na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

Upload: emerald

Post on 07-Jul-2018

375 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    1/32

    NA IMWE MUNGAKHALE

    MNZAKE WA  MULUNGU!

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    2/32

     Mulungu Akupemphani Kuti Mukhale Mnzake 1

     Mulungu Ndiye Angakhale Mnzanu Wabwino Kwambili 2

     Mufunikila Kuphunzila za Mulungu 3 Nanga Mungaphunzile Bwanji za Mulungu? 4

     Anzake a Mulungu Adzakhala mu Paladaiso 5

     Paladaiso Ili Pafupi! 6

     Kutengapo Phunzilo pa Zimene Zinacitika Kumbuyo 7

     Kodi Adani a Mulungu ni Andani? 8

     Kodi Anzake a Mulungu ni Andani? 9

     Mmene Mungadzi  ˆ wile Cipembedzo Coona 10

     Kanani Cipembedzo Conama! 11

     Kodi Munthu Akafa Cimacitika kwa Iye ni Ciyani? 12

     Matsenga na Ufiti ni Vinthu Voipa 13

     Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa 14

     Anzake a Mulungu Amacita Vinthu Vabwino 15

     Onetsani Cikondi Canu kwa Mulungu 16

     Kuti Musunge Ubwenzi, Mufunikila Kukhala Munthu Waubwenzi 17

     Khalani Mnzake wa Mulungu Kwamuyaya! 18

    NKHANI ZA MKATI PHUNZILO

    ˘   2009Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania 

     Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!

    Ofalitsa:Printed by Watch Tower Bible and Tract Society of South Africa NPC

    1 Robert Broom Drive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739, R.S.A.

    Kabuku kano kanapulintiwa mu June 2014Colinga ca kabuku kano ni kuthandiza panchito yophunzitsa Baibo

    imene icitika padziko lonse. Zopeleka zodzifunila ni zimenezimathandiza kuti nchito imeneyi ipite patsogolo.

    Mu kabuku kano talembamo Cinyanja camasiku ano cimeneanthu ambili amamvela mosavuta. Baibo imene tase

     ˆ wenzetsa ni

     Revised Nyanja (Union) Version, kusiyapo ngati taonetsa ina. Mukaona  NW ,ndiye kuti mau amenewo acokela mu Baibo ya   New World 

    Translation of the Holy Scriptures.   Koma tasintha sipeling’ikuti igwilizane na Cinyanja cimene talemba.

    You Can Be God’s Friend!Cinyanja ( gf  -CIN)

    Made in the Republic of South Africa Kabuku kano anakapangila ku Republic of South Africa 

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    3/32

    Mulungu afuna kuti imwe mukhale mnzake. Kodi munaganizapo kutiimwe mungakhale mnzake wa Mulungu? Abulahamu, amene anakhala-ko kale kwambili, anali mnzake wa Mulungu. (Yakobo 2:23) Baibo ima-kamba za anthu ena amene anali anzake a Mulungu, ndipo Mulungu ana-wadalitsa kwambili. Masiku ano, padziko lonse lapansi, pali anthu ameneakhala anzake a Mulungu. Na imwe mungakhale mnzake wa Mulungu.

    Mulungu angakhale mnzanu woposa mnzanu ali- yense. Mulungu salephela kucita zimene amalonje-za kwa anzake okhulupilika. (Salmo 18:25) Kukhala 

    mnzake wa Mulungu nikwabwino kuposa kukhala na cuma. Munthu wolemela akafa, anthu ena amate-nga cuma cake. Koma cuma cimene anzake a Mu-lungu ali naco, palibe munthu amene angacitenge.—Mateyu 6:19.

    Anthu ena angayese kukuletsani kuphunzila za Mulungu.  Ngakhale anzanu kapena acibanja anga-fune kukuletsani. (Mateyu 10:36, 37) Ngati ena aku-

    sekani kapena kukuopsani, mudzifunse kuti, ‘Kodiine nifuna kukondweletsa ndani—anthu kapena Mu-lungu?’ Ganizilani izi: Ngati munthu wina akuuzanikuti muleke kudya, kodi mungaleke? Iyai. Mukale-ka kudya mungafe. Koma Mulungu angakupatse-ni moyo wosatha! Conco, musavomele kuti aliyenseakuletseni kuphunzila za kukhala mnzake wa Mulu-ngu.—Yohane 17:3.

      P H U N Z I L O 1  

    MULUNGU AKUPEMPHANI  K UTI  MUKHALE  MNZAKE

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    4/32

    Kukhala mnzake wa Mulungu ni ci-nthu cabwino kuposa ciliconse cime-ne mungakhale naco. Iye angakuphunzi-tseni mmene mungapezele cimwemwe na cisungiko. Ndiponso adzakumasulani kuziphunzitso zonama na ku vocitacita voi-pa. Iye adzayamba kumvela mapempheloanu. Adzakuthandizani kukhala na mte-ndele wa m’maganizo na cidalilo mwa iye. (Salmo 71:5; 73:28) Panthawi ya ma-

     vuto Mulungu adzakuthandizani. (Salmo18:18) Ndiponso Mulungu akulonjezanimphatso ya moyo wosatha.—Aroma 6:23.

    Mukakhala mnzake wa Mulungu, ma-bwenzi ake nawo adzakhala anzanu.Ndipo iwo adzakhala monga abale na alongo anu. Adzakondwela kukuphu-

    nzitsani za Mulungu ndipo adzakuli-mbikitsani.

