi kupepuka ndi kukhala moyo wa dziko la pansi kwa Akhristu. Zotsatira zake ndi zakuti, mayeserowo amakula kufikira kumapeto kwa mbali yotsutsa, potero njirayo imapangidwa kukhala yocheperapo kusiyana ndi momwe zinalembedwera mu Mawu a Mulungu. Makamaka ndi zotitchera msampha mu masiku ano, pomwe pali kutukuka kochepa mu zinthu za uzimu ndipo mipingo yolimba imamwazika ndi mipatuko imachitika kawirikawiri. Potsatira apo, msampha wa Satana angathe kugwira ambiri mosadziwa.

Zizindikiro zosonyeza kugwera ku mapeto kwa mbali yotsutsa kukhoza kudziwidwa pofunsa mafunso awa. Kodi timaweruza okhulupirira ovomereza chikhulupiriro chawo? Kodi ife, monga momwe zinaliri kale timawachotsa pakati pathu, ngati sakwaniritsa kukhala monga zikhalidwe zathu, miyambo ya mpingo, kavalidwe ka mtundu wina wake kapena zinthu zomwe ife takumana nazo pa moyo ndi kuzidziwa? Monga tonse timamva za kulakwitsa kochuruka, kodi nthawi yomweyo timayesa kuti iwonso sanaphunzitsidwe mowonadi za Mulungu? Ngati timavomereza kuti angathe kuwunikiridwa mu zinthu zina, kodi timawayang’anira pansi ndi mtima wakuti ndife apamwamba?

Zimakhala zomvetsa chisoni pomwe kulungamitsidwa kumafunidwa chifukwa cha zomwe timafotokoza kuti, “zowonadi njirayo ndi yopapatiza; zoonadi, akadakhala kuti anali pa njira yopapatiza akadaphunzitsidwa mosiyana; zowonadi akadakhoza kuchita monga ife tichitira, kapena akadakumana ndi zomwe ife takumana nazo?” Zowonadi momwe Yobu akanalankhula mwa mkuluwiko moyerekeza iwo, monga adachitira kwa abwenzi ake atatu omwe amamuzenga mulandu: “Zowonadi inu ndi anthu, ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.” (Yobu 12:2). Komabe, zikhoza kukhala zokumana nazo zomwe zingatitsegule maso ndi kutichepetsa kuti tizindikire kuti wina, yemwe akunyozedwa chifukwa cha mawonekedwe ake akunja, akudziwa koposa ife za chikondi cha pa abale ndiponso chitsimikizo cha chipulumutso mu moyo mwawo.

Yesero ili lingathe kuwatsogolera ena ku malingaliro akuti omwe ali opulumutsidwa ndi ochepa, komanso kuti mipingo ndi olalikira owona ndi kovuta kuti apezeke. Komabe, tiyeni tiganizire za nkhani ya Eliya. Pomwe adathawa chizunzo cha Sinai,

6

Njira Yopapatiza Koma Yodalitsika

anafunsidwa ndi Ambuye, “Uchitanji pano Eliya? Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israeli anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu ansembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha ndipo afuna moyo wanga kuwuchotsa.” (1 Mafumu 19:9-10). Ambuye anayankha, “Ndiponso ndidasiya m’Israeli anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala mawondo awo, osampsyompsyona ndi milomo yawo.” 1 Mafumu 19:18).

Chotipatsa chidwi ndi chakuti Eliya athawire ku Sinai, chomwe chikuyimira lamulo la Mose. Iwo omwe agwera mu chiyeso chonyoza ena ali pa ngozi yakuti angathe kutengedwa mkulakwa kwa Afarisi, omwe adatsatira lemba la chilamulo osakhala nacho chidziwitso cha Uthenga Wabwino wa Khristu. Paulo analankhula kwa mpingo wa Ahebri kuti; “Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsya moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe … Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuruka wa angelo, ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro, ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano,” (Ahebri 12:18-24). Kotero kuti, tipereke tanthawuzo lowona la njira yopapatiza tiyenera tifananize lemba ndi lemba, tikufunafuna chithandizo cha uMulungu cha Mzimu Woyera. Apo tidzakhoza kuyenda njira ya pakati yomwe imatsatira ndodomeko yolembedwa ya Mawu a Mulungu, posakhudza kwambiri mbali zina zomwe sizimalemekeza Mulungu.Yesaya akufotokoza bwino za njira ya moyo, ngakhale kuti zalankhulidwanso kwina mu Mawu a Mulungu monga njira yopapatiza ndi njiranso ya khwalala yomwe onse owomboledwa ndi Ambuye adzayendamo. Palibe yemwe angapereke chiwerengero cha anthu owomboledwa. Yesaya akunena, “Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; koma Iye adzakhala nawo oyenda ngakhale opusa, sadzasochera m’menemo. Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chirombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuwomboledwa adzayenda m’menemo, ndipo owomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuyimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuwusa moyo kudzachoka.” Yesaya 35:8-10)

Osati ku dzanja la Manja kapena la ku Manzere.

Izi zomwe tangozilingalira, zokhudzana ndi kusamalitsa kusadutsa malire pochita zosiyana ndi zomwe ziri m’malemba, zinalembedwa poyambirira mu chilamulo cha Mose, “Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;

7

Njira Yopapatiza Koma Yodalitsika

musamapatuka ku dzanja la mazere kapena ku la manja.” (Deuteronomo 5:32).

Komanso bukhu la Miyambo limalankhula; “Maso ako ayang’ane m’tsogolo, zikope zako zipenye mowongoka. Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke, Usapatuke ku dzanja la manja kapena ku la manzere; suntha phazi lako kusiya zoyipa.” (Miyambo 4:25-27). Pa iwo okha mavesi amenewa akadakhoza kumasulidwa molakwika, mokhala ngati akutanthauza kuti ntchito zabwino za Mkhristu ndizo zisoweka kuti asungike mu njirayo. Komabe, Yesaya akuwonjezera kufotokoza mwa mtengo wapatali. “Ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu ku la manja, ndi potembenukira ku la manzere.” (Yesaya 30:21). Izi zimalankhula modalitsa za Ambuye pa kutsogolera ndi kuwasunga anthu ake mu njira yowona iyi, komanso kuwakonza pomwe achoka mu njirayi. Potero, ntchito iri yonse ya Mkhristu imadzera kuchokera m’chisomo cha Mulungu.

Kusungika kwa anthu a Ambuye uku kumatheka mwa mphamvu ya moyo wangwiro womwe Muwomboli anakhala, yemwe ndi Ambuye Yesu Khristu. Ngakhale mu mayesero onse, zidzudzulo ndi ziwopsyezo zochokera kwa anthu ochimwa, anayenda mu njira imeneyo kufikira ku mtanda mwa kumvera Atate mwa ngwiro. Yesaya akulankhula za Khristu mu uneneri; “Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo. Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa. Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sondinasokozenedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.” (Yesaya 50:5-7).

Lamulo lingathe kuperekedwa, ndipo monga ochimwitsitsa sitingathe pa ife tokha kumvera, komatu tiri naye Muwomboli “wotha kumva chifundo ndi zofoka zathu;” (Ahebri 4:15). Paulo akudandaulira motere “popeza tizingidwa nawo mtambo wawukuru wotere wa mboni, titaye cholemetsa chiri chonse, ndi chimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwa chipiriro makaniwo adatiyikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choyikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingalirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.” (Ahebri 12:1-3). Mphamvu zathu ndi kuthekera kwathu kuti tithe kukhalabe mu njirayo zigonera kwathunthu mwa Ambuye Yesu, yemwe anayendamo kale ndipo amatsogolera anthu ake ku moyo

8

Njira Yopapatriza Koma Yodalitsika

wosatha.

Njirayo si ili mu malo okwera omwe tikhoza kuyan’anira pansi anzathu. Polekana ndi zimenezi, “Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthawi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe. Koma kudzagwa matalala m’kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.” (Yesaya 32:17-19). Kodi nanga ndi motani momwe tingatsatire Mtumwi Paulo, pomwe akunena kuti, “ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.”(Afilipi 2:3).

Tisowa kukhala wochenjezedwa nthawi zonse, kuti Satana akadatha kutiyesa kuti titembenukire kumbali potipangitsa kuyenda monga mwa dziko la pansi kapena mu changu cha chiFarisi. Potero, monga ngati chotitsutsa ku makhwekhwe a Satana, tiyeni tisinkhesinkhe pa kufotokozera kodalitsika kwa Muwomboli koperekedwa ndi mtumwi Paulo. “ Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa mayina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba ndi za pa dziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malirime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake ndiye Mulungu.” (Afilipi 2:5-13)

Kumaliza.

Titatha kulingalira zina zomwe zimafototokoza za zoyenera za njirayo, tiyenera kutembenukira mu mutu wina wa ku chowonadi chowunda mkota chokhudza umwini yekha wa Mulungu. Ichi ndicho maziko a chikhulupiriro chathu, ndipo chili ndi chitonthozo chachikulu. Maziko awa akayalidwa, tidzakhoza kenaka kufunafuna kuti tipitirire kupeza zina zonena kuti mkhristu amakhala wotani komanso zokhudza kuyenda mu njira yopapatizayo.

9

Njira Yopapatiza Koma Yopapatiza Tiyeni tifunse funso lofunika, (Abale, musakhale otetezedwa kwambiri) Chomwe chitanthauza kukhala Mkhristu, Momwe mitima yathu tingatsimikizire. Modzikweza tidzikweza m’mapembedzedwe, Ngati pa maziko onama tinamangidwa; Chipembedzo chowona choposa maganizo; China chake chiyenera kudziwidwa ndi kuchimva. (Hart)

MUTU 2. MLENGI WA MPHAMVU YONSE

Chidziwitso.

Pa mutu woyamba tinawona za zinthu zina zofunika zokhudza njirayo. Tsopano tilingalire za funso lakuti: Kodi ndani yemwe amamukhazika Mkhristu mu mpingo? Ili ndi phunziro lofunika, komanso lobweretsa mtsutsano. Tiyenera tsopano kufunafuna kuti tiyende kuchoka pa mfundo kufika pa mfundo ina mosamalitsa ndithu ndiponso mwakuyenera kupereka ulemu.

Kufunika kwa funso, ili kukuwoneka, pomwe tizindikra matamando, ulemu ndi ulemerero womwe uyenera iye wolemba ndi woyambitsa wa ntchito imeneyi. Kotero kuti, ndi gawo la zolembedwa, pamene wolemba, osati wosindikiza amalandira kudziwika zaka zambiri zitapita iye atamwalira. Awa ndi mafotokozedwe a dziko la pansi a chowonadi chachikulu chauzimu. Iye ndiye wodzetsa chipulumutso, chomwe chiyenera kutamandidwa ndi kulemekezedwa ku nthawi zamuyaya.

Tsopano tiyeni tidzifunse tokha: kodi chotipangitsa kuti tipulumuke ndi chiyani, ndi kuti nanga zidatheka bwanji kuti tipezeke mu njirayo monga Akhristu? Kodi ndi chifukwa chakuti tasankha Khristu? Kodi tinasankha kudzipereka tokha kwa Iye? Kodi timapanga chisankho chabwino kwambiri cha miyoyo yathu? Ngati yankho lathu ndi

10

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

lakuti inde, ndiye ulemu ukhale pa ife. Koma ngati ziri choncho, nanga uli kuti ulemerero woyenera kupita kwa Mulungu? Komabe, Ambuye akulengeza: “Tawona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m’ng’anjo ya masawutso. Chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.” (Yesaya 48:10-11).

Tikunenanso kuti, ngati chipulumutso chimafika kwa ife potsatira kulingalira ndi kusankha kwathu, ndiye kuti munthu ndiye yemwe ayenera kulandira ulemu ndi ulemerero. Koma Mawu a Mulungu akulankhula motere za Yesu Khristu: “Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa zina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba, ndi za pa dziko, ndi pansi pa dziko, ndi malilime onse avomereze kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11). Chimodzimodzinso Paulo akulankhula kwa anthu a mpingo wa ku Kolose, “kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.” (Akolose 1:18).

Ambuye analemba mu Baibulo zitsimikizo zambiri zonena za uMulungu wa mphamvu yonse kumwamba ndi pa dziko la pansi ndipo zina za zolembedwazo ndi zomwe tizilingalire tsopano. Komatu tiyeneranso kukumbukira kuti malembo amalankhula za kuti munthu ali ndi udindo komanso kufotokozapo za moyo wake. Pali mawu ambiri olimbikitsa m’malembo okhudza za machitidwe a uMulungu, zomwe za izo tidzazifotokoza zambiri mu mitu yotsatira. Kotero kuti, tiyeni tifunefunenso mwa Mzimu Woyera kufananiza lemba ku lemba.

Mlengi.

Sitikhoza kumvetsetsa mowona za Mulungu mwini yekha, kapena mphamvu za uMulungu, pokhapokha titakhulupirira kuti Iye ndi Mlengi wa dziko lonse ndi kumwamba. Pa chilengedwe ndi pomwe timawona kuti Mulungu ndi wosafanana ndi wina ali yense kapena china chili chonse. Munthu angathe kupanga zinthu zovuta kuzimvetsa kapenanso zokongola, koma amapanga zonsezo kuchokera mu zinthu zomwe wapatsidwa. Komatu pomwe Mulungu adalenga zinthu zonsezi komanso moyo mosachokera ku china chirichonse.

Nkhani zophunzitsidwa za kusintha kwa zinthu pa kupita kwa nyengo zimakhudza kwambiri ku maziko ofunika kwambiri a chikhulupiriro chowona. Kukadakhala kuti dziko komanso moyo sizinalengedwe, koma kuti zidangobuka kuturuka mu madongosolo ochitika a chilengedwe, ndiye Baibulo linayamba ndi kunena za bodza. Tiyeni tilingalire mosamalitsa mawu awa omwe Paulo analankhula ku mpingo wa ku

11

Mlengi Wa Mphamvu Yonse.

Kolose, “ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nawo cholowa cha oyera mtima m’kuwunika; amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tiri nawo mawomboledwe mwa Iye, m’kukhululukidwa kwa zochimwa zathu; amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse, pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zowoneka ndi zosaoneka, kapena mipando yachifumu, kapena Mawufumu, kapena ma ukulu, kapena ma ulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye. Ndipo, Iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba woturuka kwa mwa akufa, kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.” (Akolose 1:12-18). Tikuwona kuchokera ku mawu awa omwe akufotokoza za momwe Ambuye Yesu Khristu adagwirira nawo limodzi ntchito pafupi kwambiri ya kulenga.

Ngati kusinthika kwa chilengedwe pa kupita kwa nthawi kuli kowona, ndiye kuti Yesu Khristu si Mlengi komansi si “Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza.” (Chivumbulutso 1:8). Ndiye sakanakhala Mulungu wowona, wachiwiri pa Utatu wa Umulungu. Ndiponso sipakadakhala chiwombolo kudzera mu mwazi wa Khristu, komanso chikhulukiro cha machimo. Ngakhale Afarisi ankadziwa za kulumikizana kwa chikhululukiro cha machimo ndi Mulungu. Yesu atalankhula kwa munthu wodwala, kuti machimo ako akhulukukidwa, anasinkhasinkha mwa iwo kuti, “akhoza ndani kukhulukira machimo, koma m’modzi, ndiye Mulungu?” (Marko 2:7). Kenaka Yesu anatsimikiza uMulungu wake ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo, pakuwonetsera mphamvu yake pamwamba pa chilengedwe pomwe anachita chozizwa chopambana. “Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo pa dziko la pansi (ananena ndi wodwala manjenje), ndikuwuza iwe, Nyamuka, senza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.” (Marko 2:10-11).

Ndizosavuta kuti tiwone kuti kusinthika kwa zinthu kukhala zina pakupita kwa nthawi zimakhala ndi makopedwe. Zimafuna kumukweza munthu kuti afike pamwamba pa dziko la umunthu komanso pamwamba pa chitukuko. Chilengedwe ndi nyama pa izo zokha zimayikidwa patsogolo kuti ndizo zoyambitsa moyo, ndipo zimapatsidwa ulemerero. Munthu wochimwa amafuna kukhala woyamba, ndipo samafuna kugawana ulemerero ndi wina. Kotero kuti, monga mtumwi Paulo anena, “anasandutsa chowonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira

12

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.” (Aroma 1:25).

Akhristu ambiri amayesetsa kusungabe nkhani yakuti Mulungu anagwiritsa ntchito njira ya kusinthika kwa zinthu; koma uku ndi kusokoneza mawu achimvekere a mu Baibulo. Kuseri kwake kuli chikhumbokhumbo chofuna kusalekanitsidwa ndi moyo wa dziko lochimwa ndi kukhalanso ndi “uthenga wabwino” womwe sumatsutsa osakhulupirira. Tiyeni tifotokoze momveka bwino; ngati masinthidwe a chilengedwe anachitikadi, nanga ndi chifukwa chiyani pali kugwa mu uchimo? Ngati sitidachimwe, nanga ndi chifukwa chiyani tisowa Mpulumutsi? Ngati Mulungu sanalenge dziko la pansi, ndi chifukwa chiyani pali tsiku la chiweruzo? Ngati zochitika za chilengedwe ndi zimene zinapangitsa kuti dziko likhalepo, kodi si ndiye kuti zochitika za chilengedwe zidzapangitsanso kuti dziko lithe? Mwachidule pounda mkota, ngati Mulungu sanalenge monga bukhu la Genesis lilengezera komanso malo ambiri mu Baibulo, zisonyeza kuti chikhulupiriro chomwe timayenera kukhala nacho ndi chokhazikika pa ziphunzitso zachabe.

Mwina mwake wowerenga angathe kukhala m’modzi wa ambiri, omwe amayendabe mu mtsinje wa chiphunzitso cha masinthidwe a zinthu chomwe chimaphunzitsidwa kuchokera ku umwana mpaka kukula. Ngakhale kuti umboni wa a za sayansi omwe amateteza chiphunzitso chawo cha chilengedwe monga mwa maziko a za sayansi ungathe kukhala wothandiza, apa sipoyenera kumangapo maziko a chipembedzo chathu. Zaukali za Satana komanso mitima yathu yochimwa idzapereka mwachangu zikayiko pa matsutsano abwino okhudza za sayansi, kenaka ndi kuchotsa mwa ife chitonthonzo china chiri chonse. Kotero kuti, pali yankho limodzi, ndipo ndi zotengera Mulungu mwini yekha kutipatsa ife mphotho ya mtengo wapatali ya chikhulupiriro. Ngati tikhumba kuti tiwonetsedwe chowonadi, tiyenera kuti tipemphere kwa Mulungu moona mtima kuti atipatse chikhulupiriro kuti tithe kukhulupirira pa mbiri ya uMulungu. Ambuye ali wokhulupirika kuti athe kuyankha kupemphera kapena kulira kochokera mu mtima. Titatero chikhulupiriro chathu chikhoza kupumula mwa Mulungu, osati mwa munthu. Awa ndi maziko omangidwa pa mwala, omwe adzathe kuyimabe pa nthawi ya namondwe. “Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m’mwamba omwe anakonzedwa ndi mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zowonekazo.“ (Ahebri 11:3).

Uphungu Womveka bwino ndi Wosakaikitsa wa Mulungu.

Monga momwe Mawu a Mulungu afotokozera zakuti Ambuye analenga kumwamba

13

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

ndi dziko la pansi, zikusonyeza momveka bwino kuti Iye ndi yekhayo wolamulira pa chilengedwe. Mfumu Nebukadinezara atatsitsidwa pansi, nayikidwa mu mazunzo akulu, adalengeza chowonadi cha Mulungu wa Israeli. “Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam’mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwo mibadwo; ndi okhala pa dziko la pansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake mkhamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko la pansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?” (Danieli 4:34-35).