    Mulungu sitilingana naye.   Pamenemufuna kukhala mnzake wa Mulungu,pali mfundo ina imene muyenela kuidzi-wa bwino. Mfundo imeneyo ni yakuti;mukakhala mnzake wa Mulungu sindi-ye kuti mwalingana naye iyai. Iye wa-

    khalapo kwa zaka zambili, ali na nze-lu na mphamvu zambili kuposa ife. Iyendiye woyenela kutilamulila. Conco nga-ti tifuna kukhala mnzake wa Mulungu,tifunikila kumumvela na kucita zimeneamatiuza. Tikacita zimenezo, zinthu zi-dzatiyendela bwino.—Yesaya 48:18.

      P H U N Z I L O 2  

    MULUNGU NDIYE  ANGAKHALE MNZANU W ABWINO  K  WAMBILI

    4

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    5/32

    Kuti mukhale mnzake wa Mulungu, mufuni-kila kuphunzila za iye. Kodi anzanu dzina lanualidzi  ˆ wa, ndipo amalitomola? Inde. Naye Mu-lungu amafuna kuti dzina lake mulidzi   ˆ we, ndikuti muzilitomola. Dzina lake ni Yehova. (Sa-lmo 83:18; Mateyu 6:9) Ndiponso mufunikila kudzi  ˆ wa zimene amafuna na zimene samafu-na. Mufunikanso kudzi   ˆ wa anzake na adani ake.Koma kudzi  ˆ wa munthu kumatenga nthawi. Ba-ibo imakamba kuti ni cinthu canzelu kupatu-la nthawi ya kuphunzila za Yehova.—Aefeso 5:15, 16.

    Anzake a Mulungu amacita zimene zimamu-kondweletsa.   Mwacitsanzo, tiyeni tikambe za anzanu. Ngati muma 

      ˆ wavuta na kucita zinthu zi-

    mene samafuna, kodi angapitilize kukhala anza-nu? Kutalitali! Ni cimodzimodzi na Mulungu.

    Ngati imwe mufuna kukhala mnzake, mufuniki-la kucita zimene iye amafuna.—Yohane 4:24.

    Kodi zipembedzo zonse zingakuthandi-zeni kukhala mnzake wa Mulungu? Iyai. Yesu, amene ni mnzake wa Mulungu wapa-mtima, anaphunzitsa ponena za njila zi

      ˆ wili.

    Ina niikulu ndipo ili ndi anthu ambili oye-

    ndamo. Njila imeneyo imapeleka ku ciono-ngeko. Koma njila ina niing’ono ndipo anthuoyendamo ni ocepa. Njila imeneyi imapeleka ku moyo wosatha. Conco, ngati mufuna ku-khala mnzake wa Mulungu, mufunikila ku-phunzila mmene mungamulambilile mu nji-la yoyenela.—Mateyu 7:13, 14.

      P H U N Z I L O 3  

    MUFUNIKILA K UPHUNZILA ZA MULUNGU

    5

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    6/32

    Mungaphunzile za Mulungu mwa ku   ˆ wele-nga Baibo.   Kale kwambili, Mulungu anasa-nkha anthu ena kuti alembe maganizo ake.Zimene analemba zimapanga buku lochedwa kuti Baibo. Masiku ano timaphunzila za Mu-lungu mwa ku  ˆ welenga Baibo. Baibo imache-dwanso kuti Mau a Mulungu cifukwa mulimau a Yehova, kapena kuti uthenga wake. Ti-ngakhulupilile zimene Baibo imakamba cifu-kwa Yehova sanganame. “Mulungu sakhoza 

    kunama.” (Ahebri 6:18) Mau a Mulungu ndiyecoonadi.—Yohane 17:17.

    Mulungu anatipatsa mphatso zamtengowapatali. Koma Baibo imaposa zonse.  Bai-bo ili monga kalata imene tate walembela ana ake okondedwa. Imatiuza kuti Mulungu ana-lonjeza kuti adzasintha dziko lapansi kukhala paladaiso, malo abwino okhalamo. Imatiuza-nso zimene Mulungu anacitila ana ake okhu-lupilika kumbuyo, zimene amawacitila masikuano, ndiponso zimene adzawacitila mtsogolo.Imatithandizanso mmene tingacitile na ma-

     vuto athu na mmene tingapezele cimwemwe.—2 Timoteo 3:16, 17.

      P H U N Z I L O 4  

    NANGA MUNGAPHUNZILE B WANJI ZA  MULUNGU?

    6

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    7/32

    A Mboni za Yehova ni anzake a Mulungu.Iwo adzakuthandizani kuimvetsetsa Baibo.Ngati mufuna kuphunzila Baibo, auzeni adza-kuthandizani. Samalipilitsa ndalama. (Mateyu10:8) Ndiponso, mungaziyenda kumisonkha-

    no yawo. Amacitila misonkhano imeneyi kumalo oitanidwa kuti Nyumba ya Ufumu. Mu-kayamba kuyendako ku misonkhano imeneyi,mudzaphunzila zambili ponena za Mulungu,panthawi ing’ono cabe.

    Mungaphunzilenso za Mulungu ku zinthu

    zimene anapanga.   Mwacitsanzo, Baibo ima-kamba kuti: “Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Pamene Yeho-

     va analenga “kumwamba,” anapanganso dzu- ˆ wa. Nanga zimenezi zimatiphunzitsa ciyaniponena za Mulungu? Zimatiphunzitsa kuti Ye-hova ali na mphamvu zambili. Ni yekha cabeangakwanitse kupanga cinthu camphamvu

    monga dzu

      ˆ 

    wa. Zimatiphunzitsanso kuti Yeho- va ali na nzelu. Takamba conco cifukwa sembeanalibe nzelu, sakanakwanitsa kupanga dzu

      ˆ wa 

    limene limatulutsa kutentha na kuwala, koma silikutha kapena kuzima.