Chomwe chili chomveka bwino kuchokera mu nkhani iyi, ndi chakuti chifuniro cha Mulungu chimapambana ngakhale patakhala kuti pali zochitika za mtundu wina uli wonse kapena nyengo zina ziri zonse. Chitsanzo chodalitsika chokhudzana ndi izi ndi chomwe chinaperekedwa cha kupachikidwa pa mtanda kwa Ambuye Yesu. Ophunzira a Ambuye Yesu samakhulupirira kuti izi zikhoza kuchitika ndipo adayesetsa kuletsa kuti izi zisachitike, osadziwa kuti chipulumutso chawo chomwe chidagonera pa nsembe ya Khristu ya pa mtanda yoperekedwa chifukwa cha chimo. Petro adafika powadzudzula Ambuye mwakunena kuti, “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai.” (Mateyu 16:22). Alembi ndi Afarisi adapanga chiwembu kuti amuphe Yesu chifukwa cha udani wawo pa chiphunzitso chake ndi mphamvu zake za uMulungu, chifukwa chimawonetsera poyera ntchito zawo zoyipa komanso kudzikweza kwawo pa zinthu za uzimu. Mkulu wa nsembe Kayafa anati, “nkokoma kwa inu kuti munthu m’modzi afere anthu” komatu samadziwa kuti ananenera chowonadi chozama. (Yohane 11:49-52). Kazembe wa Roma, Pilato yemwe sanasamalire kokwanira chilungamo, ndipo kuyesa kwina kuli konse kofuna kumasula Yesu komwe anachita kumalephereka mosavuta pomwe anthu akangomutsutsa: “Pa ichi Pilato nafuna kumumasula Iye; koma Ayuda anafuwula kunena, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara.” (Yohane 19:12). Kwa asirikali a chi Roma kupachikidwa pa mtanda kudawakondweretsa kwambiri, popeza kudawapatsa iwo mwayi wakumtoza Yesu ndi kumuchitira nkhanza zomumvetsa ululu waukulu. (Marko 15:16-20). Komatu pakati pa zifuniro zotsutsana zonsezi, zolinga ndi maonekedwe a anthu osawerengeka mumbiri yonse yoyambira kale, komanso posaganizira za zoyipa zonse zomwe Satana mwini anazibutsa, Ambuye Yesu anapachikidwa pa nthawi ndi malo omwe Mulungu adayikhazikitsa. Atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ophunzira anamvetsetsa kuti Yesu, “ameneyo anatengedwa ndi manja anthu osayeruzika”, ……… “nampachika ndi kumupha.”

14

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

(Machitidwe 2:23). Yesu ananena kwa Pilato, munthu woipa ndi wosawopa Mulungu, “Simukadakhala nao ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba;” (Yohane 19:11).

Ngakhale pomwe Ambuye Yesu anapita monga mwana wa nkhosa kukaphedwa (Yesaya 53:7), anatenga moyo wake ndipo palibe munthu yemwe anawulanda kwa Iye. (Yohane10:18). Sanaphedwe kapena kupambanidwa ndi imfa, koma anapereka moyo wake monga nsembe yomalizidwa yoperekedwa chifukwa cha machimo a nkhosa zake, anthu ake osankhika. “Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu. (Yohane 19:30). Ambuye Yesu wowuka kwa akufa anaphunzitsa mwini yekha pa njira ya Ku EmMawu; “Kodi sanayenera Khristu kumva zowawa izi ndi kulowa ulemerero wake? Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthawuzira iwo m’malembo onse zinthu za iye yekha.” (Luka 24:26-27).

Tikuwona kuti chochitika chachikulu kwambiri mu mbiri ya dziko la pansi, kufa ndi kuwuka kwa akufa kwa Yesu Khristu, mwana wa Mulungu, kunachitika monga mwa chifuniro cha Mulungu. Mbiri yonse ya dziko la pansi, imatsutsidwa ndi zotsatira za ulemu ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo chili tanthawuzo la chipulumutso kwa anthu ake okondedwa.

Mawu a Mulungu ali odzala ndi mphamvu za Mulungu mwini pa zochitika za munthu. Zitsanzo zina zambiri zingathe kusankhidwa; koma tiyeni timalize ndi mawu a mtumwi Paulo. “Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulalikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani? Ndipo adzambwezeranso? Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye , zichitika mwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.” (Aroma 11:33-36).

Wamphamvu Yonse mu Chipulumutso.

Monga momwemo kuti imfa ndi kuwuka kwa akufa kwa Yesu Khristu zinali monga mwa cholinga ndi chifuniro cha Mulungu, momwemonso ndi momwe chilili chipulumutso cha anthu osankhika a Mulungu, anthu osankhidwiratu. Timawerenga mu nkhani ya uneneri wa kuzunzika kwa Khristu ndi kuperekedwa pa mtanda, kuti “Iye adzawona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zawo.” (Yesaya 53:11). Yesu asanalowe mu Getsemane anapemphera; “Atate amene

15

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

mwandipatsa Ine; ndifuna kuti, kumene ndiri Ine; iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti Ine lisanakhazikike dziko la pansi.” (Yohane 17:24).

Ubwino ndi mphamvu za pemphero la Yesu kwa osankhidwiratu limagonera pa ubale wake ndi Mulungu atate ‘Kuti onse akhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko la pansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.” (Yohane 17:21). Umodzi wodalitsika wa utatu wa uMulungu, (Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera) umakambiridwa pa mpingo wa Khristu. Kotero kuti, chipulumutso cha mkhristu ali yense yemwe ali wobadwa kwatsopano zenizeni mwa Mzimu Woyera ndi kulumikizana ndi Khristu, ndi zochitika monga mwa uphungu womveka bwino ndiponso wosakaikitsa wa Mulungu monga waonetsedwa mu imfa ndi kuwukanso kwa Mwana wake wokondedwa.

Komabe, sitinasiyidwe pakuti tikhoza kutengapo phunziro pa zomwe ziganiziridwa ndiponso kumalizitsa koyenera pa zenizeni za chipulumutso. Malembo amalankhula mu njira zofotokozeredwa ndi kumveka bwino. “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Khristu; monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko la pansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chirema pamaso pake m’chikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake, kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake chimene anatichitira ife kwa ufulu mwa Wokondedwayo. Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.” (Aefeso 1:3-7). Mu bukhu la Machitidwe a Atumwi timapeza mafotokozedwe omveka bwino okhudzana ndi iwo adakhulupirira kulakidwa kwa Uthenga Wabwino “ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza Mawu a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anayikidwiratu ku kumoyo wosatha.” (Machitidwe 13:48).

Komabe, ndi chidziwitso cha chikhalidwe chosawopa kuchita zoyipa cha mtima wochimwa wa munthu, kotero kuti ukhoza kufunafuna kugwiritsa ntchito chiphunzitso cha uMulungu chotere monga ngati chifukwa chodzilolezera uchimo. Ichi ndi cholakwika chovuta kuzindikirika msanga chomwe chimabweretsa tsoka, pomwe mkhristu amapambanidwa chifukwa cha ulesi ndi kusasamala pa za kulakira kwa Uthenga Wabwino. Iye kenaka amasinkhasinkha kuti, pakuti chipulumutso ndi cha Mulungu yekha, sasowekanso kukhudzidwa ndi za kukhala mboni ya chisomo cha Yesu Khristu kwa anthu ena. Tibwereranso ku nkhani iyi mtsogolo mwa bukhuli.

16

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

Timalize mutu uwu poyang’ana pa chimodzi cha zosavomerezetsa chokambidwa ndi ambiri cha umwini mphamvu yekha wa Mulungu, ndicho chakuti munthu analengedwa ndi ufulu wakusankha. Poyankha izi titchula za munthu wamkulu wa Mulungu, Martin Luther. Magawaniko ochitika mu chikhristu okhudzana ndi nkhani iyi mu zaka pafupifupi 1500 zapitazo imatipwetekabe chimodzomodzi kufikira lero. Chofunika kwambiri ndicho kudziwa komwe chipulumutso chimachokera komanso njira yomwe chimafikira. Kodi tidzayendanso bwino motani, kapena kuti olalikira angalalikire bwino motani, ngati sitikumvetsetsa bwino pa mfundo iyi?

Luther ndi Erasmus pa za Ufulu Wachifuniro.

Luther ndi anthu ena Otchuka omwe anabweretsa kusintha kwa mbiri zina anaphunzitsa za mphamvu ya mwini yekha ya Mulungu pa chipulumutso, monga zidavumbulutsidwa mu Mawu a Mulungu. Ichi chipanga maziko omwe amakanizitsa ulamuliro omwe mpingo wa ku Roma umayembekezeredwa kuti uli ulamuliro m’manja mwawo pokhudza nkhani za chipulumutso cha dziko la pansi. Chiphunzitso cha iwo omwe adaphunzitsa zotsutsa ziphunzitso za chi Roma chinali chomkweza Mulungu, osati wansembe; chipulumutso cha munthu sichinagonere m’manja a wansembe kuti apereke ufulu kwa omangidwa, kapena mu ufulu pa munthu payekha wakusankha kotsatira chiphunzitso cha mpingo.

Chizindikiro cha Luther cha chipulumutso cha umwini mphamvu wa Mulungu ndi kudziwiratu kwake, anakuzindikira Erasmus, yemwe analemba bukhu la “Diatribe” lotsutsa Luther, potsindika kuti munthu anali ndi “ufulu wakusankha”. Erasmus amadziwa kuti anali wophunzira wamkulu pa nthawi ya moyo wake. Ngakhale kuti kulemba komwe analemba Chipangano Chatsopano mu chiGriki chinagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Mulungu pa nthawi yotsutsa ziphunzitso zonama, Erasmus sanaphunzitsidwe mfundo zofunika kwambiri zokhudza chimo ndi chipulumutso mwa Mzimu Woyera. Sanadziwe za uzimu ndi vumbulutso la chowonadi la chipulumutso. Erasmus adatsutsa magwiritsidwe ntchito ambiri olakwika a mpingo wa Roma, koma pomwe chiopsyezo cha chizunzo chinabuka pa iwo omwe ankatsatira “Luther”, Erasmus anabwerera m’mbuyo pa mgwirizano womwe anali nawo ndi Luther.

Erasmus ankawona kuti ntchito yake ya “Diatribe” inali ntchito yaikulu komanso yosayankhika pokamba zotsatira pa chiphunzitso cha omwe ankatsutsa ziphunzitso zonama. Komabe, Luther poyankhapo pa nkhani ya Erasmus adalemba bukhu lotchuka la ”Ukapolo wa Ufulu wakusankha.” Erasmus anadabwitsidwa nalo ndipo adagonja. Luther anatsimikiza pochokera m’Baibulo, kuti Mulungu sali Mulungu

17

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

wowona ngati ufulu wa kusankha wa munthu uli nawo ufulu wakusokoneza cholinga cha uMulungu. Ngakhale kuti angathe kuganiza kuti amasankha mwaufulu, umoyo ndi chikhalidwe chake cha uchimo chili nako kuthekera komupangitsa kuchita choyipa, pokhapokha atapatsidwa mphamvu mwa chisomo cha Mulungu pa kusankhapo. Mneneri Yeremiya anafunsa; “Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalungwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoyipa.” (Yeremiya 13:23). Analengezanso kuti, Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?” (Yeremiya 17:9). Chifuniro cha munthu wochimwa chimakondweretsedwa ndi kulolera zoyipa. Kotero kuti, munthu ali mlandu wakuti adzayankhepo pa mpando woweruza wa Mulungu.

Ngakhale zinthu ziri choncho, Mulungu amakwaniritsabe zolinga zake za muyaya. Chifukwa timawerenga kuti, “zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene ayitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” (Aroma 8:28). Chifuniro cha anthu olungama ndi wochimwa, omwe chili m’manja mwa Mulungu. Yosefe mwa chikhulupiriro adatha kunena kwa abale ake, poyang’ana m’mbuyo za momwe adamugulitsira monga kapolo: “Koma inu, munandipangira ine choyipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.” (Genesis 50:20). Zoonadi akadakhoza kunena ndi Solomoni; “Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.” (Miyambo 16:9).

Mtima wochimwa pamodzi ndi chifuniro cha munthu palibe zomwe zingachitike pa zokha zomwe ziri zokondweretsa Mulungu; koma pomwe Mulungu agwira ntchito mwa Mzimu Woyera, pamenepo ndipo mtima wa munthu umatembenuzidwira ku zimene ziri zabwino. Pamenepo ndi pomwe wochimwa “adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21). Kotero kuti, mtumwi Paulo adakhoza kunena kwa Afilipi, “Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.” (Afilipi 2:12-13).

Ichi ndi chotikhudza masiku ano, kuti a zipembedzo zomwe zinabadwa potsutsa chiphunzitso cha chiRoma, komanso omwe amalalikira za kubadwanso kwatsopano amagwirizana naye Erasmus ndi Mpingo wa ku Roma, kutsutsana ndi chiphunzitso

18

Mlengi Wa Mphamvu Yonse

cha Mawu a Mulungu pa chophunzitsa za mphamvu zake zokha za Mulungu pa chipulumutso cha munthu. Kodi ichi ndi chinthu chodabwitsa kuti mipingo iyi yalowa mu chiphunzitso cha chiRomachi? Ngati maziko a chiphunzitso chowona angathe kupeputsidwa, ndiye kuti makhalidwe a kunja kwake adzagweranso mwachangu mu kulakwa komvetsa chisoni.

Timalize mutu uwu ndi ndakatulo ya mzaka za 1600 yomwe adalemba mtumiki wa Mulungu Hallgi”mur Pe’tersson, yomwe idatengedwa mu mkulingalira kwake pa kumangidwa kwa Ambuye Yesu mu Getsemane.

Ambuye wathu mwa chisomo analolera Adani ake kuti adzuke Opusa omwe anamvera chisomo monama Mphamvu zawo zinatsutsidwa mlengalenga! Kenanso funso linamveka “Mufuna kuti mupeze ndani?” ndipo iwo Ambuye wathu anazinga Okonzeka manja awo kuti amange. Mbuyeyo keneka anamveka kulankhula, “Ndinakuwuzani kuti Ndine Amene. Ngati mufuna Ine, Lolani anthu awa amuke a ufulu.” Motero analankhula mbale wathu wakumwamba. Osamalira za zonse za iye, Okoma mtima monga mai wachikondi Zomwe anthu anadziwa. Chikondi chachikulu ndi mphamvu ya Yesu Pomwe ife tiyenera kusinkhasinkha bwino. Ngakhale linali ora la mdima bi, Omugwira palibe m’modzi akadakakamiza. Pomwe chosowa changa chili chachikulu. Ndi adani anga andizinga mpanda Ndidziwa inu mwakachete mudikira Njira zawo kuti muzitsutse.

19

Mlengi Wa Mphamvu Yonse. Mwa ufulu Anapereka, Atate wake kuti awamvere. Kumvera anachita Kuti alipire cholakwa chako Kodi wayiwala mangawa ena, Nsembe yokondedwa yake, Mulungu mwana wake wokondedwa, Kuti akupatse Paradiso! Anasonkhana kumuzinga Iye, Gulu ili, la ukali, losaphunzitsidwa, Ndi zingwe zowawa anam’manga Iye, Mwana wa Nkhosa woyera wa Mulungu. Anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zanga, Ambuye movutika namangidwa. Nizikhala chete zomwe timamvera Mikono ndi manja ake zinazungulira. Anali a Yuda omwe anamanga Inu, Koma ndi chifukwa cha machimo anga Anamamatira kwa Inu ngati zingwe. Chifukwa ndinasiya chilamulo cha Mulungu. Tsopano ozama mu chimo; Ndipemphera kwa inu ndimasuleni, Popeza ichi tsopano ndicho ndikhumba Kutumikira ndi kulambira Inu. Ufulu wake Iye anagonjera Kotero zondimanga anathyola Chokhumba changa cha nthawi anaphimba. Nandimasula ku gori langa. Zondizinga zamphamvu ndi zomvetsa chisoni. Pa Iye zinamkhalira kumuswanya, Kuti dalitso lolemera kwathunthu Likhoze kukhala pa ine!

20

Mlengi Wa Mphamvu Yonse Tsopano lolani gori Lanu, Ambuye wanga, Njira yanga lilamulire, Kuti ndithe kutsatira mwachangu Kufikira pa malo anga achandamale. Ndekha mu ntchito yomwe Inu mwandilemba Ufulu weniweni ndithe kupeza, Kusangalala kokhako kwenikweni Kwa moyo ndi mtima ndi malingaliro. (kuchokera mu mamamasulidwe a Chingerezi a A Gook)

MUTU 3. YESU KHRISTU WUVUMBULUTSIDWA NDI WODZIWIDWA.

Chidziwitso.

Mtumwi Paulo ananena mfundo yofunika kwambiri pomwe ananena kuti, “Chifukwa chake monga munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchuruka chiyamiko.” (Akolose 2:6-7). Pokha pokha titamvetsetsa chomwe kulandira Yesu chili, sitingathe kuyenda chitsogolo mu njira ya moyo wosatha. Kuwonjezera apo, tionanso kusowekera komwe kulipo kuti tifunefune zisomo zapaderazo zomwe zimakhazikitsidwa pa yemwe wangobadwa kwatsopano kuti ayende mu chikondi choyamba cha Yesu.

Kotero kuti tiyenera kufunsa, kuti kodi tinayamba kukhulukira koyamba motani? Kodi nanga mayesero apadera ndi madalitso a kutembenuka mtima ndi ati? Tikamvetsetsa ichi, tidzakhala ndi maziko olimba omwe tiyenera kuyendapo mwa Khristu Yesu Ambuye.

Chiyero cha Mulungu ndi Wochimwa Wolapa.

Si anthu omwe ali ndi ntchito zoyembekezeka kukhala zabwino zakuti zikasonyezedwe, kuti ndi iwo omwe alandira Yesu moona mtima. Pakuti Yesu anati,

21

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

“Sindinadze kudzayitana olungama, koma ochimwa.” (Mateyu 9:13). Ambuye wasankha otayika, owonongedwa ndi iwo opanda chiyembekezo mwa iwo eni, kuti chisomo ndi chifundo zizingowalirawalirabe.

Poyamba wochimwa samamvetsa kwathunthu za machitachita a Ambuye pa munthuyo. Amawonetsedwa kuti Mulungu anakhazikitsa m’Baibulo zomwe ziri zolondola ndi zomwe ziri zolakwika, ndipo keneka amayamba kuwona kuti chimo ndiko kulakwila lamulo loyera la Mulungu. (1 Yohane 3:4). Komabe, amayesetsa kuti atsatire malamulo mu mphamvu yake; koma pomwe ayesa yesa kuwakwaniritsa, ndi pomwenso lamulo la Mulungu liwoneka kuti ndi loyera ndiponso la uzimu. Ayenera kuphunzira kuti si kuchita kwa chimo kokha komanso, malingaliro oipawo, omwe Mulungu ayenera kulanga.

Pomwe umwini mphamvu ndi chiyero cha Mulungu zivumbulutsidwa ndi Mzimu Woyera, wochimwayo amazindikira kuti Mulungu ndi wapamwamba kosati ndikuyeseka, wamphamvu zopambana ndiponso wa ulemerero koposa munthuyo, (Yesaya 6:1-7). Ichi chititsogolera kutsutsika za chimo ndiponso kulapa kochokera pansi pa mtima. Tipereka chitsanzo cha izi kuchokera pa zinthu za dziko la pansi. Pamene tiri kukakumana ndi wina wofanana ndi ife, timamva bwino lomwe, mwina mwakenso timaganizira za kuthekera kwathu ndi momwe tingadziwonetsere mwa ubwino. Koma ngati tiyendera wina yemwe ali wapamwamba ndithu, wofunika, wotchuka, wamphamvu, wozindikira zinthu, ndiponso wa chikhalidwe chosanyozeka ndi wa ulemu wake, pamenepo timanthunthumira ndi kuwonanso kuperewera ndi kufowoka kwathu. Ichi ndi chitsanzo chofowoka chokhudzana ndi momwe wochimwa, yemwe amamvetsetsa za uMulungu ndi chiyero cha Mulungu. Chimabweretsa ku mtima kutsutsika za chimo kozama.

Pomwe munthu watsutsika amayesa mwa umunthu kufuna kuti akonze moyo wake mwa iye yekha. Komabe, kulimbana uku sikumapindula, popeza chimo liri nawo umbuye. Mkhristu ali yense ayenera kuphunzira kuti, “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuwudziwa.” (Yeremiya 17:9). Koma pomwe chisomo cha Mulungu chigwira ntchito mwa Mzimu Woyera mu mtima wa munthu, wochimwa amatsogoleredwa ku kulapa ndi kuti apemphere monga wamsonkho uja, yemwe “alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa. Ndinena ndi inu,,anatsikira kunyumba kwake kwa woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.” (Luka 18:10-14).

22

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

Monga momwe taonera, wokhulupirira wowona mwa Yesu Khristu ayenera kudziwa chiyero cha chilamulo, chomwe chimadziwika bwino ndi dzina lakuti Chilamulo cha Mose, chomwe chimafotokozeredwa mwachindunji kuti malamulo khumi. Kodi nanga pali chiyanjano chotani pakati pa chilamulo ndi Uthenga Wabwino pa moyo wa wokhulupirira? Yankho likuperekedwa ndi mtumwi Paulo yemwe analemba motere kwa mpingo wa ku Galatiya. “Nanga chilamulo tsono? Chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufukira ikadza mbewu imene adayilonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe. Koma nkhoswe si iri ya m’modzi; koma Mulungu ali m’modzi. Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nawo malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo. Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Yhristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo. Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikadavumbulutsidwa bwino bwino. Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi. Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.” (Agalatiya 3:19-26).

Omwe amakhala pansi pa uphunzitsi wa chilamulo, ndipo amamva zotsatira zomvetsa chisoni zobwera chifukwa cha kugwa kwa munthu, angathe kunena pamodzi ndi mneneri; “Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse ziri ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse titofa monga tsamba, ndi zoyipa zathu zitiweluza monga mphepo. Ndipo palibe amene ayitana dzina lanu, amene adzikangamiza yekha kugwiritsa nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoyipa zathu. Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu atate wathu; ife tiri dongo, ndipo Inu ndinu Muwumbi wathu; ndipo ife tonse tiri ntchito ya dzanja lanu. Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoyipa nthawi zonse; taonani, yang’anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tiri anthu anu. “(Yesaya 64:6-9).

Kubwera kwa Yesu.

Pomwe wochimwa yemwe walapa wapatsidwa kuwala kochepa kwa chiyembekezo mwa Yesu, malonjezano a mtengo wapatali amabweretsedwa kudzera mwa Mzimu Woyera. Ambiri a anthu a Ambuye anadalitsiddwa ndi mayitanidwe a uneneri a Muwomboli, mwana wa Davide. “Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndarama, idzani mugule vinyo ndi mkaka odanda ndarama ndi opanda

23

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

mtengo wake. Bwanji inu mulikutayira ndarama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zusakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chiri chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona. Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.” (Yesaya 55:1-3).

Chifukwa cha malonjazano a mtengo wapatali ndi mayitanidwe amenewa, anthu a Ambuye amakokedwa kutuluka mu mdima kulowa mu mkuwunika. Monga Ambuye analonjeza kubwezeretsedwa kwa Israeli mwa mneneri Yeremiya, koteronso Mawuwa analembedwa kuti atonthoze ndi kudalitsa mpingo, Israeli wa uzimu; “Inde ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.” (Yeremiya 31:3). Kudzera mu chikakamizo cha Mzimu Woyera, wochimwa yemwe walapa, yemwe anayang’ana kwa Yesu monga Mpulumutsi wake amapatsidwa kufuna pa nthawi yomwe mphamvu ya Mulungu ikugwira ntchito (Masalmo 110:3). Ukapolo wa uchimo ndi khalidwe loyipa zimaswedwa ndipo wochimwa amadziwa ufulu wa ulemerero wa Uthenga Wabwino. Timawerenga za Lydia yemwe adalambira Mulungu, ndipo, “mtima wake Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.” (Machitidwe 16:14).

Ochimwa amalungamitsidwa ndi chikhulupiriro mwa Ambuye Yesu Khristu. (Agalatiya 2:16), mtima wawo ndi kumvetsetsa kwawo zitatsegulidwa kuti adziwe kuti Yesu anafa chifukwa cha iwo. Amawona mwa chikhulupiriro, kuti kudzera mu chikondi ndi chisomo cha ulere Mulungu, Yesu analipira chilango chochititsa manyazi chifukwa cha machimo awo. Ngakhale kuti Yesu anakhala moyo wangwiro pakumvera Mulungu Atate, nakwaniritsa chilamulo chonse, anapereka moyo wake ndi kukhetsa mwazi wake. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti chilamulo cha Mose chimayenera kuti mwazi wa nyama ukhetsedwe, chomwe chinali chifanizo chakulozera ku kufunika kwa mwazi wokhetsedwa wa Yesu, Mwana wa Nkhosa wa Mulungu. “ Koma atafika Khristu, Mkuluwansembe wa zokoma zirinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi, kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha,, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo chiwomboli chosatha. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi wa ng’ombe zamphongo, ndi makala a ng’ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?” (Ahebri 9:11-14).

24

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

Ambuye Yesu sikuti anangokhetsa mwazi kokha, koma tinawerenga kuti pa Kalvari pomwe asirikali “pofika kwa Yesu, m’mene anamuwona Iye, kuti wafa kale sanathyola miyendo yake; koma m’modzi wa asirikali anamgwaza ndi nthungo m’nthiti yake, ndipo panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi. Ndipo iye amene anawona, wachita umboni, ndi umboni wake uli wowona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zowona, kuti inunso mukakhulupurire.” (Yohane 19:33-35). Izi zimalankhulidwa za zinthu zodalitsika zingapo zomwe Mzimu Woyera amavumbulutsa kwa wokhulupirira. Poyamba, pali mwazi wachitetezero wochokera mu mtima wokonda wa Yesu, kumupangitsa Mulungu ndi wochimwa “pa amodzi” mu umodzi odalitsika. Chachiwiri, pali madzi amoyo oyeretsa wochimwa ku kusalungama kwake pamaso pa Mulungu. Koma kupitirira apo, ichi ndi kukwaniritsa kwa uneneri uwu, “ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake m’modzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana mwake woyamba.” (Zakariya 12:10). Izi zionetsa kuti, ngakhale msirikali wa chiRoma anamulasa m’nthiti Ambuye Yesu, moyo woyera ndi wosachimwa wa Ambuye unalasidwa chifukwa cha machimo a anthu Ake. Pamene wochimwa azindikira ichi mwa chikhulupiriro, ndi kupenya za momwe kuchimwa kwake kulili, padzakhala kulira kwa kudzimvera chisoni chifukwa za zomwe uchimo wachita. Komabe padzakhala chikhumbo choyaka moto cha kufuna kumasulidwa kuchoka ku kuyipa kwa chimo, ndi kuti atumikire Ambuye kuchokera mu chikondi cha moyo watsopano.

Si imfa ya Khristu yokha yomwe iyenera kudziwika mu mtima wa munthu, komanso kufunikira kwakukulu kwa kuwukanso mu thupi kwa Yesu ndi kukwera kupita kumwamba kwake. Paulo akulemba za Yesu, “Amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, nawukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama. Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tirikuyimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 4:25-5:2). Pa kukwera kwake kwa umunthu kupita kumwamba anapembedzera anthu ake pa mpando wachifumu wa Mulungu. “Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbewu ya Abrahamu. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m’zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoyipa za anthu.” (Ahebri 2:16-17). Monga Ambuye Yesu anawuka kwa akufa ndi kukwera kupita kumwamba, kotero kuti mu umodzi ndi Yesu okhulupirira owona amakwera mu moyo watsopano kwa Mulungu. Pa dziko la pansi amadziwa umodzi wa uzimu, koma

25

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

atamwalira moyo wawo udzabweretsedwa pa mpando wachifumu wa Mulungu mwa chikondi ndi chifundo kuti ukhale kumeneko kwa muyaya. Pakuti Mulungu, “anatiwukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m’zakumwamba mwa Khristu Yesu; kuti akawonetsere m’nyengo zirinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m’kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.” (Aefeso 2:6-7).

Chivomerezo Chopanda Chipulumutso Chenicheni.

Tilingalira za iwo omwe mbewu ya Uthenga Wabwino inabzyalidwa pa nthaka yabwino, “ndiye wakumva Mawu nawadziwitsa; amene abaladi zipatso.” (Mateyu 13:23). Komabe, tiyeni tisiyanitse chidziwitso chowona cha chipulumutso ndi chivomerezo cha anthu, omwe afanana ndi mbewu yofesedwa pa nthaka ya miyala: amamva nalandira Mawu ndi chimwemwe, koma amagwa pomwe mazunzo ndi mayesero abuka chifukwa cha Uthenga Wabwino. Chimodzimodzinso, tiyeni tichenjezedwe za mkhristu yemwe anavomereza “amene akumva Mawu amene afesedwa kuminga,” uyu ndi yemwe; “wakumva Mawu; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa Mawu, ndipo akhala wopanda chipatso.” (Mateyu 13:22).

Ndi zomvetsa chisoni kulingalira za momwe masiku ano mipingo yachikhristu iliri yomwe idavomereza Khristu. Chowonadi kawirikawiri chimaponderezedwa pansi pa mapazi ndi iwo otumikira amene, omwe ayenera kumadyetsa nkhosa. Ndizosadabwitsa kupeza mipingo yodzala ndi abambo ndi amai omwe sadziwa Uthenga Wabwino, monga momwe anavumbulutsira Mzimu Woyera ndipo nakhazikitsa mu Baibulo. Ngakhale kuti zikuwoneka kuti akuwoneka ngati akulankhula za chipulumutso, sadziwa china chiri chonse chokhudza kutayika mu uchimo! Chizindikiro cha chipembedzo chonama ichi ndi kusowekera kwa kutsutsika kwa chimo ndi kulapa kochokera pansi pa mtima. Kwa ena chipembedzo chawo chiri mu zinthu za pa dziko la pansi lino; komatu Paulo analemba, Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tiri ife a umphawi oposa a anthu onse.” (1 Akorinto 15:19). Kumanga mpingo pa makhalidwe ndi zokhudza miyoyo ya anthu kapena zotikondweretsa kwambiri zomwe zokumana nazo, ndiko kumanga pa mchenga. Izi sizingalowe m’malo mwa thanthwe, lomwe ndi Khristu Yesu Ambuye, pomwe mpingo wowona wamangidwa. (Mateyu 16:18).

Tiyenera kuvomereza, za kuchepa kwa omwe lero angalankhule za chidziwitso mwa chikhulupiriro za mphamvu za mwazi wa Khristu, womwe “womwe umatisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” 1 Yohane 1:7). Pali anthu ochepa omwe amafika pa

26

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

malo opembedzera, omwe amakhutitsidwa ndi Uthenga Wabwino mu uthunthu wodalitsika mu kumveka bwino kwake. Kotero kuti, tiyeni mwa chikhulupiriro tidzifufze tokha. Kodi tiridi pa thanthwe, lomwe ndi Khristu Yesu Ambuye? Kodi ndi zoona kuti talumikizidwa ku Mpesa ndipo tikubereka zipatso, zomwe zili zosafota, ku ulemerero wa Mulungu? Kodi timadziwa liwu la “wokondedwa” yemwe ndi Khristu akulankhula ku mpingo wake” “Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine, tawuka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye, pakuti, tawona, chisanu chatha, mvula yapita yaleka; maluwa awoneka pansi; nthawi yoyimba mbalame yafika, Mawu a njiwa namveka m’dziko lathu;” (Nyimbo ya Solomo 2:10-12).

Tiyeninso tionetserenso kusiyana pakati pa chikhristu chowona ndi chonama pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ku thupi. Tingoyerekeza kuti tayamba ulendo tiri ndi zoyembekezera ndi zokhumba zambiri za umunthu; mwina mwake pamakhala kuti pali kukhazikitsa kwa moyo wabwino ndi wapamwamba ku mayiko ena. Ndipo mwadzidzidzi ngalawa ija ndi kuyamba kumira. Chiyembekezo chathu chonse chimatayika; timafuwula kuti ena atithandize kutipulumutsa. Ndipo pomwe tangotsala pang’ono kuti tiwonongeke, ngalawa ina kapena othandiza pa ngozi afika kuti atipulumutse ndi kutitengera ku dziko losiyaniranatu ndi lomwe ife timayembekezera kukafikako. Izi ziri chimodzimodzi wochimwa yemwe sadziwa Mulungu, koma mwadzidzidzi abweretsedwa mu mavuto akulu ndi Mulungu, kuti awone kuti ali wotayika mu chimo ndi kuti alilire kwa Mulungu kuti amuchitire chifundo. Ambuye ndipo amamuyandikira ndi kumupulumutsa iye mwa chikhulupiriro cha moyo mwa Khristu Yesu.

Palinso chitsanzo china chofanana chakuti pomwe tanyamuka pa ulendo wathu, koma pang’ono ndi pang’ono timazindikira kuti ngalawa yathu siyabwino kwathunthu kuti iyende pa nyanja monga momwe timaganizira. Timayesa kuti tikonze kapena kuti titulukemo, koma vuto la ngalawa yathu limangonka likulirakulirabe, kufikira pomwe mapeto ake tifuwula kuyitanitsa chithandizo ndipo ndi kupulumutsidwa mwa chisomo. Izi zifotokozera nkhani za wina yemwe abweretsedwa mwa pang’ono pang’ono, mwina mwake kwa zaka zambiri, kuti athe kuwona kuti ali otayika mu chimo. Komatu pamakhala kulira komweko kofuna chifundo cha Mulungu, ndi vumbulutso lomwelo la chipulumutso mwa Khristu Yesu.

Tsopano tiyeni tisiyanitse ndi iwo omwe ali pa chisangalalo pa gombe la nyanja ndipo akopeka ndi kulengeza kwa ulendo womwe wakonzedwa wachisangalalo pa nyanja. Zimakhala ndi kuchonderera, ndipo tsikulo limakhala la bata komanso dzuwa labwino. Ndalama zake zimaperekedwa za ulendo wa ngalawa, ndipo patapita nthawi

27

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

pang’ono aulendo onse amabwereretsedwanso pa malo omwe aja amene anayambira ulendo. Izi ziri ngati chipembedzo chonama. Sipakhala kufuwula kuti alandire chifundo, sipakhalanso kuwoneka kwina kuli konse kwakuti angathe kuwonongeka monga azipembedzo zonama pakuphwanya malamulo oyera a Mulungu, ndipo wochimwa amakhalabe ali mu machimo ake. Ngakhale kuti chivomerezo chonama cha chikhristu ichi chingathe kukhala ndi zokondweretsa ndi zopindula zambiri mu moyo uno, Gahena ali kudikira kuti alandire wina ali yense wochimwa yemwe salapa! Tingathe kuchita bwino kukumbukira fanizo lukhudza za munthu wachuma ndi Lazaro. (Luka 16:19-31).

Tiyeni tsopano tidzifunse tokha; kodi timadziwa chiyani pa chidziwitso chowona cha chipulumutso cha Yesu Khristu chovumbulutsidwa ndi Mzimu Woyera? Kodi izi zimatikhudza motani m’moyo wathu? Ngati timaperewera, kapena ngati tiribe chitsimikizo chakuti timadziwa za zowonadi zodalitsika izi pa ife eni tokha mu mitima, tiyeni tifunefune mopanda chinyengo mwa pemphero kwa Yesu. Ngati timva kukokedwera kwa Yesu, tiyeni tsopano titule katundu wa mu mtima mwathu mwa pemphero. Tiyeni tifunse kuti Mzimu Woyera atsegule Baibulo ndi kutipatsa ife chikhulupiriro chowona ndi kulapa, ndi kutinso zotchinga za malingaliridwe a dziko la pansi komanso kusakhulupirira kuti zichotsedwa.

Ambuye Yesu amapereka chilimbikitso cha mtengo wapatali kwa iwo omwe afunafuna. “Pemphani ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzampatsa njoka m’malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chikhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?” (Luka 11:9-13).

Ambuye ndi mpulumutsi wa onse omwe akhulupirira mwa chikhulupiriro cha uMulungu . Iye, “safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike ku kulapa.” (2 Petro 3:9). Ambuye atulutse zikhumbo zowona za uzimu, ndi ife mwa chisomo tikhale ndi makutu kuti tithe kumva kuyitanidwa kochokera kwa Uthenga Wabwino. Yesu anati, “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28). “Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu.” (Yohane 1:17). Tilole kuti zinthu izi zikhale zathu!

28

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

Zisomo za Wobadwanso Kwatsopano.

Kwa mkhristu aliyense nthawi ya chikondi choyamba, pomwe iwo adafika podziwa chipulumutso mwa Yesu, ndi nthawi yapaderadera. Komabe, tiyeni tisangopumira pa zomwe tikungokumbukira, koma tiyeni tilingalire pa lembo lomwe tinayambira mutu uwu; “Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye.” (Akolose 2:6). Zisomo zapadera izi ndi zotsatira za chipulumutso ziyenera kukhumbidwa mu zaka zotsatira kuti munthu ayende mu zimenezo. Pomwe padzakhala kukula mu chisomo ndi chidziwitso mwa Ambuye pa moyo mkhristu, zisomo zapadera za kutembenuka ndi maziko pa mayendedwe ndi makhalidwe a mkhristu: zisomozi sizimasintha. Tsopano tiyeni tizilingalire.

Kulapa ndi chinthu chosowekera pa moyo wake wonse wa Mkhristu. Ngakhale atakhala kuti akudziwa za chiwombolo ndi chikhululukiro cha machimo, mkhristu sakhala wosachimwa pomwe ali pa dziko la pansi. Izi zikutsimikizidwa ndi mtumwi Paulo, yemwe adadziwa kuti iye mwini anali mfumu ya ochimwa. (1 Timoteyo 1:15). Paulo analembanso kuti, kulimbana kwa mkati mwa munthu kwa pakati pa munthu wakale wa uchimo ndi munthu watsopano wa chisomo. “Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choyipa chiriko. Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiwona lamulo lina m’ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndikundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziwalo zanga. Munthu wosawuka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo. Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.” (Aroma 7:21-8:2).

Tisowekera kuyenda mu kulapa komanso chikhulupiro, kufika kwa Yesu kawiri kawiri! Tilole kutsogozedwa ndi mzimu kuti tipemphe chifundo komanso mphamvu zotipatsa kutha kuyenda mu malamulo ake, kuti munthu wakale wa chimo agonjetsedwe. Tilole kuti tikokedwe ndi Mzimu Woyera kuti tipemphere monga Yabezi; “Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, choyipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye,” (1 Mbiri 4:10).

Munthu yemwe wangotembenuka mtima kwatsopano amakhala ndi chikhulupiriro

29

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

ngati cha mwana komanso amadalira Yesu mokhala ngati momwe amachitira mwana. Zikapezeka mwa mkhristu yemwe wakula, chimakhala chokongoletsa cha mtengo wapatali ku mphamvu ya Uthenga Wabwino. Chipatso cha kubwera kwa munthu kwa Yesu mwa pemphero, limene zolabadira za mtima zimaperekedwa pa mapazi ake, ndi pamene mayankho ambiri a mapemphero amafika omwe amapereka ulemerero kwa Mulungu. Zitsimikizo zowonekera ku thupi za chikhulupiriro chokhala ngati cha mwana ichi ndiko kutaya zokondweretsa za dziko la pansi, ndi kukokeredwa kwa Yesu mu malamulo ake komanso kuti aone kuti za pa dziko la pansi nzachabe.