    Zimene Mulungu analenga zimaonetsa kutiamatikonda.  Ganizilani zipatso zosiyanasiya-na zimene zili padziko lapansi. Yehova akana-funa, sembe anatipatsa mtundu umodzi cabewa zipatso, kapena osatipatsa cipatso ciliconse.Koma, anatipatsa zipatso zambili zosiyanasiya-na mu maonekedwe, ukulu, na kukoma kwake.Zimenezi zimaonetsa kuti Yehova ni Mulunguwacikondi, wopatsa, woganizila ena komansowabwino mtima.—Salmo 104:24.

    7

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    8/32

    Paladaiso idzakhala malo osiyana na dziko li-mene tikhalamo panthawi ino. Mulungu sana-fune ngakhale pang’ono kuti padziko lapansi pa-khale mavuto alionse na zinthu zocititsa cisoni.Mtsogolo, Mulungu adzasintha dziko lapansi ku-khala Paladaiso. Kodi Paladaiso idzakhala maloabwanji? Tiyeni tione zimene Baibo ikamba:

    Anthu abwino. Mu Paladaiso mudzakhala cabeanzake a Mulungu. Adzayamba kucitilana zinthuzabwino wina na mnzake. Pamoyo wawo adzatsa-tila njila za Mulungu zolungama.—Miyambo 2:21.

    Zakudya za mwana alilenji. Mu Paladaiso simu-dzakhala njala. Baibo imakamba kuti: ‘M’dziko-mo mudzakhala zinthu [kapena, zakudya] zocu-luka.’—Salmo 72:16.

    Manyumba abwino na nchito zokondweletsa.Mu Paladaiso padziko lapansi, banja lililonse li-

    dzakhala na nyumba yawoyawo. Munthu aliyenseadzacita nchito imene idzamukondweletsa.—Yesa-ya 65:21-23.

      P H U N Z I L O 5  

    ANZAKE A MULUNGU ADZAKHALA MU PALADAISO

    8

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    9/32

    Kudzakhala mtendele padziko lonse. Nkhondona kuphana kudzakhala kulibe. Mau a Mulunguamakamba kuti: ‘[Mulungu] aletsa nkhondo kumalekezelo a dziko lapansi.’—Salmo 46:8, 9.

    Umoyo wabwino. Baibo imalonjeza kuti: “Ndipowokhalamo [mu Paladaiso] sadzanena, Ine ndi-dwala.” (Yesaya 33:24) Ndiponso, sipadzakhala munthu wolemala kapena wosaona kapena wosa-mva kapena wosakamba.—Yesaya 35:5, 6.

    Zo  ˆ wa   ˆ wa, cisoni na imfa zidzacoka. Mau a Mu-lungu amakamba kuti: ‘Ndipo sipadzakhalansoimfa; ndipo sipadzakhalanso malilo, kapena kuli-

    la, kapena co  ˆ wa 

      ˆ witsa; zoyambazo zapita.’—Cibvu-mbulutso 21:4.

    Anthu oipa sadzakhalamo.  Yehova analonjeza kuti: “Oipa . . . adzalikhidwa [kucotsedwa] m’dzi-ko, aciwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.

    Anthu adzakondana na kulemekezana.  Siku-dzakhala kucitilana zosalungama, kuponde-

    lezana, dyela, na kuzondana. Anthu adzakhala ogwilizana, ndipo adzatsatila njila za Mulunguzolungama.—Yesaya 26:9.

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    10/32

    Voipa vamene vicitika padziko lapansi vionetsa kuti Paladaiso ili

    pafupi. Baibo inakambilatu kuti pamene Paladaiso ili pafupi kubwe-la, padzakhala nthawi yovuta kwambili. Nthawi imeneyo ndiye ino!Onani vinthu vina vamene Baibo inakambilatu kuti vidzacitika:

    Nkhondo Zikuluzikulu. “Mtundu umodziwa anthu udzaukilana ndi mtundu wina, ndiufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Ulo-si umenewu wakwanilitsika. Kuyambila mucaka ca 1914, kwacitika nkhondo zi

      ˆ wili za 

    padziko lonse na nkhondo zina zing’ono-zing’ono zambili. Ndipo anthu mamiliyoniambili afa m’nkhondo zimenezi.

    Kuwanda kwa matenda. Padzakhala “mili-li [matenda owanda] m’malo akuti akuti.’’(Luka 21:11) Kodi zimenezi zacitika? Inde.Matenda a kansa, matenda a mtima, cifuwa 

    ca TB, maleliya, AIDS, na matenda ena ama-pha anthu mamiliyoni ambili.

    Njala.   Padziko lonse lapansi pali anthuambili amene alibe cakudya cokwanila. Caka ciliconse anthu mamiliyoni amafa na njala.Cimeneci ni cina codzi

      ˆ wila kuti Paladaiso ili

    pafupi. Baibo imakamba kuti: “Padzakhala 

    njala.”—Marko 13:8.

      P H U N Z I L O 6  

    PALADAISO ILI  PAFUPI!

    10

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    11/32

    Zivomezi.   ‘Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akuti akuti.’ (Mateyu24:7) Nazo izi zacitika m’nthawi yathu. Kuyambila mu 1914, zivomezizapha anthu opitilila miliyoni imodzi.