Chizindikiritso china chowonjezera cha yemwe watembenuka mtima posachedwa ndi chikondi pa akhristu anzake. Samakhala ndi maganizo olakwika kapenanso kuweruza komwe momvetsa chisoni nthawi zambiri kumasokoneza mpingo. Pomwe wotembenuka mtima kwatsopano adziwa kukoma kwa chikondi cha Mulungu pa moyo wake, kenaka iyenso amakonda abale ake mwa Ambuye. “Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikra Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:7-8).

Pamene m’modzi wafika podziwa za chuma cha m’mwamba mwa Khristu Yesu, pamakhala chikhumbo choyaka chakufotokozera ena za chowonadi cha mtengo wapatali chomwe chavumbulutsidwa. Kotero kuti, chimwemwe chakukhala mwa munthu yemwe watembenuka posachedwa. Pomwe Ambuye Yesu adadzivumbulutsa yekha kwa mai wa ku Samaria, “anamuka kumudzi, nanena ndi anthu, Tiyeni, mukawone munthu, amene anandiwuza zinthu ziri zonse ndinazichita; ameneyu sali Khristu nanga?” (Yohane 4:28-29). Momwenso, munthu wamisala wa ku Gadara analamulidwa ndi Yesu, pomwe adatulutsa ziwanda zambiri mwa iye, “Muka kwanu kwa abale ako, nuwawuze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.” (Marko 5:19). Pakadakhala popanda chikhumbo chakuti ena adziwe za phindu lalikulu lomwe liri mwa Yesu? Ngati umboni ukusowa mu moyo wathu, kodi zitanthawuza kuti tataya chikondi chathu choyamba; kapena ku kuipira apo, kuti sitidazikirepo ndi kale lonse za chikondi cha Yesu m’mitima mwathu.

Tiyeni tikumbukire momwe yemwe watembenuka mtima posachedwa amakhalira ndi chidwi ndi kulakalalaka kusunga Mawu a Mulungu, komanso mwachangu amawerenga Baibulo. Pali zinthu zomwe amakhala akungozipeza kumene zokhudza Yesu, monga mwa vumbulutso la Mzimu Woyera. Izi zimapereka chitonthozo

30

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

chokoma ndi malingaliro abwino mkati mwa mayesero ndi mavuto. Kenaka mayamiko ochokera pansi pa mtima amapita kwa Mulungu chifukwa cha mphatso zambiri za Mulungu, mu chisomo ndi kupatsa.

Zinthu izi, makamaka kubwera kwa Yesu, ndi zosowekera osati kamodzi, koma pa ulendo wonse wa moyo. Tiyeninso tikumbukire za machenjezo a Ambuye ku mpingo wa ku Sardis. “Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira, zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga. Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.” (Chivumbulutso 1:1-3).

Khristu Yesu ndi Ambuye.

Tiyeni tsopano titembenukire ku mfundo ina ya Mawu omwe tawerenga ku bukhu la Akolose: imene iri njira imene mtumwi Paulo akunena za Muwomboli monga “Khristu Yesu ndi Ambuye” (Akolose 2:6). Sitiyenera kudutsa apa mwachangu, koma mwa Mzimu tilingalire za kufunika kwa mutu uwu.

Mawu akuti “Khristu” amachokera ku mawu a chiGriki, “Christos” kutanthauza kuti “wodzozedwa”; mu chiHebri mawu awa ndi “Messiah.” Dzina lakuti “Yesu” ndi mawu chiGriki omwe mu chiHebri ndi “Yoshua”, kutanthawuza kuti “Mpulumutsi.” Kotero kuti, Yesu Khristu ndiye Messiah, wodzozedwa wa Mulungu, ndiye Mpulumutsi. Mawu omwe mngelo analankhula Yosefe anali akuti “ndipo adzamutcha dzina lake Emmanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.” (Mateyu 1:21). Gawo la chitatu la dzina lake ndi “Ambuye”, limatanthawuza za uMulungu wa Yesu Khristu monga Mwana wa Mulungu, wachiwiri pa utatu wa uMulungu. Yesu ali wodzozedwa monga Mneneri, Wansembe ndi Mfumu; ndipo ngati tilandira kudzoza kwina kuli konse kapena mphamvu kuchokera kwa Mulungu, izi zimachitika mwa mphamvu ya kulumikizika kwathu kwa Yesu wodzozedwayo.

Kuphatikiza kwa maina awa “Khristu Yesu Ambuye” ndi zofunika kwambiri. Kumasiyanitsa pakati pa chowonadi ndi cholakwika; kumawonetsera poyera iwo omwe sadziwa chowonadi (monga momwe Mzimu Woyera anavumbulutsira), koma omwe Mawu awo amveka mwapamwambamwamba kuti ali Mkhristu. Pali ambiri omwe adzakhulupirira mwa “Khristu”; wina yemwe sali Yesu, koma mpulumutsi wina wake. Ena amatsatira Yesu monga munthu wabwino chabe, yemwe anapereka chitsanzo cha kudzipereka nsembe. Palinso ena omwe amakhulupurira mwa

31

Yesu Khristu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

“Ambuye” wina yemwe sali Ambuye Mulungu wa Israeli. Komabe, pomwe tilankhula za “Khristu Yesu Ambuye” palibe mpata wakuti pakhale zikhulupiriro zamitundumitundu mu mpingo. Pakutsusa izi, Yesu Khristu anakhazikitsidwa monga munthu weniweni ndi Mulungu weniweni amene ndiye yekhayo Mpulumutsi. Tiyeni tione phunziro ili mopitirirapo.

Pamene Mulungu adawoneka kwa Mose mu chitsamba choyaka ndi moto, adafunsa zokhudza dzina la Mulungu. “Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani? Ndipo Mulungu anati kwa Mose, “INE NDIRI AMENE NDIRI INE” Anatinso, Ukatero ndi ana a Israeli, INE NDINE wandituma kwa inu.” (Eksodo 3:13-14). Dzina lakuti, ‘INE NDINE’ mu chiHebri limatanthauza kuti “Yehovah” mu Baibulo la chingerezi lotchedwa “King James Version” likutanthawuza “AMBUYE”, (linatanthawuzidwa ndi zilembo zazikulu kusiyana ndi maina ena akuti “Ambuye” mu mamasulidwe a m’Baibulo ili). Liwu la chiHebri ili lomwe litanthawuza “Yehovah”, linayesedwa la uMulungu ndi aYuda, kotero kuti silimatchulidwa chifukwa cha kuwopa kutchula dzina la Ambuye pachabe.

Pakutero, tikuwona uMulungu wa Ambuye Yesu, pomwe adalankhula kwa aYuda, “asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndiripo.” (Yohane 8:58). Momwemonso, m’munda wa Getsemane timawerenga kuti; “Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa Iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani? Anayankha Iye, Yesu mnazarayo. Yesu ananena nawo, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka Iye , anayima nao pamodzi. Ndipo m’mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m’mbuyo, nangwa pansi.” (Yohane 18:4-6). Apa tikuwona ulemerero wa uMulungu unawala pomwe Yesu analankhula Mawu akuti “Ine ndine”, komwe kunali kuonetsera kuti sanali Yesu Mnazarayo wongonyozedwa, komatu kuti ali Mwana wa Mulungu.

Zitsanzo zambri zingapezeke mu Chipangano Chakale, zomwe zimasonyeza mu uneneri kwa Yesu monga “MBUYE”. Tiyeni tifananize Mawu awa, “Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimariziro ndine ndemwe.” (Yeasaya 41:4), ndi mawu a Ambuye Yesu wowuka kwa akufa akuti, “Ndine Woyamba ndi Womaliza.” (Chivumbulutso 1:11). Chitsanzo china chikupezeka pa kufananiza Yesaya 40:3 ndi Mateyu 3:3. Kupitirira apo, pomwe Paulo analira kwa Mulungu pa njira ku Damasiko, anati “Ndine Yesu amene amene umlondalonda.” (Machitidwe 9:5).

Talankhula pang’ono za mgwirizano pakati pa Mulungu Atate ndi Mulungu Mwana, komanso pali Mulungu Mzimu Woyera. Yesu, mwana wa Mulungu, analankhula za

32

Yesu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

Mzimu kupitiriza kuchokera kwa Atate ndi Mwana (Yohane 15:26). Utumiki wodalitsika wa Mzimu Woyera, wachitatu pa Utatu wa uMulungu, ndiyo kuvumbulutsa Yesu kwa anthu osankhika a Mulungu; “Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zinthu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” (Yohane 14:26). Kotero kuti, mtumwi Yohane analemba za Utatuwu; “Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye chowonadi.” (1 Yohane 5:7).

Chiphunzitso chakale cha Mawu a Mulungu cha mpingo, ndi chakuti Mwana wa Mulungu ndi mwana wa muyaya wa Mulungu. Ali Mwana wa Mulungu chifukwa cha ubale monga Atatu a uMulungu, osati chifukwa cha chikhalidwe cha umuyaya wawo onse pamodzi, (onani bukhu la, uMwana wa muyaya lolembedwa ndi J.C. Philpot). Ichi ndi chowonandi chokhazikitsa maziko akuti mwana wa Mulungu anakhala mu mgwirizano ndi uMulungu wake “pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbewu ya Abrahamu. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m’zonse kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoyipa za anthu.” (Ahebri 2:16-17). Kusiyana kofunika kwambiri pakati pa Yesu Khristu ndi abambo ndi amayi ena onse ndi kwakuti Yesu sanabadwe ndi mbewu ya umunthu, koma anabadwa mwa namwali. Sanadetsedwe ndi kugwa kwa munthu ku chimo, kotero kuti analibe chimo.

Kuposera apo, posiyana ndi Adamu ndi Hava, Yesu sanali wopanda chimo kokha, komanso wakuti sakadatha kuchimwa. Kudzera mu mphamvu ya mgwirizano wa uMulungu ndi umunthu wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ali mkhala pakati wa Mulungu Atate ndi ochimwa okhulupirira, movumbulutsidwa ndi Mulungu Mzimu Moyera. “Pakuti pali Mulungu m’modzi, ndi Mtetezi m’modzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu.” (1 Timoteyo 2:5).

Yesu Khristu anayenda moyo wa ngwiro ndipo anakwaniritsa chilungamo chonse, komatu Mulungu Atate “anamyesera uchimo m’malo mwathu; amene sanadziwa chimo , kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.” (2 Akorinto 5:21). Monga munthu Yesu anafa, chimene chiri chinthu chakuti sichingachitike ndi uMulungu. Koma, mu mgwirizano ndi uMulungu, Yesu Khristu anapereka nsembe yangwiro ya chimo yomwe mtengo wake ndiwosayeseka, yomwe mwa umunthu paokha ndiyosatheka. Mu mgwirizano wa uMulungu ndi umunthu, mwa uMunthu wodalitsika wa Yesu Khristu Mwana wa Mulungu, chiwombolo chakwaniritsidwa.

Kuonjeza apo, chikondi cha muyaya cha Atate kwa Mwana chimakhazikitsidwa mwa

33

Yesu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

wokhulupirira aliyense wosankhidwa “lisanankhazike dziko la pansi.” (Aefeso 1:4). Ambuye Yesu analengeza mu pemphero kwa Mulungu atate; “Ine mwa, iwo ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa m’modzi; kuti dziko la pansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.” (Yohane 17:23). Kukana umwana wamuyaya ndiko kusalemekeza Mwana ndiponso kutsutsana ndi chikondi chosatha cha Mulungu ku mipingo.

Komabe, pali mfundo zamaziko ofotokoza za uMulungu wa umunthu wa Ambuye Yesu. Mpingo woyamba udali ndi mavuto a nkhambakamwa pa phunziro ili, chimodzimodzi zolakwika zokhudza Utatu wa Mulungu monga zimakambidwa lero. Ambiri a chipembedzo chotchedwa m’chingerezi “Gnostics” adakana kuti Yesu anali ndi thupi la umunthu, koma kuti analipo mu mzimu wokha. Apatu ndiye kuti sipakadakhala kukhetsa kwa mwazi, umene popanda kukhetsa uwo palibe chiwombolo (Ahebri 9:22). Mbali ina ndi yakuti mu zaka za 300AD, Arius ndi omutsatira ake (odziwika kuti ma Arian) adakana kuti Yesu anali ndi umoyo wa umunthu (onani Robertson’s Church History, kusindikiza kwa chitatu, John Murray). 1864, bukhu loyamba, masamba 208 ndi 275). Komabe, Yesaya analankhula mu uneneri wa Yesu; “Koma kunamkomera Yehova kumtundudza; unamvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yoparamula, Iye adzawona mbewu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m’manja mwake. Iye adzawona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zawo. Chifukwa chake ndidzamgwadira gawo ndi akuru; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake ku imfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.” (Yesaya 53:10-12). Mawu a chiHebri otanthauza “moyo” ndi chimodzimodzi omwe agwiritsidwa ntchito pokamba za miyoyo ya anthu wamba (onani mu Young’s Analytical Concordance).

Mphekesera ziwiri zonsezi, za chiGnostic ndi chiArian, zimagogoda pa mtima wa Uthenga Wabwino. Ngati Yesu sanavutike mwa umunthu mu thupi ndi moyo, sipakadakhala chipulumutso cha thupi ndi moyo wa wochimwa omwe okhulupirira. Ngati anali mwa umunthu mokhudza ndi thupi lake, monga anena otsatira “Arian”, sipakadakhala kuyeretsedwa ndi kuwomboledwa kwa moyo. Pakadakhala popanda kumasulidwa kochoka mu vuto la moyo, popanda dalitso, komanso popanda chimwemwe ndi mtendere pakukhulupirira.

Pomaliza, tikuwona chikondi chakusankhula cha Atate kwa ochimwa osayenera

34

Yesu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa

kuchilandira, potumiza mwana wake obadwa yekha. Kuti tingathe kukhala ana a pa banja omwe achotsedwa ku umasiye. (Agalatiya 4:5), Aefeso 1:5). Madalitso a kumwamba ndi amuyaya ali mwa Yesu awa amavumbulutsidwa kwa ochimwa kudzera mwa Mulungu Mzimu Woyera. Koma samalani! Utatu wa uMulungu sungayesedwe kapena kufotokozedwa kapenanso kuzindikiridwa ndi malingaliro a umunthu; ndi chinsinsi cha uMulungu chomwe chiyenera kuvumbulutsidwa ndi Mzimu. “Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu; Iye amene anaonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dziko la pansi, wolandiridwa m’ulemerero.” (1 Timoteyo 3:16).

Umodzi wa Mawu Olembedwa ndi Osandulika Thupi.

Mtumwi Yohane analemba motere za Yesu Khristu. “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu” (Yohane 1:1). Mawu awa samangopereka umboni wowonjezera wa uMulungu wa Muwomboli, komanso kutitsogolera ku kulingalira za Mawu olembedwa a Mulungu, omwe anauziridwa ndi Mzimu Woyera, ali mu mgwirizano wa ulemerero ndi Mawu a Mulungu osandulika munthu, yemwe ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chifukwa chake, tinganene bwanji kuti timatsatira Yesu, ngati timatchula kusankha kusamvera malamulo oyikidwa a chikhalidwe cha Uthenga Wabwino omwe akhazikitsidwa mu Baibulo? Ngati timakonda Yesu, payenera kukhala kuwonetsedwa mwa ife chikondi ndi ulemu woperekedwa ku Mawu olembedwa. Yesu anati, “Ngati mukonda ine, sungani malamulo anga.” (Yohane 14:15). Wolemba ndakatulo akufotokoza izi motere.

Nena, mkhristu, kodi iwe ukadaposa, Muchidziwitso cha Ambuye wako? Potsata Malemba kuyesetsa nthawi zonse Koma kunthunthumira pa Mawu ake. Pereka ulemu kwa tsamba la Mulungu; Kuti uvulaze chiwalo chirichonse. Kumpereka , ndi ukali wofowoka ndi wa umbuli, Mtima wowuma ndi wodzikuza.

35

Yesu Wovumbulutsidwa ndi Wodziwidwa Ngati apo mdima uwoneka, Kulilira kufuna kuwona kwako; Zochotsa ungwiro zonse sizikhalapo, Pakuti Mawu omwe a Mulungu ali kuwunika. Malembo ndiponso Ambuye, Zikhala ndi dzina lalikulu limodzi; Mawu Olembedwa ndi Osandulika thupi, Mu zonse ali chimodzimodzi. (Hart).

Ndi chifundo cha Mulungu kuti anthu osankhika ake akabereke chipatso cha uzimu cha ku ulemerero wa muyaya wa Mulungu (Yohane 15:16, Aroma 7:4). Komabe, tiyeni tikumbukire kuti mphamvu ndi kuthekera kwa kuchita ntchito sizimakhala mwa wochimwa, koma mwa Mpulumutsi. “Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense. Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita zabwino, zimene Mulungu anazipangitaru, kuti tikayende m’menemo.” (Aefeso 2:8-10).

Tiyeni potero tipemphere mowona mtima kwa Mulungu kuti tiphunzitsidwe ndi Iye, ndi kuti tidziwe kukula mu chisomo, cha Mulungu. Pamenepo ndipo tidzakhoza “kukhala iwo opatulidwa oyitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu.” (Yuda 1:1). Ngakhale zili chomwecho, mu moyo uwu mkhristu sakhala monga wochimwa, koma amalandira vumbulutso la umoyo wa kuchimwa kwake poakupita kwa nthawi. Kusonyeza kuti Mkhristu adzaphunzitsidwa kukula mu kudalira pa chisomo ndi chifundo cha Mulungu mu ulendo wake wonse wa chikhristu wa pa dziko la pansi. Pemphero la wolemba Salmo ndi logwirizana kwambiri ndi iwo omwe atsatira Yesu mu njirayi.

“Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa Mawu anu. Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, Mutakulitsa mtima wanga. Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake. Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; Ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse. Mundiyendetse mopita malamulo anu; Pakuti ndikondwera m’menemo. Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu. Si ku chisiriro ai. Muchititse mlubzya maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.” (Masalmo 119:25,32-37).

36

MUTU 4. UMBONI WA MPINGO.

Umodzi wa okhulupirira.

Pa mutu womwe wapitawu, tinakhazikika mwapadera pa chidziwitso cha munthu cha Yesu. Tsopano tiyenera kuti tifike polingalira za thupi la okhulupirira, lomwe ndi mpingo.

Chowonadi chokhazikika chomwe Khristu, omwe adawomboledwa mwa Yesu Khristu ndi chakuti ali olumukizidwa mwa uzimu. Izi ziwonetsedwa ndi pemphero la Yesu lopempherera okhulupirira onse, “Kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife; kuti dziko la pansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine. Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi monga Ife tiri amodzi.” (Yohane 17:21-22).

Tiyeni tiyang’ane mosamalitsa Mawu a Ambuye. Awa akulankhula za umodzi wa anthu osankhika a Ambuye womwe udzakhala weniweni, ndipo udzawonedwa ndi iwo omwe ali kunja kwa Mpingo, udzakhala umboni wamphamvu wa Uthenga Wabwino ndi chikondi cha Khristu. Zotsatira zake, ndi zakuti padzakhala dalitso laling’ono ku miyoyo yomwe ili ndi chipulumutso, pamene palibe umodzi komanso kusamvetsetsana pakati pa okhulupirira enieni. Zinthu zoterezi sizimalemekeza Mulungu. Tiyeni tikhulupirire kuti anthu osankhulupirira adzaona izi ndipo angathe kunyoza dzina la Ambuye.

Chifukwa chake. Paulo anadandawulira okhulupirira a mpingo wa ku Efeso kuti, “muyende koyenera mayitanidwe amene munayitanidwa nawo, ndi kuwonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mzake, mwa chikondi; ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere. Thupi limodzi ndi Mzimu m’modzi monganso anakuyitanani m’chiyembekezo chimodzi cha mayitanidwe anu.” (Aefeso 4:1-6).

Wolemba Salmo analembanso za kukongola ndi dalitso la umodzi wa okhulupirira. “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu, kuti abale akhale pamodzi! Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake; ngati mame a ku Hermoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni: pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.” (Masalmo 133).

37

Umboni Wa Mpingo

Malemba awa ayenera kukhala moni wa chenjezo kwa iwo omwe atumphuka ndi kuyamba mitsutsano ndi okhulupirira anzawo. Pakati Akhristu enieni payenera kukhala chisomo chakugwirizana kuti pamakhala kusiyana mu zinthu zina. Sipangakhale chifukwa cha kulolera kuti mu mpingo mukhale kusamvana ndi mwano; kapena kuti pakhale kuchotsa mwadzidzi iwo omwe ife tikusiyana nawo pa nkhani zomwe ziri zosafunikira pa chipulumutso. Tiyeni tisamale za nkhwidzi zomwe ziri zosafunikira pa chipulumutso. Tiyeni tisamale za nkhwidzi zomwe kawirikawiri zimabwera kuchokera mu uchimo wa kunyada wa munthu. Pakukana izi, tiyeni tiyende mu chikondi ngati cha mwana cha Khristu ndiponso malamulo ake, potsatira Mawu a mtumwi Petro; “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choyipa ndi choyipa, kapena chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwayitanidwa, kuti mukalandire dalitso.” (1 Petro 3:8-9).

Ngati Akhristu alumikizidwa kwa Yesu, adzasiya pambali kusiyana kwawo kulikonse pomwe asonkhana. Zisomo za chikondi ndi zipatso za mtengo wapatali za mzimu, zomwe zituluka mwa chikondi cha Khristu, zidzaposa mphamvu za kusiyana kuli konse komwe kumawoneka kunja. Makoma ndi zotchinga za miyambo ndi chikhalidwe cha anthu, fuko kapena mtundu zidzagonja, pomwe okhulupirira enieni alumikizidwa kwa Yesu yemwe ndi mpesa. Chifukwa chake mtumwi Paulo analemba zokhudza munthu watsopano wa chisomo, “amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m’zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kukolerana wina ndi mzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso munayitanidwa m’thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mawu a Khristu akhalitse mwa inu chichurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunitsa ndi kuyimbirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo za uzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.’ (Akolose 3:10-16).

Momvetsa chisoni, uchimo ukupezekabe mkati mwa wina ali yense wa ife. Monga mtumwi Yohane analemba; “Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha ndipo mwa

38

Umboni Wa Mpingo

ife mulibe chowonadi.” (1 Yohane 1:8). Mpingo wa dziko la pansi ndiwopangidwa ndi ochimwa. Mpingo wokhawo wangwiro uli kumwamba, mpingo wopambana. Tiyeninso tikumbukire kuti okhulupirira onse sali nako kumvetsetsa kofanana; ena amapatsidwa kuwala koposa ena pa Mawu a Mulungu kusiyana ndi ena. Komabe pali umodzi wa uzimu mwa Yesu, ngakhale patakhala kisiyana pakati pa mipingo yosiyana.

Komabe, sitiyenera kuti tizifufuza umodzi wina uli wonse kapena kukhalira pamodzi ndi mipingo yomwe imakana Malembo kapena ziphunzitso za maziko a chikhulupiriro (Aroma 16:17-18, 2 Yohane 9-11). Iwo omwe ali mu bungwe lakukhazikitsa umodzi wa chipembedzo “Ecumenical Movement” anapeza umodzi wowoneka ndi maso wa mipingo yomwe imavomereza ndi kukhulupirira mwa Yesu. Pochita ichi anayesa kuti ayanjanitse chowonadi ndi cholakwika, poganiza kuti Uthenga Wabwino ungathe kupita patsogolo mwa njira ya umodzi wa kuthupi. Komabe, tiyeni tizindikire kuti okhulupirira enieni ali kale ogwirizana mwa mzimu ndiponso ali kale amodzi mwa Khristu Yesu, ngakhale pali kuyesayesa kwa anthu.

Tiyeni tsopano, posalowa mu kusiyana kwa mipingo, titembenukire ku mfundo zopindula zokhudza Mpingo, thupi la okhulupirira.

Mipingo Yoyendetsedwa Monga mwa Mawu.

Kuli konse komwe atumwi analalikira ndi kuti Uthenga unapindula, iwo omwe atembenuka mtima amapanga mpingo (Machitidwe 14:21-23). Gulu la anthu openyeka ili la okhulupirira linali lakuti lilambire Mulungu mu Mzimu ndi mchowonadi, kupereka umboni ku kufa ndi kuwuka kwa akufa kwa Ambuye Yesu. Koma nanga ndi mu njira yotani momwe izi ziyenera kuchitikira?

Mulungu ndi Mulungu wa dongosolo. Izi timaziwona mu chilengedwe, mu chilamulo choyera cha Mulungu, komanso mu ndondomeko ya chipulumutso mwa Yesu Khristu. Davide adakhoza kunena pa kutha kwa ulendo wake wa dziko la pansi, ngakhale anali mu machimo onse aja komanso masawutso omwe adafika pa iye, kuti Mulungu adapangana pangano losatha ndi iye “Lolongosoka mwa zonse ndi losungika.” (2 Samueli 23:5). Kotero kuti, ndi lamulo la Ambuye kuti mipingo ikhale chimodzi modzi mwa dongosolo. Mamembala ena a mpingo amakhazikitsidwa pa Mawudindo kapena kutumikira, ndipo Mawudindowa ayenera kuti asungidwe ndi ulemu. Paulo adakhoza kulankhula ku mpingo wa ku Kolose kuti, “ndingakhale ndiri kwina m’thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya

39

Umboni Wa Mpingo

makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.” (Akolose 2:5).

Pakuti Mzimu Woyera sangaphunzitse motsutsana ndi malemba, chisowekera kuti mipingo iyende mu dongosolo la Mawu a Mulungu. Ichi ndi chomwe chimapangitsa kuchoka pa njira yoyenera ngati mpingo ungayendere dongosolo lakuti ligwirizane ndi la dziko la pansi, kapena malingaliro amakono. Zili zomvetsanso chisoni kwa Mzimu ngati maziko a dongosolo la mpingo ali chizolowezi cha chipembedzo kapena ali omangika ku zokomera banja lina, ngakhale chikhulupiriro chomwe mpingowo wamangikapo chili chabwino.

Chikondi ndi Chiyanjano mwa Yesu.

Pali mfundo zina ziwiri za maziko kuseri kwa dongosolo la malemba lomwe mpingo uyenera kuyendamo. Izi zikupezeka mu malamulo awiri ochokera mu chpangano Chakale, omwe Ambuye Yesu analankhula za iwo. “Mvera, Israeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye m’modzi; ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.” (Marko 12:29-31).

Ngati tiyenera kukonda mzathu, ngakhale izi sizitanthawuza kukondweretsedwa ndi zomwe achita kapena kukhulupirira), ndi koposa kotani kuti pakhale chikondi pakati pa okhulupirira! Mtumwi Yohane analemba motere; “Okondedwa, tikondane wina ndi mzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Umo chidawoneka chiokondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anatuma mwana wake wobadwa yekha alowe m’dziko la pansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Umo muli chikondi sikuti ife tinakonda Mulungu koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mzake. Palibe munthu adamuwona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mzake, Mulungu akhala mwa ife; ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife; m’menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.” (1 Yohane 4:7-13). Tiyeni tiphunzitsidwe zinthu izi mu mtima ndi Mzimu Woyera. Motani nanga momwe tisowa kupempehera kuti tisungidwe kutali ndi mzimu wonyada ndi wodzikweza, womwe kudzera mu mzimu umenewu Satana angathe kubzyala mbewu za chisokonezo ndi nkhwidzi mkati mwa mpingo.

40

Umboni Wa Mpingo

Pamodzi ndi chikondano pakati pa mpingo, chisomo cha mtengo wowona ndicho chiyanjano mwa Yesu. Ichi sichiyenera kusokonezedwa ndi zisangalalo za umunthu kapena ubwenzi wa dziko la pansi. Ambiri a mipingo yovomereza Khristu amalephera kumvetsa kuti chiyanjano cha chikhristu chimadalira pa ubale wa wina ali yense payekha ndi Mulungu. Mtumwi Yohane akufotokoza chowonadi ichi. “Mulungu ndiye kuwunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima. Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi; koma ngati tiyenda m’kuwunika, monga Iye ali m’kuunika, tiyanjana wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” (1 Yohane 1:5-7). Ngati pali kuyenda mfupi ndi Mulungu mu chikondi ndiponso umodzi wa uzimu ndi Yesu, pamenepo ndi pomwe pangakhale chiyanjano. Chiyanjano ichi chingakhale kuzindikira ngakhale pakati pa iwo omwe samadziwana. Popeza chimachokera ku umodzi womwe onsewa ali nawo womwe ndi umodzi ndi Yesu yemwe ndi mpesa.

Ndikwabwino kwa okhulupirira kukumana pamodzi kuti apemphere komanso kulambira. Yesu analankhula lonjezo la mtengo wapatali, kuti “kumene kuli awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo.” (Mateyu 18:20). Komatu iwo omwe ali okha kapena mu masawutso kotero kuti sangathe kukumana pamodzi ndi anzawo, pali chitsanzo chabwino cha Mtumwi Yohane pa chisumbu cha Patmos, pomwe iye adakayikidwa chifukwa cha Uthenga Wabwino. Timawerenga kuti Yohane analandira vumbulutso lodalitsika pomwe anali “mu mzimu pa tsiku la Ambuye”, (Chivumbulutsi 1:10). Ambuye ali wodzala ndi chisomo chakuti ayendere iwo omwe ampsyinjika ndi mayesero akukhala pa okha kapena kupatulidwa pakati pa abale.

Komanso, ndi lamulo la Mulungu kuti Mkhristu ayenera kumasonkhana ndi anzake kuti alambire pamodzi ndi okhulupurira ena omwe amagwiritsitsa maziko a chikhulupiriro, pomwe ayenera kutsatiridwa. Mtumwi Paulo adachenjeza okhulupirira a mpingo wa ku Ahebri, “Tigwiritsitse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane ku chikondano ndi ntchito zabwino osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandawulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku lirikuyandika.” (Ahebri 10:23-25).

Tiyenera kupitirira kuwona kuti Ambuye anakhazikitsa ma sakramenti awiri omwe ayenera kutsatiridwa ndi Akhristu mu mpingo. Ma sakramentiwa ndi Ubatizo ndi Chakudya cha Ambuye (Mgonero), zomwe ziri mboni zapoyera za imfa ndi kuwukanso ka Ambuye Yesu. Pokhudza ubatizo, mtumwi Paulo analemba kuti;

41

Umboni Wa Mpingo

“Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake tinayikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muyimfa; kuti monga Khristu anawukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizo cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake.” (Aroma 6:3-6). Chimodzimodzinso, Paulo analemba ku mpingo wa Akolose; “Munaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mu ubatizo, momwemonso munawukitsidwa pamodzi ndi Iye mchikhulupuriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuwukitsa Iye kwa akufa.” (Akolose 2:12).

Pokhudza za Chakudya cha Ambuye (Mgonero) timawerenga kuti “Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate; ndipo mmene adayamika, ananyema, nati ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukilo changa. Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukilo changa. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.” (1 Akorinto 11:23-26).

Ambuye sanapereke ma sakramenti awa kuti tiwanyalanyaze. Kodi timawerenga mu Baibulo za okhulupirira owona, ophunzitsidwa ndi Mzimu Woyera, omwe ayenera kupatulidwa kuti asalandire ma sakramentiwa? Kumvetsa chisoni kwa kusalandira chakudya cha Ambuye kwa anthu ambiri mu mipingo zisonyeza kusowa kwa chiphunzitso cha uzimu wa mtima. Mawu a Mulungu anena momveka bwino kuti: “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.” (Yohane 14:15).

Kufala kwa Uthenga Wabwino.

Ngati pali chikondi chowona cha kumukonda Ambuye ndi chidziwitso cha chipulumutso, pamenepo padzakhala chikhumbo chochokera pansi pa mtima chofuna kuti ena amve Uthenga Wabwino ndi kuukhulupirira. Izi ziyenera kukhala ndi zotsatira za kupemphera ndi kuchitachita kokhudzika kwa kulalikira kwa Uthenga Wabwino, poyamba pa munthu aliyense payekha komanso m’mipingo. Koma wina angathe kufunsa, “kodi Mulungu si amene amapulumutsa anthu ake osankhidwa mu chifundo chake chapadera?” Kodi ndi koyenera kuti munthu angathe kuyikapo dzanja lake lochimwa pa chipulumutsocho?

Zowonadi, chipulumutso ndi cha Mulungu, osati munthu. Yesu anati, ”Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja. Kulibe m’modzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate

43

Umboni Wa Mpingo

wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomariza.” (Yohane 6:37 ndi 44). Komabe, kuli kwakuti ndi cholinga cha muyaya cha kuti, “ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza Mawu a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48), ndi cholinga chakenso kuti ochimwa apulumutsidwe kudzera mu kulalikira kapena kufalitsa kwa Uthenga Wabwino.

Kotero kuti, Yesu anapereka ntchito yake yayikulu kwa ophunzira. “Mukani ku dziko lonse la pansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.” (Marko 16:15). “Ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.” (Luka 24:47). Mtumwi Paulo analangiza Timoteyo kuti; “Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uyike kwa anthu akhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.” (2 Timoteyo 2:2). Lemba ili ndi lamulo kwa mipingo, kufikira lero, kuti iyesetse kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuphunzitsa chiphunzitso cholama.

Tiyeni tilankhule momveka bwino , palibe kusiyana kulikonse pakati pa kulalikira kwa poyera kwa Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu ndi chiphunzitso cha kusankhidwiratu, chomwe chimaphunzitsa kuti ndi anthu osankhidwa ndi Mulungu omwe amapulumutsidwa. Kodi chiphunzitso chakuti Mulungu ndi mwini mphamvu yekha mu chipulumutso chidali chotchinga kwa Paulo ndi Petro mu utumiki wawo? Kodi chidamutsogolera Martin Luther ku ulesi kapena kusasiyana kokhudza osakhulupirira? Yankho lake lotsindika ndi la kuti, ai! Monga tafotokoza kale, Ambuye Yesu anaphuzitsa za kusankhidwa, mosabisa; ndipo alipo nanga mkhristu yemwe angayerekeze kuti Yesu analakwitsa pakutero? Komabe, sitimawerenga za Mulungu mu mphamvu yake yonse kuti ndiye chiphunzitso chokhacho m’Baibulo; kapena kuti linali phunziro lokhalo la ma ulaliki kapena makalata a atumwi. Pali kugwirizana kwa uzimu apa.

Mtumiki wa chikhristu alibe udindo wakudziwa yemwe ali mu msonkhano yemwe angathe kumva Mawu a chowonadi omwe amatengera munthu ku chipulumutso cha moyo. Lamulo ndi lakuti, “Lalika amu; chita nawo pa nthawi yake, popanda nthawi yake, tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.” (2 Timoteyo 4:2). Palinso chilimbikitso chotsatirachi kwa iwo omwe ayitanidwa kufesa mbewu ya Uthenga wabwino, kaya ndi pa guwa, pogawa mathirakiti okamba za Mulungu kapena kuchitira umboni. “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola. Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m’mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu

44

Umboni Wa Mpingo

amene achita zonse. Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.” (Mlaliki 11:4-6).

Pomwe mphamvu za uMulungu za Mulungu ziyang’anidwa moyenera mwa chikhulupiriro, mtumiki wolalikira Uthenga Wabwino, kapena mkhristu yemwe akuchitira umboni wa Yesu, adziwa kuti zotsatira zimagonera pa Mulungu, ndi kuti angathe kudalira mwa ufulu mwa iye pa zonse. Chilimbikitso chachikulu ndi chakuti chilimbikitso sichimadalira pa mitima yawo yochimwa yosakhulupirika kapena pa ntchito zawo. Ambuye adzalandira ulemu ndi ulemerero mu chipulumutso cha miyoyo, ndipo mwa chikhulupiriro amakhutitsidwa kuti ziyenera kukhala choncho. Koma kuchokera mu kumkonda Ambuye, amakhala ochitachita potsatira lamulo lake lakuti akhale mboni zokhulupirika za chipulumutso chachikulu chotere. Ngakhale kuti zinalembedwa kuti Paulo “anafika kundunji kwa Musiya, anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza.” (Machitidwe 16:6-7), chinali chifukwa chakuti Ambuye mwa chisomo analamulira kuti utumiki wa Paulo udalitsike kwakukulu mu Makedoniya. Osakhala kuti chinali chopezerapo mwai kuchita ulesi mu utumiki, chinali mbali imodzi ya chitsogozo cha Ambuye ku dela la utumiki lomwe Uthenga Wabwino unayenera kupambana.

Mphamvu za uMulungu za Mulungu pa chipulumutso siyimathetsa nkhani yakuti chiwombolo chimadalira pa ntchito zabwino za ochimwa. Imatsutsanso chidziwitso cholakwika chakuti chipulumutso chimagonera potsatira mtumiki wapadera kapena mpingo wapadera. Tiyenera tikumbukire nthawi zonse kuti mtumiki ayenera kupatsidwa ulemu, koma sayenera kuyikidwa m’malo mwa Mulungu (2 Atesalonika 2:1-4).

Nkhani Yabwino ya Uthenga Wabwino.

Pomwe Uthenga Wabwino walalikidwa mokhulupirika, pamakhala kulengeza kwa Uthenga Wabwino, kapena nkhani yabwino, chifukwa ichi ndi chomwe Mawu akuti Uthenga Wabwino amatanthauza. Mutu wake wa ukulu ndi kumasulidwa, kudzera mu kulapa komanso chikhulupiriro mwa Yesu Khristu, kuchoka ku chiweruzo ndi mkwiyo wa Mulungu chifukwa cha uchimo. Ichi ndi chimwemwe kwa mtima uli wonse wokhulupirira womwe ukufufuza chikhulukiro cha machimo. Komabe, kwa iwo omwe sakhuluprira, ndipo afuna kuti akhalebe mu chomwe iwo achiyesa mwa iwo okha kuti ndicho chilungamo, kwa otere Uthenga Wabwino ndi chowatsutsda (Aroma 9:30-33, 1 Petro 2:8). Panali ena omwe adatsutsidwa ndi chiphunzitso cha

46

Mboni Wa Mpingo

Yesu mwini, ngakhale ena a ophunzira ake anati, “Mawu awa ndi usautsa; akhoza kumva awa ndani?” (Yohane 6:60). Ngati anthu adakhumudwa ndi Mawu a Ambuye, kodi antchito ake sadzapezanso ena ambiri lero omwe angakhumudwe ndi kulalikira kwa Uthenga Wabwino? Tiyeni tisunge ichi nthawi zonse m’malingaliro kuti kulalikira za Yesu ndi chosowekera kwambiri pa utumiki wa Uthenga Wabwino. Paulo analemba ku mpingo wa ku Korinto kuti, “Pakuti ndatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.” (1 Akorinto 2:2). Pamene Yesu analalikidwa ndi pomwe dalitso la chipulumutso linabwera ndi mphamvu. Paulo chifukwa cha ichi akadakhoza kunena kwa anthu a ku mpingo wa ku Aroma, “Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene. Pakuti m’menemo chawonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.” (Aroma 1:16-17).