    Anthu oipa.   Anthu adzakhala “okonda ndalama” ndi “odzikonda okha.” Adzakhala “okonda zokondweletsa munthu, osati okonda Mu-lungu.” Ana adzakhala “osamvela akuwaba-la.” (2 Timoteo 3:1-5) Kodi simuvomeleza kuti masiku ano pali anthu ambili amene aliconco? Iwo alibe ulemu kwa Mulungu, ndipoamavutitsa aja amene amafuna kuphunzila za Mulungu.

    Kucita zaupandu.  Kudzakhalanso ‘kuculu-

    ka kwa kusaweluzika.’ (Mateyu 24:12) Nga-khale imwe mungavomeleze kuti masiku anozaupandu zimacitika kwambili kusiyana na kale. Anthu kulikonse amaopa ku

      ˆ wabela, ku-

     ˆ wanama kapena ku

      ˆ wapweteka.

    Zonse izi zionetsa kuti Ufumu wa Mulu-ngu uli pafupi.  Baibo imakamba kuti: “Pa-

    kuona zinthu izi zilikucitika, zindikilanikuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Kodi Ufumu wa Mulungu ni ciya-ni? Ni boma yakumwamba imene idzabwe-letsa Paladaiso padziko lino lapansi. Ufumuwa Mulungu ukabwela udzacotsapo mabo-ma onse a anthu.—Danieli 2:44.

    11

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    12/32

     Yehova sadzalola kuti anthu oipa akakha-

    lemo mu Paladaiso cifukwa angaiwononge. Anzake cabe a Mulungu ni amene adzakhalamo.Nanga anthu oipa cidzawacitikila ni ciyani? Kutimudzi  ˆ we, mvelani vimene vinacitika mu ntha   ˆ wiya Nowa. Papita zaka masauzande pamene iyeanakhalapo. Anali munthu wabwino wolimbi-kila kucita zimene Yehova anali kufuna. Koma anthu ena padziko lapansi anali kucita vinthu

     voipa. Conco, Yehova anauza Nowa kuti adza-

    bweletsa cigumula ca madzi kuti aononge anthuonse oipa. Kuti Nowa na banja lake asafe pacigu-mula cimeneco, Yehova anamuuza kupanga ci-ngalawa copulumukilamo.—Genesis 6:9-18.

    Nowa na Banja lake anapanga cingalawa. Ci-gumula cikalibe kubwela, Nowa anacenjeza anthu, koma iwo sanamumvele. Iwo anapitili-za kucita vinthu voipa. Pamene Nowa anatsili-za kupanga cingalawa, analo  ˆ wetsamo vinyama.Ndiyeno, iye na banja lake anangena mu cingala-wa. Pambuyo pake, Yehova anabweletsa cimvu-la cikulu. Cimvula cimeneco cinagwa kwa masi-ku 40 usana na usiku. Ndipo madzi amenewoanaculuka na kudzala padziko lonse lapansi.—Genesis 7:7-12.

      P H U N Z I L O 7  

    K UTENGAPO PHUNZILO PAZIMENE ZINACITIKA  K UMBUYO

    12

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    13/32

    Anthu oipa aja onse anafa, koma Nowa na banja lake anapulumuka.   Pambuyo pakuti

     Yehova awapulumutsa ku cigumula, anawabwe-zela padziko lapansi limene anayeletsa mwa ku-cotsapo anthu oipa. (Genesis 7:22, 23) Baiboimakamba kuti mtsogolo Yehova adzaononga-nso anthu amene safuna kucita zinthu zabwi-no. Koma anthu abwino sadzawaononga. Iwoadzakhala na moyo wosatha mu Paladaiso pa-dziko lapansi.—2 Petro 2:5, 6, 9.

    Masiku ano anthu ambili amacita vinthu

     voipa.   Mu dziko muli mavuto ambili. Yehova watumiza Mboni zake mobwelezabweleza kutizicenjeze anthu, koma anthu ambili safuna ku-mvela mau ake. Iwo safuna kuleka makhalidweawo oipa. Safuna kuti Mulungu aziwauza zime-ne zili zabwino na zoipa. Kodi ni ciyani cidzaci-tikila anthu amene ali conco? Kodi tsiku lina adzasintha makhalidwe awo? Ambili sadzaleka.

    Ndiye cifukwa cake nthawi ibwela pamene Mu-lungu adzaononga anthu onse oipa, cakuti sa-dzakhalaponso.—Salmo 92:7.

    Dziko lapansi silidzaonongedwa; koma adzalipanga paladaiso. Anthu amene ni anza-ke a Mulungu adzakhala na moyo wosatha muPaladaiso padziko lapansi.—Salmo 37:29.

    13

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    14/32

    Satana Mdyelekezi ndiye mdani mkuluwa Mulungu.   Iye ni mngelo amene ana-pandukila Yehova. Ndipo Satana amene-yo apitiliza kutsutsa Mulungu na kucititsa mavuto akulu kwa anthu. Satana ni woipa.Ni wabodza ndipo amapha anthu.—Yohane8:44.

    Angelo ena anagwilizana na Satana ku-pandukila Mulungu. Angelo amenewo Ba-

    ibo imawaitana kuti vi  ˆ wanda. Monga mme-ne Satana alili, vi   ˆ wanda navo ni adani a 

    anthu. Vimakonda kuvutitsa anthu. (Mate-yu 9:32, 33; 12:22) Koma Yehova adzaono-ngelatu Satana na vi   ˆ wanda vake. Iwo atsa-la na nthawi ing’ono cabe yovutitsa anthu.—Cibvumbulutso 12:12.

    Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulu-ngu, osacita zimene Satana amafuna kutimucite. Satana na vi   ˆ wanda vake amazonda-na na Yehova. Iwo ni adani a Mulungu, ndi-po amafuna kuti na imwe mukhale mda-ni wa Mulungu. Conco, muyenela kusankha amene mufuna kukondweletsa—Satana ka-pena Yehova. Ngati mufuna moyo wosatha,muyenela kucita zimene Mulungu amafu-

    na. Satana ali na njila zambili zonamila-mo anthu. Iye amapusitsa anthu ambi-li.—Cibvumbulutso 12:9.

      P H U N Z I L O 8  

    K ODI  ADANI A  MULUNGU NI  ANDANI?

    14

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    15/32

     Yesu Khristu ni Mwana wa Mulungu,ndipo ni mnzake wapamtima.   Poya-mba, Yesu anali kumwamba mongamngelo wamphamvu. (Yohane 17:5) Ndi-yeno, anabwela kudzakhala munthu pa-dziko lapansi, kudzaphunzitsa coonadiponena za Mulungu. (Yohane 18:37) Pa-mbuyo pake, anataya moyo wake waumu-nthu kuti apulumutse anthu omvela Mu-lungu ku ucimo na imfa. (Aroma 6:23)

    Panthawi ino, Yesu ni Mfumu ya Ufumuwa Mulungu. Ufumu umenewo ni boma imene idzabweletsa Paladaiso padziko la-pansi pano.—Cibvumbulutso 19:16.

    Angelo nawo ni anzake a Mulungu. Angelo sa-nayambile moyo wawo padziko lapansi. Mulu-ngu anawalengela kumwamba akalibe kupanga 

    dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo aliko ma-miliyoni ambili. (Danieli 7:10) Anzake a Mulu-ngu akumwamba amenewa amafuna kuti anthuaphunzile coonadi conena za Yehova.—Cibvu-mbulutso 14:6, 7.

    Mulungu ali na anzake ena padziko lapansi;iye amawaitana kuti mboni zake.   Mboni, nimunthu amene mu khoti amanena zimene adzi- ˆ wa ponena za munthu kapena cinthu cina. AMboni za Yehova amauza anthu zimene adzi

      ˆ wa 

    ponena za Yehova na cifunilo cake. (Yesaya 43:10)Mofanana na angelo, a Mboni amafuna kuku-thandizani kuti muphunzile coonadi conena za 

     Yehova. Afuna kuti na imwe mukhale mnzake wa Mulungu.

      P H U N Z I L O 9  

    K ODI  ANZAKE A  MULUNGU NI  ANDANI?

    15

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    16/32

    Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulu-ngu, mufunika kulambila mu cipembe-dzo cimene iye amavomeleza.   Yesu ana-kamba kuti “olambila oona” adzalambila Mulungu mogwilizana na “coonadi.” (Yoha-ne 4:23, 24) Pali njila imodzi cabe yoyene-la kulambilila Mulungu. (Aefeso 4:4-6) Cipe-mbedzo coona cimapeleka ku moyo wosatha,koma cipembedzo conama cimapeleka kuimfa.—Mateyu 7:13, 14.

    Cipembedzo coona mungacidzi   ˆ we mwa kuona zocita za anthu ake.  Cifukwa Yeho-

     va ni wabwino, nawo amene amamulambi-la m’njila yoyenela, ayenela kukhala anthuabwino. Monga mmene mtengo wabwino wa maolenji umabalila maolenji abwino, nacocipembedzo coona cimakhala na anthu abwi-no.—Mateyu 7:15-20.

    Anzake a Yehova amalemekeza Baibokwambili.   Amadzi  ˆ wa kuti Baibo inacokela kwa Mulungu. Amalola mau a m’Baibo ku-watsogolela m’moyo wawo. Mau a Mulunguamawathandiza kudzi  ˆ wa mocitila na mavu-to awo, ndipo amawathandiza kuphunzila za Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Ndipo iwo ama-

    cita zimene amalalikila.

      P H U N Z I L O 1 0  

    MMENE MUNGADZI ˆ 

     WILE CIPEMBEDZO COONA

    16

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    17/32

    Anzake a Yehova amakondana wina na mnzake. Yesu anaonetsa cikondi kwa anthumwa kuwaphunzitsa za Mulungu, na kuci-litsa odwala. Komanso, amene ali mu cipe-mbezo coona amakondana wina na mnza-

    ke. Mofanana na Yesu, iwo samaona anthuosauka kapena a mtundu wina kukhala apa-nsi. Yesu anakamba kuti anthu adza   ˆ wadzi  ˆ wa ophunzila ake cifukwa ca kukondana kwawo.—Yohane 13:35.

    Anzake a Mulungu amalemekeza dzina la Mulungu, lakuti Yehova.   Ngati munthuwina akana kuse  ˆ wenzetsa dzina lanu, kodi

    angakhale mnzanu wazoona? Kutalitali!Ngati tili na mnzathu timamutomola dzi-na lake, ndipo timakamba zabwino za iyekwa ena. Conco anthu amene afuna kukha-la anzake a Mulungu afunika kuse  ˆ wenzetsa dzina lake na kuuzako ena za iye. Ni zimene

     Yehova afuna kuti tizicita.—Mateyu 6:9; Aro-ma 10:13, 14.

    Mofanana na Yesu, Anzake a Mulunguamaphunzitsa ena za Ufumu wa Mulu-ngu.   Ufumu wa Mulungu ni boma yaku-mwamba imene idzabweletsa paladaiso pa-dziko lapansi. Anzake a Mulungu amauzakoanthu ena za uthenga wabwino wa Ufumuwa Mulungu.—Mateyu 24:14.