Tiyeni tsono tidzifufuze tokha, Kodi Yesu akulalikidwadi pakati pathu, kapena Uthenga wa ukulu mu utumiki uli chiphunzitso china chake? Inde, pakusowekera chilangizo mu ziphunzitso zokhala ngati malamulo khumi, kulephereka kwa kudzipulumutsa yekha kwa munthu, dongosolo la mpingo, mphamvu za Mulungu mwini, ndi chikondi kwa abale (pakungonenapo zochepa zokha). Koma pokhapo pakuti zikuloza kwa Yesu, utumiki ndi umboni wa mpingo udzakhala wopanda moyo wa uzimu ndi mphamvu. Kodi timakhutitsidwa pakungomva Ma uthenga ongotchula dzina la Yesu? Ngati ziri chomwecho, ndiye kuti tachokeratu kwenikweni pa Khristu.

Atumiki, omwe amagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Mulungu pakupulumutsa miyoyo ya ochimwa ndi kulimbikitsa okhulupirira, ndi omwe amakweza Ambuye Yesu ndi kubweretsa mwa Mzimu mphamvu yake ndi kukongola kwake. Monga Paulo analemba kwa a ku mpingo wa ku Korinto, “Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silvano ndi Timoteyo) sanakhala eya ndi iyayi, koma anakhala eya mwa Iye. Pakuti monga mawerengedwe a malonjazano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.” (2 Akorinto 1:19-20). Popanda Yesu Khristu sipadzakhala chimwemwe ndi mtendere mwa kukhulupirira.

Komabe, tiyeni tichenjezedwe kuti utumiki wa Uthenga Wabwino, womwe tikhoza kuwutchula bwino kuti utumiki “wakuyeserera”, siwumangokhala ndi kulawa kwa kulalikira kokha. Payenera kukhalanso zinthu zitatu za magawo omwe apanga utumikiwu, monga zasonyezedwa machitidwe ake mu makalata a Paulo. Izi ndizo

47

Umboni Wa Mpingo

chiphunzitso, zomwe takumana nazo, ndi kugwira ntchito. Popanda maziko a chiphunzitso chabwino ndi malangizo mu malemba, zokumana nazo zina zoyipa zingathe kuwoneka ngati kuti ndi zochokera kwa Mzimu Woyera, ndipo tingathe kugwa mu chinyengo cha Satana ndi mitima yathu yochimwa. Paulo analemba kwa Timoteyo kuti, “Ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu, Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo; kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:15-17). Koma ngati utumiki ungofikira nzeru kapena malingaliro okha, ndiye kuti uli wakufa ndi wowuma; payenera kukhalanso kulawa kwa mphamvu ya Uthenga Wabwino. Chifukwa cha ichi Paulo analemba: “ Ndipo Mawu anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi Mawu okopa a nzeru, koma m’chiwonetso cha mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya munthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 2:4-5). Chimodzimodzinso, pokhapokha patakhala kuyika mu ntchito kwa Mawu a Mulungu, ndiye kuti tingokhala onyenga basi. Chidziwitso china chili chonse cha chiphunzitso chowona kapena kuti talawa zotani mu utumiki, chikhulupiriro chathu ndi chakufa ngati sichiphatikana ndi kuyenda mu malamulo a Yesu. “Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.” (Yakobo 2:26). Tiyeni mwa pemphero tifufuze chisomo chakuti tidziwe chiphunzitso choyenera, zomwe tiziwona, komanso kuchita.

Mkwatibwi wa Khristu.

Pomwe tikumaliza mutu uwu, tiyeni tikumbukire kuti mpingo wowomboledwa ndiwo mkwatibwi wa Ambuye Yesu Khristu wowuka kwa akufa. Mtumwi Paulo akukhazikitsa izi mu chifanizo cha ukwati wa anthu a pansi pano. “Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, Iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina. Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anawukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso. Pakuti pamene anali m’thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinali kuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso. Koma tsopano

48

Umboni Wa Mpingo

tinamasulidwa ku chilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ayi.” (Aroma 7:2-6).

Mu ntchito zake ndinso kukhudzika kwake pa mpingo wa ku Korinto, mtumwi Paulo analemba kuti; “Pakuti ndinakulipatsani ubwenzi mwamuna m’modzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.” (2 Akotinto 11:2). Tiyeni titsogozedwe monga mipingo ku chowonadi ichi, kuti maso athu akhazikike pa Khristu yekha osati pa wina aliyense. Tiyeni tifunefune ulemerero wake, osati wa ife tokha. Chikondi chathu pa iye chiyatsidwe ndi Mzimu Woyera, podziwa kuti okhulupirira owomboledwa anavekedwa ndi chovala cha ukwati cha ulemerero, chomwe ndi chilungamo cha Khristu.

Timaliza ndi zolingalira za Hallgi’mur P’etursson zokhudza mnthiti molasidwa mwa Ambuye Yesu. Izi zikadziwidwa m’mitima mwathu, padzakhala chikondi chanthete cha pa abale, kuyenda mchifupi ndi Mulungu ndi umboni monga mwa Mawu a Mulungu womwe umveka bwino mu mipingo. Tiyeni tifunefune madalitso awa mwa pemphero.

Adamu payekha anazindikira Mulungu anamulengera mkwatibwi Tulo tofa nato ululu nupeputsa Anamtenga pa mbali yovulazidwa Kwa mwamuna adziphatika nthawi zonse. Pamodzi ndi mwamuna wake akhala muyaya. Momwemonso kwa Khristu mkwatibwi wake napatsidwa. Wotengedwa pa mbali pake povulazidwa. Ndi mkondo mbali mwake munang’ambidwa. Kumasula funde loyeretsa Apo machimo ake onse nakhululukidwa Mkwatibwi kwa nthawi zonse napatulidwa. Onani, moyo wanga! Ndi masomphenya akumwamba, Mwazi ndi madzi inu muzidziwa Kwa inu Mulungu anapereka, Kubatizidwa mu mtsinje woyeretsa.

49

Umboni Wa Mpingo Chikhupiriro chivomera kuzindikira Zachisomo chomwe Iye wapereka. Monga Mbuye wachisomo waloleza Tomasi wokayika anayandikira, Mwa kukhudza kwake iye nagonjera, Apo kuyandikira Iye ine sindingachite? Zikayiko ndi mantha zomwe zagonjetsedwa. Pomwe kulasidwa kwake ine ndiwona patali. Kuchokera mumtima wake mitsinje ya machiritso, Kukhetsedwa kuti ipulumutse anthu Ake, mwazi unayenda; Chisamaliro cha Mulungu chonse ndi chikondi ziwululidwa, Chikondi chake chonse pa ife chakhazikitsidwa. Pomwe, ufulu wa chiwomboli chasindikiza, Anapereka ngongole yomwe tinali nayo. Kuti ndithe kuwona bwino lomwe. Muyeso wathunthu wa chisomo chake. Amavumbulutsa mabala ake bwino lomwe; Anandibweretsa kwa iye maso ndi maso, Kuti mapazi Ake ine mowona mtima Ndi modzichepetsa kwambiri ndithe kuzikumbatira. Kudzera mu mtima wa Khristu, Mpulumutsi wanga. Chikhulupiriro pa kumwamba kwa Mulungu chiwone; Mu kuwala kwa dzina kwa kukondera kwa Mulungu. Chiwothera kwa masiku amuyaya; Cholimbikitsidwira chikhalidwe chachipembedzo, Kuyenda mu njira zake zoyera. Israeli, ndi mneneri Mose Anamva ludzu mu chipululu. Mulungu, mu chifundo, akhala pakati; Achita changu kuthandiza mu zisoni zawo. Mose ndodo yomenya itsegula. Mitsinje yozizizra kusangalatsa ndi kudalitsa.

50

Umboni Wa Mpingo Zinafotokozedwa kuti tiphunzirepo Malemba akuti: “nthanthwelo ndi Khristu”. Pomwe mtima wa Mpulumutsi unang’ambidwa, Mwa ndodo ya ulemerero chiweruzo analangidwa, Madzi amoyo, achokera kumwamba, Ludzu lathu la muyaya linathetsedwa. Pambali pa kasupe uyu ine ndikhala; Ndimeza pomwe mtsinje wonyezimira uyenda; Ludzu, mantha ndi kukayika zichotsedwa, Pano okhutitsidwa ndi mtendere ndidziwa, Ndi chimwemwe choposa zimwemwe zonse, Mukusefukira kodabwitsa. Onani, Ambuye, womwe mtima wanga aliri, Wotsutsika, odzala ndi uchimo, ndili nawo. Imvani. Inde imvani kupempha kwanga tsopano- Lilani mwazi wanu wamtengo uteteze. Pakuti inu muli sing’anga wamkulu, Inu mutha kuchiza, ide Inu nokha. Tsopano mtima wanga matamando olimba, Upereka nthawi zonse kwa inu, Pakuti mwazi wanu machimo anga ufananiza; Ubweretsa moyo wosatha kwa ine. Nyimbo kwa Inu mzimu wanga ukweza, Tsopano ndiponso mpaka Muyaya. (Kuchokera ku mamasulidwe a Chingerezi a G. Gook).

51

MUTU 5

CHITSIMIKIZO MKATI MWA MAYESERO.

Njira za Mulungu ndi Zangwiro.

Tangolingalira za chiyanjano cha oyera mtima mwa Ambuye Yesu ndi umodzi wa

uzimu wa abale. Komabe, pali mfundo ina yokhudza chiyanjano, yomwe analankhula Paulo. “Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Khristu, ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro; kuti ndim’zindikre Iye, ndi mphamvu ya kuwuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake.” (Afilipi 3:8-10).

Ichi chilankhula za zinthu ziwiri zotsutsana. Poyamba, pali kuzunzika chifukwa cha zomwe zatayika ndiponso mayesero akuya. Chachiwiri pali chidziwitso cha ulemerero cha Yesu Khristu ndiponso chitsimikizo cha chipulumutso. Mkhristu ayenera kuyenda mu zinthu ziwiri zonsezi. Komabe zinthu izi ziri chinsinsi chathunthu kwa iwo omwe sanaphunzitsidwe ndi Mzimu Woyera. Si chachilendo kumva za iwo omwe sadziwa za Yesu Khristu mumtima, omwe amanena kuti sangakhulupirire kuti Mulungu angalole mazunzo, ululu kapena kumwalira kwa achibale masiku awo asanakwane. Mulungu wa malingaliro awo ndi yemwe angalole aliyense kuti asangalale ndi zinthu za moyo uno, Ngakhale anthu a Ambuye amayesedwa ndi zinthu zimenezo. Ngakhale ziri chomwecho chowonadi cha Mulungu sichimagwedezeka.

Tiyeni tsopano tifunefune kuti tiyang’ane ku machitachita a Ambuye kwa anthu ake okondedwa. Ambuye asangalatsidwe ndi kuti avumbulutsire chikondi chake ndi zolinga za mphamvu ya uMulungu wake, makamaka iwo omwe akuwona kuti akumira chifukwa cholemedwa ndi mayesero ena. Tiyeni tipemphere mowona mtima kuti Mzimu Woyera atipatse chikhulupiriro chomwecho komanso kuzindikira monga Davide. “Ndipo mudzapulumutsa anthu osawutsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzawunika mumdima mwanga. Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; ndi Mulungu wanga ndilumphira linga. Kunena za Mulungu, njira yake iri yangwiro; Mawu a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu? Mulungu ndiye linga langa lamphamvu; ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.” (2 Samueli 22:28-33).

52

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

Chipatso cha Chimo.

Pali chitsimikizo chochuluka chotizungulira kuti mazunzo, kuvutika ndi mayesero ndi zambiri kwa amuna ndi amai onse. Monga Baibulo linena, “munthu abadwira mavuto, monga mbaliwali zikwera ziwuluzika.” (Yobu 5:7). Tiyeni potero tifufuze chifukwa chake izi ziri chomwecho. Ili ndi funso lomwe limafunsidwa kawiri kawiri, koma pamakhala popanda yankho lokwanira. Mwachisoni, anthu ambiri safunsa kwa Mulungu mwa chikhulupiriro, koma amangosankha kufunafuna mayankho opanda pake a m’malingaliro a anthu anzawo.

Yankho la m’malembo ligonera mu nkhani ya kugwa mu uchimo kwa munthu, pomwe Adamu ndi Hava adachimwa mu munda wa Edeni. Mulungu atatemberera njoka (kapena Satana) chifukwa cha chinyengo, timawerenga kuti Ambuye analankhula kwa Hava Mawu awa, “Ndidzachulukitsa kusawuka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala; udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe. Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera Mawu a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuwuza iwe kuti, usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; mkusawuka udzdyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo; m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera ku nthaka; chifukwa kuti m’menemo unatengedwa; chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:16-19).

Adamu ndi Hava sikuti anangowonongeka iwo okha pakugwa mu uchimo, komanso mtundu wonse wa anthu. “Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m’dziko la pansi mwa munthu m’modzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12). Kotero kuti, moyo uwu umakhala ndi mayesero ambiri, zosamvetsetseka ndi zokhumudwitsa. Wina wolemba Chipangano Chakale anafuwula: “Ndawona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi za chabe ndi kungosawutsa mtima. Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe.” (Mlaliki 1:14-15). Choyambitsa chenicheni cha masawutso, imfa ndi mazunzo ndicho uchimo. Tiyeni tizindikire kuti uchimo womwe wabweretsa zonse izi siwokhawo wa anzathu komanso wa ife tomwe.

Dzanja la Kulanga la Ambuye.

Komatu pali yesero lozama lomwe mkhristu anayitanidwa kuti adutsemo. Ili ndilo

53

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

vuto la moyo, lomwe anthu osakhulupirira samadziwa za ichi. Apa tikutanthawuza za yesero la mkati ndi katundu wolemedwa ndi machimo a iwe mwini, momwe wochimwa amamva za chiyero cha Mulungu ndi mkwiyo wotsutsa chimo. Izi sizimamveka pokhapo pomwe Ambuye akutitsutsa za uchimo mu mtima, komanso kutsatira apo nthawi ndi nthawi pomwe mkhristu akudutsa mu nthawi ya kuzunzika mu moyo. Izi nthawi zambiri timaziyamba tokha, kukhumudwitsa Mzimu Woyera.

Timawerenga za Petro, pomwe adamukana Ambuye Yesu, adafika mu kusawutsika kopweteka ndi kozama, mu moyo wake. (Luka 22:54-62). Momwenso Davide adafika mu madzi akuya, pomwe mneneri Natani adamutsutsa za chimo la chigololo komanso kupha chifukwa cha Beresheba. (2 Samueli 11 ndi 12). Kenaka Davide anafuwula ndi kulapa; “Pa Inu, Inu nonkha, ndachimwa, ndipo ndinachichita choyipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera. Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala. Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera; kuti mafupawo munawathyola akondwere. Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. Mundilengere mtima woyera, Mulungu; Mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga. Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.” (Masalmo 51:4,7-12). Ngakhale kuti mwa chisomo anamukhululukira Davide mwa Muwomboli wodalitsika, Ambuye adawona kuti ndi koyenera kuti amufikitse Davide mu mayesero ozama mu banja lake ndi ufumu wake, mu moyo wake onse, Davide anayenera kuti ayende mu njira ya kusawutsika kozama kwa moyo, ndipo zinalembedwa mu Baibulo kuti zikhale phunziro kwa ife.

Tiyeni pakutero tsopano tilingalire kuti izi si Davide yekha komanso anthu ake onse a Ambuye ndi kuti onse “ayenera kulowa ufumu wa Mulungu ndi zisawutso zambiri.”(Machitidwe 14:22). Ena amayitanidwa kuti ayende mu mayesero ozama kusiyana ndi ena; komatu Ambuye adzawonetsetsa kuti aliyense wa anthu ake aphunzire zotsatira zowawa ndi zokondweretsa za uchimo, kuti asadzikuze kapena kudalira mphamvu zawo. Chifukwa cha ichi adzatsogoleredwa kuti tsiku ndi tsiku afunefune chisomo ndi chifundo mwa Yesu Khristu. Ngakhale kuti Ambuye wachotsa machimo onse a anthu ake kwa muyaya, adzapangitsa iwo kuti akumbukire mu moyo umo za chimo, kuti onse athe mowona mtima kuthawira kwa Yesu. Ambuye mu zolinga zake za muyaya amangwiritsa ntchito izi kuti achepetse, aphunzitse ndi kusunga anthu ake mu njira za chilungamo, kuti athe kulandira madalitso a

54

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

chipulumutso. Mtumwi Paulo analemba; “podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masawutsowo, koteronso ndi chitonthozo. Koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuwukitsa kwa akufa.’ (2 Akorinto 1:7,9). Timazindikira pang’ono za zinthu zomwe tinayenera ife kuwomboredwako kudzera mu njira zomwe zimachepetsa za Ambuye.

Tiyeni tilimbikitsidwe ndi nyimbo ya wolemba Masalmo, yemwe adayesedwa pakusilira opusa pomwe adawona kulemera kwa anthu ochimwa. Adawoneka kwa Iye kuti sanali mu mavuto monga ena. Koma pomwe wolemba Masalmo adafika ku nyumba ya Mulungu, pomwepo anazindikira chitsiriziro cha oyipa. “Indedi muwayika poterera: muwagwetsa kuti muwawononge. Ha! M’kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zowopsya. Monga anthu atawuka, apepula loto; Momwemo, Inu Ambuye, pakuwuka mudzapeputsa chithunzithunzi chawo. Pakuti mtima wanga udawawa, ndipo ndinalaswa m’imso zanga; ndinali wam’thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu. Koma ndikhala ndi Inu chikhalire: mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira m’ulemerero. Ndiri ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo pa dziko la pansi palibe wina wondikonda koma Inu. Likatha thupi langa ndi mtima wanga: Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha. Pakuti, tawonani, iwo okhala patali ndi Inu adzawonongeka; Muwononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu. Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.” (Masalmo 73:18-28).

Yeremiya adabweretsedwa mu mayesero ozama komanso chisoni mu moyo wake, pomwe adawona kusiyidwa kwa Yerusalemu chifukwa cha uchimo wa ana a Israeli. Komatu adatha kunena; “Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka; chiwoneka chatspano m’mawa ndi m’mawa; mukhulupirika ndithu. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira. Yehova akhalira wabwino omlindira, ndi moyo womfuna funa. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindira modekha chipulumutso cha Yehova. Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuruka kwa zifundo zake.” (Maliro 3:22-26,32).

Ambuye amalola masawutso popeza amabweretsa phindu la muyaya la mkhristu. Dzanja lake la chikondi, komanso lolanga, lomwe limatifikitsa ife mu njira izi. Uwu ndi mwawi wosungidwira iwo okha omwe ali ana a Mulungu. Tiyeni tiyang’ane Kumwamba mwa chikhulupiriro ndi kusaiwala “dandawuliro limene linena nanu

55

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

monga ndi ana, Mwana wanga, usayesa chopepuka kulanga kwa Ambuye, Kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye amukonda amulanga, nakwapula mwana ali yense amulandira.” (Ahebri 12:5-6).

Kuyanjana ndi Khristu mu Zivutiko zake.

Tawona za njira ya mazunzo ya mkhristu, yomwe imagwiritsidwa ntchito ndi Ambuye kuti atilange chifukwa cha machimo. Koma tingathe bwanji kukhala m’chiyanjano ndi Khristu mu mazunzo ake, pomwe Ambuye Yesu anali wopanda chimo, ndipo ife ndife wochimwitsitsa. Yankho likupezeka mu Mawu a Paulo: pakuti Mulungu Atate “anamuyesera Yesu uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.” (2 Akorinto 5:21). Ambuye Yesu Khristu sanazunzike chifukwa cha chimo lake, koma chifukwa cha machimo athu omwe anayikidwa pa Iye. Mneneri analemba zokhudza Yesu: “Zowonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu ndi wovutidwa. Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundunduzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamugwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa. Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anayika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.” (Yesaya 53:4-6).

Ambuye Yesu anazunzika kwambiri mu thupi lake kuchokera mu nkhanza za asirikali a chiRoma, komatu sitimamva ngakhale liwu limodzi la chidandawulo kuchokera pa milomo yake yoyera. Sitimawerenga kuti Ambuye Yesu analira chifukwa cha kutonza kwa nkhanza kapena ululu wa mu thupi lake koma chifukwa cha kupachikidwa pa mtanda. Anakwaniritsa Mawu a mneneri Yesaya, “Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pake.” (Yesaya 53:7). Komatu m’mbuyo mwake Yesu ali pa mtanda “tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.” (Yohane 19:30), analira kuchokera pa mtanda mu ululu wa ukulu mwa Mawu womwe ali pa Masalmo 22: “Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46). Izi zikuwonetsera za mawululu akulu ndi masawutso a moyo wake wa umunthu, zomwe zidaposa masawutso a thupi lake; chifukwa Iye “(Yesaya 53:12). Ichi chinachitika kupulumutsa miyoyo yodetsedwa ndi chimo, ya anthu ake wokondedwa, kuti awomboledwe ku mavuto onse a moyo ndipo pamapeto pake adzabweretsedwe ku kukhala ndi Iye mu ulemerero.

Tili ndi chiyanjano chowona ndi Iye mu masawutso ake, pomwe tabweretsedwa mwa

56

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

chikhulupiriro “tiyang’ana pa Iye amene anampyoza.” (Yohane 19:37, Zakariya 12:10), pozindikra kuti masawutso a Ambuye anawafikira chifukwa cha machimo athu. Izi zimabweretsa kulira ndi kulapa kowona. Mwina mkatikati mwa mayesero owawa ndi momwe mkhristu amayesedwa kukhala kakasi, kapena kumva chisoni chifukwa cha momwe aliri; pomwe mwadziddzidzi ayang’ana Kumwamba mwa chikhulupiriro ndi kuzindikira kuti Ambuye Yesu adadutsa mu yesero lomwelo, koma mu njira yozama yosatha. Kodi mkhristu wathawidwa ndi abwenzi? Ambye Yesu anasiyidwa ndi kukanidwa ndi ophunzira omwe amakhala naye pafupi kwambiri. Kodi mkhristu ali mu mayesero akulu. Ambuye Yesu “wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.” (Ahebri 4:15). Zonsezi, kuti anthu ake wokondedwa athe kumasulidwa ndi kuwomboledwa! Kotero kuti, tingathe “kulimbika mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi ya kusowa.” (Ahebri 4:16). Apa mkhristu angathe kunena pamodzi ndi mtumwi Paulo; “Pakuti chisawutso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukuru ndi kosatha kwa ulemerero.” (2 Akorinto 4:17).

Pamene mayesero athu awonedwa ukulu wake, ndi kuti Mzimu Woyera nativumbulutsira ife ukoma wa chipulumutso, padzakhala pamenepo kusangalala ndiponso mtendere womwe “umaposa chidziwitso chonse”. (Afilipi 4:7). Tidzapeza zomwe Yakobo analemba: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu, pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.” (Yakobo 1:2-3). Mkatikati mwa zochitika zomvetsa chisonizi zomwe zinayenera kufika pa ana a Israeli chifukwa cha machimo, mneneri Habakuku adakhoza kunena, “Koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.” (Habakuku 3:18). Tiyeni, monga mneneri wakale tifunefune chisomo chakutsatira chilimbikitso cha Mtumwi Paulo: “Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero kondwerani.” (Afilipi 4:4).

Kudzera mu chigonjetso cha ulemerero cha Ambuye Yesu Khristu pa chimo, dziko ndi zimphamvu za oyipa ndi momwe madalitso awa amaperekedwa. Monga Ambuye ananena kwa ophunzira usiku womaliza asanafe; “Zinthu izi ndilankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko la pansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko la pansi Ine.“ (Yohane 16:33). Monga Mtumwi Yohane analemba mu kalata yake, “Pakuti chiri chonse chobadwa mwa Mulungu chililaka dziko la pansi, ndipo ichi ndi chilako tililaka nacho dziko la pansi ndicho

57

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wolilaka dziko la pansi koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu.” (1 Yohane 5:4-5).

Kenaka mwa chikhulupiriro mkhristu amatsogoleredwa kuti awayang’ane mayesero mu njira yosiyana ndi ya yemwe ali wosakhulupirira. Mkhristu amapatsidwa kuthekera kwakuti akhoza kudalira mwa Ambuye ndi chitsimikizo, kuyenda mu chilimbikitso cha Petro, “Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani; kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukurukuru. “ (1 Petro 4:12-13).

Cholakwika cha Kuchoka pa Chowonadi.

Pa nthawi ino tiyenera kuti tisamalire kuti phunziro la chitsimikizo ndi lomwe kawiri kawiri silimamvetsetsedwa bwino. Chenjezo likusowekera lokhudza nkhani iyi. Pali mbali ziwiri zomwe zimadutsidwa malire zomwe mkhirstu ayenera kuzipewa. Poyamba tiyeni tiwone kwa iwo omwe amalakwitsa pa kukhazikika pa chitsimikizo cha chomwe amadziwa pang’ono mu uzimu.

Ena ananena, koyambirira pa nthawi yomwe adayamba kukhulupirira, kuti anakhala nacho chitsimikizo nthawi zonse ndi kuti sanavutikepo ndi zikayiko, mantha kapena kusakhulupirira. Komabe, ufulu wotere ku zipatso za uchimo ndi wa mpingo wokhawo wogonjetsa wa Kumwamba, kumasangalala ndi kupezeka kwa muyaya kwa Mulungu ndi Mwana wa Nkhosa, Ambuye Yesu Khristu. Pakuti palibe mkhristu yemwe anganene zowona kuti iwo alibe chimo. (1 Yohane 1:8), apa ndiye kuti kumakhala kudzinyenga tokha, ponena kuti nthawi zonse amakhala nacho chitsimikizo chosagwedezeka.

Cholakwika ichi nthawi zambiri chimagwirizana ndi “kukhulupirira kosavuta”, chomwe chili matenda omvetsa chisoni omwe ali pa ambiri omwe ali akhristu. Ichi chiyenera kukhala chochititsa mantha kuti iwo omwe amanena kuti ali ndi chitsimikizo cha chipulumutso, samadziwa za ukali wa chimo ndi chiyero cha Mulungu. Ambiri a anthu awa amafanana ndi mbewu yomwe “inagwa pa nthaka yathathwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya; ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.” (Marko 4:5-6). Ambuye Yesu anatanthawuzira kuti, ichi chiyimira iwo, omwe, “atamva Mawu awalandira pomwepo ndikusekera; ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masawutso kapena mazunzo chifukwa cha Mawu, pomwepo akhumudwa.” (Marko 4:16-17).

58

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

Anthu ena, pokhapokha Ambuye mwa chifundo chake atsegule maso awo akhungu, adzapitirira mu chinyengo chofewa cha kukondwerera ndi chipembedzo chopepuka mpaka pomwe adzawonekera pa mpando woweruza wa Mulungu. Ambuye analankhula motere za anthu awa, “si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera Mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoyipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:21-23). Tiyeni potero tisamalire pa kusunga Mawu ofunika kwambiri. Tiyeni tisanthule mitima yathu yomwe, kuti tiwone ngati chimo ndi chipulumutso timazidziwadi, kapena kuti ndi chinthu chakungowoneka kunja kwa miyoyo kwathu kokha.

Pomwe mkhristu weniweni agwa mu chimo kapena kulakwitsa, Mzimu Woyera amamumvetsedwa chisoni. Ambuye pamenepo amalanga pakuchotsa kupezeka kwake komwe timakumva, kuti mkhristu athe kudziwa mu chikumbu mtima ndi moyo wake kuti wachita cholakwika. Pogwiritsa ntchito njira iyi Ambuye mwa chisomo amafikitsa anthu ake kuti alape ku kubwerera m’mbuyo kwawo ndi kuti abwere mowona mtima, ndi kulilira kukonzedwanso kwa miyoyo yawo mwa chifundo cha Mulungu.

Pochenjezedwa mwa iwo omwe sasamalira za chiphunzitso cha chitsimikizo, pali Akhristu ena omwe amapyola malire ku mbali yotsutsana ndi iyi. Pakuwopa chipembedzo chomwe chilibe maziko a uzimu kapena kutsutsidwa kwa chimo, amagwa mu cholakwika cha kunyalanyaza dalitso la chitsimikizo cha chikhristu. Kukana chitsimikizo chimenenchi kukhoza kukhalapo mwakusadziwa, koma chikhoza kulimbuikitsidwa ndi utumiki womwe nthawi zonse umakhazikika pa chimo, zikayiko, mantha, mayesero, kusakhulupirira ndi kulephera kwa mkhristu. Zotsatira zake, mulingo womwe unakhazikitsidwa mu mpingo umaperewera zambiri za zipatso za Mzimu Woyera, monga chikondi, chimwemwe, mtendere, ndi chikhulupiriro (Agalatiya 5:22). Utumiki wu si umakhala nthawi zonse ndi uthunthu wa nkhani yabwino ya chipulumutso mwa Yesu Khristu. Zotsatira zake, ambiri mu misonkhano amayikidwa mu malingaliro akuti, zikayiko, mantha, kusakhulupirira ndizo zizindikiro za chikhristu chowona. Potero iwo amayang’ana modabwa iwo omwe akuyenda mu chikondwerero cha chitsimikizo ndi ufulu wa chipulumutso mwa Yesu Khristu.

Tiyeni tiwone momveka bwino: zikayiko, mantha a umunthu, ndi kusakhulupirira ndi zipatso za uchimo. Osati za Mzimu Woyera. Mawu akuti,”Kodi anati Mulungu?”

59

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

analankhulidwa ndi chinjoka osati ndi Mpulumutsi (Genesis 3:1). Kusakhulupirira, pamodzi zatsatira zonse za zikayiko, zimachokera ku kugwa mu uchimo kwa munthu, osati chipatso cha chiwombolo chake mwa Khristu Yesu. Ngakhale ziri choncho, timakondwera kuti Ambuye ali ndi chifundo kwa ochimwa, omwe ali akufa m’chosalungama ndi chimo. Iye mu chisomo chake samawasiya mu chimo. Kodi ulemerero ndi ulemu wa Ambuye ukadakhala kuti mu mpingo, pakadakhala popanda zitsimikizo zamoyo za chikhulupiriro, popanda kufika kwa Mulungu ndi kulimbika mtima mu pemphero popanda kugwiritsitsa malonjezo a mtengo wapatali, kapena popanda chikondwero cha matamando cha Muwomboli wa mtengo wapatali? Pamalo pomwe Yesu akulalikidwa mokometseta, Uthenga wabwino udzadza “mu mphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m”kuchuruka kwakukuru.” (1 Atesalonika 1:5).

Tiyeni ife potero tifunefune mwapemphero kukhazikika koyenera pa malembo, ndi kukhumba kuti dzina la Yesu lithe kukhala loyamba pakati pathu. Mawu a Mulungu omwe tatengapo omwe talingalirapo mu mutu uwu, asonyeza njira iyi yokhala ndi mbali ziwiri. Ngakhale kuti pali mayesero, zosamvetsetseka, ndi masawutso, komatu mkhristu amapatsidwa mphamvu kuti akondwere, podziwa kuti zinthu izi zidakhazikitsidwa ndi Atate wake wa Kumwamba mwa chikondi kuti zigwire ntchito pakulanga ndi kulangiza. Mkati mwa mayesero mkhristu amatsogozedwa mwa chikhulupiriro kuti ayang’ane kwa Yesu.

Chitsimikizo mwa Yesu.

Chitsimikizo chowona cha chipulumutso ndi chomwe chimatsimikizidwa ndi chiphunzitso, zokumana nazo komanso pakuchita. Iwo ophunzitsidwa ndi Mzimu Woyera adzadziwa zina zake za “chikhulupiriro chokwanira” (Ahebri 10:22), “chiyembekezo chokwanira”, (Ahebri 6:11) ndi “chidzalo cha chidziwitso,”. (Akolose 2:2). Pamakhala kutsimikiza pomwe Mzimu Woyera atsegula Baibulo pa kuyankha pemphero, ndi kutipatsa chizindikiritso cha chiphunzitso cha mtengo wapatali cha chipulumutso. Chimodzimodzinso, timadziwa za chitsimikizo cha mtengo wapatali pomwe tapatsidwa chikhulupiriro kuti tikhulupirire ndi kuti timve chikondi cha Khristu chikutsanulidwa, ndipo m’miyoyo yathu, machimo athu atachotsedwa, ndipo mtendere womwe umaposa chidziwitso chonse timawupeza. Pamenepo, ngakhale mu yesero lozamitsitsa, Ambuye amasangalatsidwa kuti atipatse ife mphatso ija ya chiyembekezo chopanda kanthu chomwe oakhulupirira amakhala nacho, koma ndi chiyembekezo chimene, “tiri nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m’katikati mwa chophimba; m’mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga

60

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

mwa dongosolo la Melikizedeki.” (Ahebri 6:19-20).

Chitsimikizo china ndi chomwe chichitira umboni ku chikhulupiriro ndicho kuyendabe osasiya, mu malamulo a Mulungu. Tiyeni tiganizire kuti popanda ichi sitingathe kukhala ndi chitsimikizo chowona cha chipulumutso mwa Yesu. Mtumwi Yohane analemba kuti, “Ndipo umo tindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe chowonadi; koma iye amene akusunga Mawu ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M’menemo tizindikira kuti tiri mwa Iye.” (1 Yohane 2:3-5).

Tiyeni tsopano titembenukire ku kulingalira za nkhani ya ophedwa chifukwa cha Uthenga Wabwino, womwe adapereka moyo wawo chifukwa cha umboni wa Yesu. Ambiri, makamaka pa nthawi yomwe Martin Luther amabweretsa Uthenga weniweni, adasawutsika mu imfa zopweteka. Adapereka umboni wa chitsimikizo chawo mwa Khristu mwa kulolera kwawo modekha, kulimbika mtima komanso ngakhale chimwemwe pa kusawutsidwa kwawo chifukwa cha Yesu, podziwa kuti anali ndi korona wa chilungamo oyikidwira iwo Kumwamba (2 Timoteyo 4:8). Chipembedzo chopepuka, chachidzikodziko, chopanda uzimu chikadakhoza kusungunuka mwachangu mu malawi a moto a chizunzo. Chimodzimodzinso, utumiki womwe unangolankhula za chitsimikizo mwa Khristu Yesu ukadakhoza kukhala chitonthozo chochepa kwa iwo akuzinzidwa kuti afe, ogulitsidwa monga akapolo, otenthedwa amoyo atamangidwa ku mitengo.

Pa nthawi yomwe Martin Luther amabweretsa chiphunzitso chowona, chidziwitso cha chitsimikizo cha chipulumutso mwa Yesu ndi chomwe chinali chizindikiritso chimodzi chachikulu pakati pa mipingo yotsutsa chiphunzitso cha chiRoma. Zotsatira zake, mpingo wa ku Roma unalankhula motsutsa mipingo ina mu msonkhano wawo wa “Reformation Council of Trent” polemba temberero ili. “Ngati munthu wina aliyense amayesedwadi kukhala wopanda mlandu ku machimo ndi kulungamitsidwa, natsimikiza ndi khulupirira mwa Iye mwini kuti wakukhululukidwa nalungamitsidwa, kapena kuti palibe wina aliyense yemwe angalungamitsidwedi, koma iye yekhayo yemwe akhulupirira kuti iye walungamitsidwa; iyeyo akhale wotembereredwa.” (Secrets of Romanism”, J. Zacchello, ISBN 0-87213-981-6). Posunga otsatira awo mu chikayiko chopitirira, Mpingo wa chiRoma udawasunga mu ukapolo wa ndondomeko ya mpingo wawo. Tilole iwo omwe avomereza Khristu athawe ku cholakwika cha uSatana chotere, ndi kusatsatira mwadala zalakwika za chiRoma.

61

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

Kumbukirani Njirayo.

Ichi chitibwerertsa ife ku chilimbikitso chomwe Ambuye amapereka, pomwe akhristu apatsidwa kuthekera kwakutha kuyang’ana m’mbuyo ndi kuwona njira yomwe Ambuye Mulungu wawo wawafikitsamo. Mkati mwa mayesero njirayi imakhala yothetsa nzeru, koma pomwe tiyang’ana m’mbuyo za dzanja la chisomo cha Ambuye ndi pomwe limavumbulutsidwa. Mwina mwake chinali chisawutso kapena chokhumudwitsa chachikulu, koma mu zaka zotsatira amazindikira kuti zinali zabwino ku moyo wawo wa uzimu; zinawasunga iwo ku msampha wa dziko womwe umatsogolera anthu kuchoka kwa Mulungu. Monga mtumwi Paulo analemba; “Ndipo tidziwa kuti akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene ayitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” (Aroma 8:28). Chimodzimodzinso, pangathe kukhala chilangizo chachikulu, chilimbikitso ndi chiyanjano chauzimu ndi okhulupirira ena, pomwe tiwerenga kuti anadutsa mu mayesero ofanana ndi ife, ndipo anapambana mwa Yesu.

Zimapindulitsanso kulingalira za zipwirikiti za uzimu zazikulu kuyambira mu nthawi za Chipangano Chatsopano, momwe abambo ndi amayi anapereka miyoyo yawo chifukwa cha umboni wa Yesu. Pali maphunziro ambiri mu mbiri ya mpingo, makamaka mokhudzana ndi Uthenga wa Martin Luther, womwe umapereka chitsanzo pa nthawi yoyenera, chilimbikitso ndi chenjezo kwa ife lero. Adani a Uthenga Wabwino amakondwerera kuti mamembala a mipingo ndi misonkhano amadziwa pang’ono mwinanso osadziwa chilichonse za zinthu izi. Iwo omwe ali m’mipingo, omwe sasamalira mbiri ndi cholowa chathu mu chitsutso cha chiphunzitso cha chiRoma, amachita izi mwa kudziyika mu ngozi yayikulu.

Kuyang’ana m’mbuyo uku kwa pa njirayi kumatsamira pa dongosolo la malemba. Baibulo limapereka zitsanzo zambiri pamene ana a Israeli analamulidwa kuti akumbukire njira yomwe Ambuye Mulungu wawo anawatsogolera kuti ayendemo. Mose analankhula kwa Israeli asanalowe mu dziko lolonjezedwa. “Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka izi makumi anayi, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa cokhala mu mtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iyayi.” (Deuteronomo 8:2). Chimodzimodzinso, Paulo analemba kwa akhristu a mpingo wa ku Korinto; “Koma izi zinachitika mwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife. Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:11-12).

Kotero kuti, Baibulo limakhazikitsa dongosolo la mbiri ya machitachita a Ambuye

62

Chitsimikizo Mkati Mwa Mayesero

chifukwa cha; chilangizo chathu, chenjezo ndi chilimbikitso. Titatha kuwerengera za chikhulupiriro cha anthu okhulupirra osiyanasiyana a Chipangano Chakale mkati wa mayesero, Mtumwi Paulo analemba: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo wawukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chiri chonse, ndi chimoli limangitizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiyikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu ameneyo chifukwa cha chimwemwe choyikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:1-2). Tiyeni potero tipatsidwe kuthekera kwakupereka ulemerero kwa Yesu, tikukondwera mu chipulumutso chake cha ulemerero.