    A Mboni za Yehova amalimbikila kukhala anzake a Mulungu. Amalemekeza Baibo na kukondana wina na mnzake. Amase

      ˆ wenzetsa 

    dzina la Mulungu na kulilemekeza, komansoamaphunzitsa ena za Ufumu wake. A Mboniza Yehova padziko lonse lapansi amalambila mu cipembedzo coona.

    17

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    18/32

    Satana na vi   ˆ wanda vake safuna kuti imwe mu-zitumikila Mulungu.   Iwo amafuna kuti aco-tse munthu aliyense ku mbali ya Mulungu ngatiangakwanitse. Kodi amayesa kucita zimenezi ku-pitila mu njila za bwanji? Imodzi mwa njila zime-nezo ni cipembedzo conama. (2 Akorinto 11:13-15) Cipembedzo ciliconse cimene cimaphunzitsa zimene sizicokela mu Baibo ni conama. Cipembe-dzo conama cili monga ndalama yabodza—nga-khale kuti ingaoneke monga ni yazoona, imakha-

    la ilibe nchito. Ingakubweletseleni mavuto akulu.

    Mabodza a cipembedzo sangakondweletse Ye-hova, Mulungu wa coonadi.  Pamene Yesu ana-li padziko lapansi, panali anthu ena acipembe-dzo amene anafuna kumupha. Anali kuona kuti

    cipembedzo cawo ndiye cinali coona. Iwo anaka-mba kuti: “Tili naye tate mmodzi ndiye Mulu-ngu.” Kodi Yesu anavomeleza zimenezo? Kutali-tali! Koma iye anawauza kuti: “Inu muli ocokela mwa atate wanu Mdyelekezi.” (Yohane 8:41, 44)

     Anthu ambili masiku ano amaganiza kuti amala-mbila Mulungu, koma kwenikweni amatumikila Satana na vi

      ˆ wanda vake!—1 Akorinto 10:20.

      P H U N Z I L O 1 1  

    K ANANI CIPEMBEDZO  CONAMA!

    18

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    19/32

    Monga mmene mtengo umene uli na matenda umabalila zipatso zoipa, cipembedzo conama cimakhala na anthuocita voipa. Padziko lapansi pali mavuto ambili cifukwa ca 

     vinthu voipa vimene anthu amacita. Pali uhule, kumenya-na, kuba, kupondelezana, kuphana, na kugona akazi mo-kakamiza. Ambili amene amacita vinthu ivi ali na cipe-mbezo cawo, koma cipembedzo cawo siciwalimbikitsa kucita zinthu zabwino. Kuti akhale anzake a Mulu-ngu afunikila kuleka kucita voipa.—Mateyu 7:17, 18.

    Cipembedzo conama cimaphunzitsa anthu kupe-mphela ku mafano.  Mulungu amaletsa kupemphe-la ku mafano. Ndipo zimenezi ni zomveka. Mwaci-tsanzo, kodi mungamve bwanji ngati munthu wina,m’malo mokamba na imwe, amakamba cabe na cithu-nzithunzi kapena cipikica canu? Kodi mungakambekuti munthu ameneyo ni mnzanu wazoona? Iyai. Co-nco, Yehova amafuna kuti anthu azikamba naye, osatikukamba na cifanizilo copanga kapena cipikica cime-ne cilibe moyo.—Eksodo 20:4, 5.

    Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti si kula-kwa kupha anthu pankhondo. Yesu anakamba kutianzake a Mulungu adzakhala okondana pakati pawo.Ife sitingaphe anthu amene timakonda. (Yohane13:35) Ngakhale kupha anthu oipa ni kulakwa. Pame-ne adani a Yesu anabwela kuti amumange, iye sanalo-le kuti ophunzila ake amenyane nawo kuti amucinjili-ze.—Mateyu 26:51, 52.

    Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti anthuoipa adzapsa m’mulilo ku helo.  Koma Baibo ima-

    phunzitsa kuti ucimo umapeleka ku imfa. (Aroma 6:23) Yehova ni Mulungu wacikondi. Nanga Mulu-ngu wacikondi angaoche anthu m’moto kwamuyaya?Iyai, sangacite zimenezo. Mu Paladaiso mudzakhala cipembedzo cimodzi cabe, cimene Yehova amavomele-za. (Cibvumbulutso 15:4) Mulungu adzaononga vipe-mbedzo vonse vimene vimaphunzitsa mabodza a Sa-tana.

    19

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    20/32

    Munthu akafa ndiye kuti alibe moyo.  Imfa ili monga tulo tukulu, kapena kuti tulo tofa nato. (Yohane 11:11-14) Anthu akufa sangamve, sangaone, sanga-kambe, kapena kuganiza ciliconse. (Mlaliki 9:5, 10) Cipembedzo conama cima-phunzitsa kuti anthu akafa amayenda ku dziko la mizimu kukakhala pamodzi

    na mizimu ya makolo awo. Koma Baibo siiphu-nzitsa zimenezi.

    Anthu amene anafa sangatithandize pa ci-liconse, ndipo sangatiukile ci   ˆ wanda.   Anthuambili amakonda kucita miyambo na kupele-ka nsembe zimene amakhulupilila kuti zimako-

    ndweletsa anthu amene anafa. Zimenezi Mulu-ngu sakondwela nazo cifukwa ni mabodza a Satana Mdyelekezi. Sizingakondweletse ngakhaleakufa cifukwa alibe moyo. Sitiyenela kuopa kape-na kulambila anthu amene anafa. Tifunikila ku-lambila Mulungu yekha cabe.—Mateyu 4:10.

    Anthu amene anafa adzauka.  Yehova adzauki-tsa anthu amene anafa kuti akakhale na moyo mu

    paladaiso padziko lapansi. Zimenezi zidzaciti-ka mtsogolo. (Yohane 5:28, 29; Macitidwe 24:15)Kwa Mulungu, ni cosavuta kuukitsa anthu aku-fa, monga mmene cilili cosavuta kwa imwe kuu-tsa munthu amene ali mu tulo.—Marko 5:22, 23,41, 42.

    Maganizo akuti anthu ife sitimafelatu ni ma-bodza amene Satana Mdyelekezi amafalitsa.

    Satana na vi

      ˆ 

    wanda vake amapangitsa anthu ku-ganiza kuti mizimu ya anthu amene anafa ili na moyo. Amakamba kuti mizimu imeneyo ni ime-ne imadwalitsa anthu na kubweletsa mavuto ena.Nthawi zina Satana amanama anthu kupitila m’maloto na masomphenya oona vinthu. Yehova amawazonda anthu amene amayesa kukamba na anthu amene anafa.—Deuteronomo 18:10-12.

      P H U N Z I L O 1 2  

    K ODI  MUNTHU AKAFA CIMACITIKA KWA   I YE NI  CIYANI?

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    21/32

    Satana amafuna kuti muzicita vamatsenga. Anthu ambili amapeleka nsembe ku mizimuya akufa kuti iziwachinjiliza. Amacita zimene-zi cifukwa amaopa mphamvu za mizimu yoi-pa. Amavala mphete (maling’i) zamatsenga ka-pena mabango (makhoza). Amamwa kapena kudzola mankhwala amene amaganiza kuti alina mphamvu zowachinjiliza. Ena amabisa ma-nkhwala mu nyumba kapena kukumbila pa-nsi kuti achinjilize nyumba yawo, kapena kuti

    kuitsilikila. Palinso ena amene amase   ˆ wenzetsa mankhwala cifukwa amakhulupilila kuti adza-wapatsa mwayi pa bizinesi, pamayeso, kapena ofunila mkazi kapena mwamuna.

    Njila yabwino kwambili yodzichinjiliza 

    kwa Satana ni kukhala mnzake wa Yehova. Yehova na angelo ake ni amphamvu kwambilikuposa Satana na vi

      ˆ wanda vake. (Yakobo 2:19;

    Cibvumbulutso 12:9) Yehova ni wokonzeke-la kuse

      ˆ wenzetsa mphamvu zake kuti achinjili-

    ze anthu amene ni anzake. Amene  ˆ wa ni anthu

    amene ali okhulupilika kwa iye na mtima wo-nse.—2 Mbiri 16:9.

    Mau a Mulungu amakamba kuti: “Musa-macita nyanga kapena kuombeza.”  Yehova amazonda zamatsenga, ufiti, kapena kuombe-za. Zimenezi amazizonda cifukwa munthuamene amacita zinthu zimenezi amayamba kulamulilidwa na Satana Mdyelekezi.—Leviti-ko 19:26.

      P H U N Z I L O 1 3  

    MATSENGA NA UFITI NI V INTHU V OIPA

    21

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    22/32

    Satana amanyengelela anthu kuti azicita  vinthu voipa.  Munthu amene amafuna ku-khala mnzake wa Mulungu, naye afunika ku-zonda vimene Mulungu amazonda. (Salmo97:10) Onani vinthu vina voipa vimene anza-ke a Mulungu amakana kucita:

    Macimo a zogonana.  “Usacite ci-gololo.” (Eksodo 20:14) Nako ku-gonana mukalibe kukwatilana ni

    kulakwa.—1 Akorinto 6:18.

    Kuledzela kapena ‘kukolewa.’“Oledzela, . . . sadzalo  ˆ wa Ufumuwa Mulungu.”—1 Akorinto 6:10.

    Kupha munthu, Kucotsa mimba.“Usaphe.”—Eksodo 20:13.

    Kuba. “Usabe.”—Eksodo 20:15.

    Kunama.   Yehova amazonda mu-nthu wa “lilime lonama.”—Miya-mbo 6:17.

      P H U N Z I L O 1 4  

    ANZAKE A  MULUNGU AMAKANA  K UCITA  V OIPA

    22

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    23/32

    Ciwawa na kukalipa kopitilila.   ‘Yehova . . .amuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.’ (Sa-lmo 11:5) ‘Nchito za thupi, . . . [ziphatikizapo]kupsa mtima.’—Agalatiya 5:19, 20.

    Njuga. “Muleke kuyanjana ndi aliyense . . . wa-umbombo.”—1 Akorinto 5:11,  NW.

    Kuzondana cifukwa cosiyana khungu(nkhanda) kapena kusiyana mitundu.   ‘Ko-ndanani nao adani anu, ndi kupemphelela iwoakuzunza inu.’—Mateyu 5:43, 44.

    Zimene Mulungu amatiuza zimatipinduli-tsa. Nthawi zina cimavuta kukana voipa. Koma  Yehova na Mboni zake angakuthandizeni ku-kana kucita voipa vimene Mulungu samafuna.—Yesaya 48:17; Afilipi 4:13; Ahebri 10:24, 25.

    23

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    24/32

    Ngati muli na mnzanu amene mumakonda na kumulemekeza, mumayesa kukhala mo-nga iye. Baibo imakamba kuti: “Yehova ndiyewabwino ndi wolunjika mtima.” (Salmo 25:8)Kuti tikhale mnzake wa Mulungu, tifuniki-la kukhala anthu abwino ndi a mtima wo-lungama. Baibo imakambanso kuti: “Khalaniakutsanza a Mulungu; monga ana okondedwa ndipo yendani m’cikondi.” (Aefeso 5:1, 2) Ona-ni mmene mungacitile zimenezi:

    Muzithandiza ena.   “Ticitile onse cokoma.”—Agalatiya 6:10.