Ulemu wosafa umagonera pa mutu wa Yesu. Mulungu wanga, Cholowa change, ndi mkate wanga wamoyo Mwa ine ndikhala ndi moyo, pa Iye nditaya nkhawa zanga Andipulumutsa ku imfa, chiwonongeko ndi kakasi. Ndiye pothawira panga mu zovuta zanga zozama. Ambuye mphamvu yanga ndi chilungamo cha ulemerero. Kudutsa madzi osefuka ndi malawi anditeteza nanditsogoza. Tsiku ndi tsiku andiwonetsera mphamvu ya uMulungu wake. Chosowa changa chili chonse akwaniritsa mkulemera. Kapena chifundo chake sichidzalola kuti ndife. Mwa Iye mukhala chuma chonse cha uMulungu Ndi chisomo choposa wapanga chumacho kukhala changa. Inde kuti moyo wanga ukadamulemekeza Iye kosatha, Kukongola kwake kupeza, ndipo ulemu wake kulambira; Khala pafupi ndi mtima wake, pa chifuwa chake tsamira; Mvera Mawu ake, ndi chifuniro chake chonse chilemekeze. (Gadsby)

62

MUTU 6. MATHERO ABWINO OCHOKERA KUMWAMBA.

Mtima wanu Usavutike.

Momwe kumwambako kumakonzera mapeto abwino a zovuta za pansi pano ndi phunziro lomwe liri lulomikizana ndi chitsimikizo mwa Khristu Yesu, lomwe tangolingalirapo mutu wapitawu. Mayang’anidwe odalitsika awa ali chilimbikitso kwa mkhristu kutu apilire mkati mwa mayesero. Mathero abwino ochokera Kumwambawa ayenera kuchitika a uzimu mwa chikhulupiriro a mathero a ulemerero a ulendo amapereka mphamvu zatsopano zoyenda kudutsa zovuta ndi kukumana ngakhale ndi imfa imene.

Pomwe tikhala nawo mayang’anidwe a Kumwamba m’maso mwathu, Mtumwi Paulo adazindikira kuti, “Imfayo yamezedwa m’chigonjetso. Imfawe, mbola yako iri kuti? Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo; koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuruka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akoritno 15:54-58).

Ngakhale zinthu ziri chomwecho anthu a Ambuye kawiri kawiri amasawutsika ndi zinthu zambiri, ndipo amatayidwa pansi ndi zikaiko ndi mantha. Za mtengo wapatali izi, pomwe Mzimu Woyera alankhula Mawu a Ambuye Yesu mu mtima, “mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuwuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha, kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:1-3).

Ambuye Yesu analankhula mokoma mtima Mawu awa kwa ophunzira ake asanakhomedwe pa mtanda. Ayuda adaganiza kuti Messiah adzakhala mfumu ina yake ya dziko la pansi komanso Muwomboli wa Israeli. Ngakhale ophunzira sadathe kumvetsetsa za zochitika, mpaka pomwe Mzimu Woyera anawavumbulutsira iwo. Sadazindikire kwathunthu pa nthawi iyi kuti ufumu wa Ambuye si uli wa dziko lino, koma kuti uli ufumu Kumwamba. (Yohane 18:36).

Kotero kuti, tiyeni tichenjezedwe ndi mwa Mawu a mtumwi Paulo; “Ngati

63

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tiri ife awumphawi oposa a anthu onse.” (1 Akorinto 15:19). Cholakwika chachikulu ndicho kukhala ndi ziyembekezo ndi zokhumba zomangiririka mu zinthu za moyo uno. Ambuye athe kutithandiza kutiwombola ife kuchokera ku nsinga za chimo zomwe zimatimangirira ife ku dziko, zokhumba ndi zokopa zake. Mphamvu ya Mulungu wam’mwamba yokha ndi yomwe ingachite izi. Davide analemba; “Anthu anu adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Masalmo 110:3). Tiyeni ndi mtima wowona tifunefune chisomo ndi mphamvu ya uzimu kuti tiyende mu chilimbikitso cha Ambuye; “weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.” (Luka 21:28). Tiyeni nthawi zonse tikumbukire kuti chiyemmbekezo cha mkhristu chiyenera kukhazikika pa madalitso a muyaya ndi a Kumwamba mwa Khristu Yesu. (Aefeso 1:3).

Yerusalemu Wa Kumwamba.

Anali mtumwi Yohane, yemwe adatengedwa ukapolo nayikidwa pa chisumbu cha Patmo chifukwa cha umboni wa Yesu, yemwe adapatsidwa masomphenya a Kumwamba. Izi zinalembedwa kuti tilangizidwe kuti tilangizidwe ndi kutonthozedwa. “Ndipo ndinawona mzinda woyerayo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva Mawu akuru ochokera ku mpando wachifumu ndi kunena Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuyichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:1-3). Yohane keneka anawonetsedwa mwa ulemerero a mzinda wa Kumwambawo; koma panali chinthu china chachikulu chomwe chidavumbulutsidwira iye. “Ndipo sindinawona Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake. Ndipo pa mzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuwuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uwunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:22-23).

Yohane kenaka anawonetsedwa kuti okhawo omwe analembedwa mu bukhu la moyo la Mwanawankhosa amalowa kumeneko; china chili chonse chodetsedwa ndi chimo sichingalowe. (Chivumbulutso 21:27). Okhawo omwe ali anthu a Ambuye adzasangalala ndi “mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, oturuka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 22:1). Kuwonjeza apo owomboledwa a Ambuye adzatumikira Iye, ndipo adzamuwona Iye.

64

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

Timawerenganso kuti, “suikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuwunika kwa nyali, ndi kuwunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawawunikira; ndipo adzachita ufumu ku nthawi za nthawi.” (Chivumbulutso 22:5). Chokhumba chachikulu cha owomboledwa cha Kumwamba si ndicho wina ndi mzake, kapena dziko lomwe alisiya m’mbuyo, koma ndi Ambuye Mulungu wamphamvu yonse ndi Mwanawankhosa, Ambuye Yesu wowuka kwa akufa.

Izi ndi zosiyaniranatu ndi zokhulupirira za dziko la pansi zokhudza Kumwamba! Sitidzatengeredwanso ku kufotokozera za kukondweretsa thupi kapena za m’malingaliro omwe amawonera anthu zinthu (ngakhale iwo omwe adzitcha kuti ali atumiki a uthenga wabwino) anazilengeza. Malingaliro awa kwambiri ali pa mfundo yakutenga popita ku ulemerero zonse zokondweretsa za dziko la pansi zomwe ochimwa amakondwera nazo kwambiri. Ngakhale zitayengedwa mwa njira ina iliyonse komanso kulandirika pa maso pa munthu, zomwe tizitsatira za pa dziko, Mawu a Mulungu ananena momveka bwino kuti, “chinthu chiri chonse chosaturuka m’chikhulupiriro, ndicho uchimo.” (Aroma 14:23). Kunja kwa Yesu kulibe mathero abwino ochokera Kumwamba, komatu chilango chamuyaya chokha ku Gahena. (Mateyu 25:31-46).

Anthu a Ambuye adzadziwa pang’ono za kukoma kwa madalitso a Kumwamba pansi pano. Padzakhala nthawi zomwe Ambuye amakhala pafupi, ndipo amadabwitsidwa ndi chikondi cha Mulungu, momwe muli chiyanjano chapadera ndi chopatulika ndi Yesu. Ichi chikhoza kuchitika kwa ka nthawi kochepa kokha, koma kulowa pang’ono kwa zomwe iwo akozedwera mu ulemerero. Mwa chisoni, mkhristu savula minthu wakale wa chimo mu moyo uno wa pansi pano, ndipo sachedwa kugwa mukusakidwa ndi malingaliro ndi ntchito za uchimo zomwe. Ngakhale zili chomwechi, zolowa za ulemerero izi zidzawapangitsa iwo kukhumba mowona mtima ndi kupemphera kuti akhale oyera, kuti amasulidwe ku chimo, ndi kuti akhale ndi khristu chomwe chili choposa zonse. Ngakhale zonse ziri chomwecho, iwo adzagonjera ku chifuniro ndi chikhumbo kudikira nthawi yake yokhazikidwiratu, kukhumba kutumikira Ambuye ku ulemerero ndi ulemu. (Afilipi 1:21-26).

Pokhala nawo mathero abwino ochokera Kumwambawa pa ife, Mtumwi Paulo analemba; “Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tiri nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha m’Mwamba. Pakutinso m’menemo tibuwula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba; ngatitu povekedwa sitipezedwa amaliseche. Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuwula, pothodwa; si kunena tifuna

65

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo. Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.” (2 Akorinto 5:1-5).

Uku ndi kukonderedwa kwa mtengo wapatali, komwe kuyenera kufunidwa mwa pemphero, kuti kuwonekera mwa chikhulupiriro kwa mathero abwino ochokera Kumwamba omwe adaperekedwa kwa wolemba ndakatulo uyu.

Inde, Posachedwa ndidzatera Pa tsidya ilo la chisangalalo. Uko, ndi mphamvu zanga ndikula Ndikakhala komwe Yesu ali. Inde, Posachedwa ndidzakhala pansi, Pamodzi ndi Yesu pa mpando wake. Adani anga onse agonjetsedwa. Ndi mtendere wopatulika udziwidwa. Pamodzi ndi Atate, Mwana ndi Mzimu, Ndidzalamulira nthawi zonse. Chimwemwe chokoma ndi mtendere ndilandira. Chabwino chiri chonse ndilandira. Posachedwa ndifika pa gombe, Komwe ndithamangira Ndidzapuma ku ntchito zanga zonse. Kumeneko ndidzakhala nthawi zonse. Mzimu wokoma, nditsogolereni Pa nyanja ya mayesero a moyo; Ndisungeni, Inu wokonda Woyera Chifukwa ndidalira pa inu. O! kuti mu kufufuma kwa Yordan Ndithe kuthandizidwa kuyimba, Ndi kudutsa mtsinje, kunena Zipambano za Mfumu yanga.

(Gospel Magazine, 1804)

66

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

Khalani Wosaledzera ndi Watcheru.

Kuyembekezera kwa zotsatira zabwino kochokera Kumwamba si komwe kdasungidwira mkhristu kuti kudzachitike masiku otsiriza a dziko la pansi. Ngakhale akhristu ambiri anakumanapo ndi dalitso lapadera pomwe amatsala pang’ono kulowa ku ulemerero, mawonekedwe mwa chikhulupriro, a kumwamba ndiwosowekera pa njira yonse ya mkhristu. Sitimadziwa zomwe tsiku lingatibweretsere, kapena tsiku lomwe Ambuye adzabwere (Yakobo 4:13-15). Ngakhale ziri chomwecho, ndi chitonthozo chapadera kwa iwo omwe akuyandikira kumapeto kwa ulendo wa dziko la pansi kumva kufowoka kwakulu, ululu ndi mayesero.

Mawu a Mulungu amalankhula za zotsatira mu moyo wa mkhristu za chiyembekezo cha zotsatira zabwino a Kumwamba. Mtumwi Yohane analemba motere za mphamvu yake yakuyengetsera. “Tawonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ichi dziko la pansi silizindikira Iye. Okondedwa, tsopano tiri ana a Mulungu, ndipo sichinawoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuwoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye. Pakuti tidzamuwona Iye monga ali. Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.” (1 Yohane 3:1-3).

Mtumwi Paulo analembanso za zotsatira zotipangitsa tcheru za chidziwitso chakuti Ambuye adzabwera tsiku lina. “Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale sikufunika kuti tidzakulemberani. Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse. Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwerani monga mbala; pakuti inu nonse muli ana a kuwunika, ndi ana a usana; sitiri a usiku, kapena a mdima; chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:1-6).

Tisowa chilimbikitso chakuti tikhale tcheru ndi wosaledzera! Momwemonso, timawerenga za chilimbikitso cha Yesu kwa ophunzira mu nthawi ya yesero; “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa.”(Mateyu 26:41). Kusaledzera kwa uzimu ndi chisomo cha mtengo wapatali pomwe mkhristu ali nacho. Chimagonera mwabwino pa Ambuye Yesu Khristu, yemwe anavumbulutsidwa ngati Mawu osandulika thupi ndiponso Mawu olembedwa. Kusaledzera kwa kunja popanda kudziwa za Yesu kuli kopanda phindu ndiponso chonyansa pamaso pa Mulungu.

67

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

Chimodzimodzinso, tiyenera kuchenjezedwa kuti tisatengeke ndi malingaliro wopanda maziko womwe sakhazikika pa maziko a Mawu a Mulungu. Izi zimanyoza kusowa kwa kusaledzera kwa uzimu, pomwe ayesa kutsutsa m’malo mwa chitsimikizo chodala mwa Yesu. Ambiri analakwitsa (ngakhale atumiki a Mulungu) mu malingaliro okamba za pomwe masiku otsiriza adzafikire, kapena za momwe dziko lingadzathere. Tiyeni m’malo mwake tisamalire Mawu a Ambuye Yesu; “Koma za tsiku ilo ndi nthawi yake sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36).

Umulungu Wathunthu mwa Yesu.

Tiyenera tsopano tifikitse bukhuli ku mapeto. Komabe, wolemba akuwona kuti pali zina zambiri zomwe zikadakhoza kulembedwa zokhudza Yesu. Zinali chomwecho ndi Mtumwi Yohane kumapeto kwa Uthenga Wabwino wake, “Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko la pansi silikadakhala nawo malo a mabukhu amene akadalembedwa.” (Yohane 21:25). Pali uMulungu wodzaza mwa Yesu womwe mtima wa munthu ndi moyo zikhoza kulawa pansi pano; koma kumwamba Ambuye Yesu adzadziwika mu ulemerero wake wonse ndi wokhulupirira wowona ali yense. “Pakuti tsopano tipenya m’kalilore, ngati chimbuwuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.” (1 Akorinto 13:12).

Ngakhale ziri chomwecho, mtumwi Yohane adakhoza kunena; “Koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nawo moyo m’dzina lake.” (Yohane 20:31). Pokhala nawo mtolo umenewu ndicho chifukwa chake wolemba wagwira ntchito ya kulemba, kupemphera kuti Ambuye athe kukondweretsedwa ndi kupereka madalitso a muyaya kwa wowerenga. Ngakhale kuti bukhu ili langokhudza pa chowonadi cha Uthenga Wabwino, pali uthunthu ndi kuya mu Baibulo kwa zomwe ngakhale miyoyo yathu yonse singathe kuzifukula zonse. Yesu yemwe ndi Mawu a muyaya alipo mu Mawu onse olembedwa. Tiyeni tisanthule malemba mwa chikhulupiriro, kupemphera kuti Mzimu Woyera athe kuvumbulutsa kwa ife Ambuye Yesu Khristu mukukongola ndi uMulungu wake wonse. Tiyeni tipatsidwe chikhumbo cha kukonda kutembenuza miyoyo ya anthu ochimwa, kupemphera kuti Ambuye athe kokundweretsedwa kuti atigwiritse ntchtio monga zipangizo zosawuka mu chipulumutso cha ena, kuti dzina la Ambuye lipatsidwe ulemu ndi kulemekezedwa. Mose munthu wa Mulungu anachisonyeza ichi motere. “Chochita inu chiwoneke kwa atumiki anu ndi ulemerero wanu pa ana awo. Ndipo chisomo chake cha Yehova Mulungu wathu chikhale pa ife;

68

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba

ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu; inde, ntchito ya manja athu muyikhazikitse.” (Masalmo 90:16-17).

Timalize ndi mawu otsiriza a mtumiki wa ku Scotland yemwe ndi Samuel Rutherford, yemwe anagwira ntchito mu mudzi wa Anworth. Zimawonetsa chikhumbo cha mtumiki wowona ali yense wa Uthenga Wabwino. Momwemonso, anthu ake a Ambuye amatsogozedwa ndi Mzimu Woyera mwa munthu mwini kuti awone Mpulumutsi mwa chikhulupiriro. Pomwe chikondi cha Mulungu chadziwidwa mwa mphamvu, amakhumba mowona mtima kuti ena athenso kukhala ndi chiyembekezo cha mathero okoma chodalitsika chochokera Kumwamba.

Mchenga wa nthawi ukupita pansi, M’mawa wa Kumwamba ufika, M’mawa wokoma udzuka Mdima, mdima wakhala pakati pa usiku. Koma mbandakucha wafika Ndi ulemerero – ulemerero ukhalapo M’dziko la Emmanueli. Mfumuyo kumeneko mu kukongola kwake. Popanda chophimba, awonekera, Unali ulendo woyenda bwino, Ngakhale imfa zisanu ndi ziwiri zinali pakati pa ulendo. Mwana wa nkhosa ndi gulu lake lake la nkhondo. Pa phiri la Ziyoni liima; Ndi ulemerero – ulemerero ukhalapo, Mdziko la Emmanueli. O! Khristu iye ndiye kasupe, Chitsime chozama cha chikondi! Mitsinje pa dziko ndayilawa, Ozama ndikamwa m’mwamba Uko, ku kudzala kwa Nyanja ya mchere. Chifundo chake chikula. Ndi ulemerero – ulemerero ukhalapo, Mdziko la Emmanueli.

69

Mathero Abwino Ochokera Kumwamba Anworth m’mbali mwa Solway. Kwa ine inu ndinu wokondedwa. Ngakhale kuchokera Kumwamba Ndigwetsera inu msozi Oh! Ngati moyo umodzi wa ku Anworth, Mukawone nane ku dzanja la manja la Mulungu, Kumwamba kwanga kudzakhala Kumwamba kuwiri. M’dziko la Emmanueli! Maso a mkwatibwi osati chovala, Koma nkhope mkwati wake wokondedwa; Sindidzayang’ana pa ulemerero, Koma pa Mfumu yanga ya Chisomo. Osati pa korona Iye apereka Mphatso; Koma pa dzanja Lake lolasidwa: Mwana wa Nkhosa ndiye ulemerero wonse. Wa dziko la Emmanueli.

(Rutherford).

70

YESU, NDIYE NJIRA.

Bukhu ili likukhazikitsa njira ya chipulumutso mwa Ambuye Yesu Khristu mwakuti likhoza kuwerengeka mosavuta ndi momveka bwino; koma lakhazikika pa Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu.

Tsiku la lero, mbali yayikulu ndi yomwe pali kulowa pansi kwa chidziwitso cha Mulungu. Izi sizikuwoneka mu mipingo ndi mu dziko mokha, koma zimamvekanso mu mitima ya okhulupirira ambiri. Mphamvu ya Mzimu Woyera siyikumvekanso monga mu mibadwo ya m’mbuyomo. Pali kumveka kwambiri kwa Mawu, koma pali kuchita kochepa kwa Mawu a Mulunguwo. Mipingo yambiri yovomereza Khristu imakana poyera za chowonadi cha Baibulo. Enanso amagwiritsitsa ku kalata yakunja ya chowonadi, koma kukoma kwa Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu kumamveka mochepa kapena mwa apa ndi apo.

Chitsimikizo cha Wolemba ndi chakuti kuchiza kwa izi kugonera mwa Yesu. Bukhu ili kotero kuti likufunafuna kuti liyese chowonadi cha maziko chomwe ambiri ataya, ndi kuti liwonetsere kufunika ndi dalitso la kuyenda mu njira ya Yesu. Ndi cholinga cha Wolemba chomwe wapempherera kuti Yesu athe kukwezedwa ndi kuti onse wowerenga adalitsidwe mu miyoyo yawo ndi Mzimu Woyera.

Dr. Ian Sadler (BSc, PhD, DLit) ndi membala wa mpingo wa Strict Baptist Church. Anaphunzitsidwa monga wa kafukufuku wa za Sayansi, koma pano akugwira ntchito mu magawo a za umoyo ndi chitetezo cha umoyo wa thanzi. Ali pa banja lomwe liri laling’ono. Analembanso mabukhu ena omwe ndi Chinsinsicho, Babulo wamkulu, ndi Chikondi cha Mulungu.