    Khalani wolimbikila panchito.  “Wakubayoasabenso; koma makamaka agwilitse nchito,nagwile nchito yokoma ndi manja ake.”—Aefe-so 4:28.

    Khalani munthu waukhondo ndi wama-khalidwe abwino. ‘Tizikonzele tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi ku-tsiliza ciyelo m’kuopa Mulungu.’—2 Akorinto7:1.

      P H U N Z I L O 1 5  

    ANZAKE A  MULUNGU AMACITA V INTHU  V ABWINO

    24

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    25/32

    Muzikondana na kupatsana ulemuna onse a m’banja mwanu.   “Yenseakonde mkazi wake wa iye yekha, mo-nga adzikonda yekha; . . . ndipo mkazi-yo akumbukile kuti aziopa mwamuna.

     Ananu, mvelani akukubalani.”—Aefeso5:33–6:1.

    Kondani anthu ena.   “Tikondane

    wina ndi mnzake: cifukwa kuti ciko-ndi cicokela kwa Mulungu.”—1 Yoha-ne 4:7.

    Muzimvela malamulo a dziko.‘Anthu onse amvele maulamulilo aa-kulu [boma]; . . . Pelekani kwa anthuonse mangawa awo; msonkho kwa eniake a msonkho.’—Aroma 13:1, 7.

    25

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    26/32

    Kuti ubwenzi wanu na munthu wina upiti-lize, mufunikila kumakambitsana.  Muma-mumvela, nayenso amakumvelani. Ndiponso,mumauzako anthu ena zinthu zabwino pone-na za iye. Ni cimodzimodzi na kukhala mnza-ke wa Mulungu. Onani zimene Baibo imaka-mba pankhani imeneyi:

    Muzikamba na Yehova m’pemphelo ntha-wi zonse.   “Limbikani cilimbikile m’kupe-

    mphela.”—Aroma 12:12.Muzi   ˆ welenga Mau a Mulungu, Baibo.  “Le-mba lililonse adaliuzila Mulungu, ndipo lipi-ndulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzelo,cilangizo ca m’cilungamo.”—2 Timoteo 3:16.

    Muziphunzitsa ena za Mulungu.  “Cifukwa cake mukani, phunzitsani anthu a mitunduyonse, . . . asunge zinthu zonse zimene ndina-kulamulilani inu.”—Mateyu 28:19, 20.

      P H U N Z I L O 1 6  

    ONETSANI CIKONDI CANU KWA  MULUNGU

    26

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    27/32

    Khalani mnzawo wa aja amene ni anza-ke a Mulungu. “Ukayenda ndi anzelu udza-khala wanzelu.”—Miyambo 13:20.

    Muzipezeka kumisonkhano ku Nyumba  ya Ufumu.   ‘Tiyeni tiganizilane wina ndimnzake, kuti tilimbikitsane pa cikondi ndinchito zabwino.’—Ahebri 10:24,  NW.

    Muzithandiza panchito ya Ufumu na zo-peleka zanu. ‘Yense acite monga atsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza,pakuti Mulungu akonda opeleka moko-ndwelela.’—2 Akorinto 9:7.

    N Y UMB A  Y  A  UFUMU ya Mboni za Y eho va

    27

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    28/32

    Kuti ubwenzi upitilize payenela kukhala ci-

    kondi.  Mukaphunzila zambili ponena za Ye-hova, cikondi canu kwa iye cidzakula kwambi-li. Ndipo cikondi canu pa iye cikakula, cifunocanu comutumikila naco cidzakula. Zimenezi zi-dzakuthandizani kukhala wophunzila wa YesuKhristu. (Mateyu 28:19) Mukalo

      ˆ wa mu gulu la 

    Mboni za Yehova, limene ni banja lacimwemwe,mudzakhala mnzake wa Mulungu kwamuyaya.Kodi mufunika kucita ciyani kuti mulo  ˆ we mubanja limeneli?

    Mufunika kuonetsa cikondi canu kwa Mulu-ngu mwa kusunga malamulo ake.  “Ici ndi ci-kondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ake;ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane5:3.

    Muzicita zimene mumaphunzila.   Yesuanasimba nthano ina imene imaonetsa zi-menezi. Munthu wocenjela anamanga nyu-mba yake pa cimwala kapena kuti thanthwe.Koma munthu wopusa anamanga nyumba yake pamcenga. Pamene cimvula camphepocinabwela, nyumba imene anamanga paci-mwala siinagwe. Koma nyumba imene ana-manga pamcenga inagwa kugwelatu. Ndi-yeno, Yesu anakamba kuti anthu amene

    amamvela, na kucita zimene amawaphu-nzitsa, ali monga munthu wocenjela uja,amene anamanga nyumba yake pacimwala.Koma awo amene amamvela cabe zimene iyeamaphunzitsa koma sazicita, ali monga mu-nthu wopusa uja, amene anamanga nyumba yake pamcenga. Kodi imwe mufuna kukha-la monga munthu uti?—Mateyu 7:24-27.

      P H U N Z I L O 1 7  

    K UTI  MUSUNGE UBWENZI, MUFUNIKILAK UKHALA MUNTHU W AUBWENZI

    28

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    29/32

    Kudzipeleka.  Kudzipeleka kumatanthauza ku-muuza Yehova m’pemphelo kuti mufuna kucita cifunilo cake kwamuyaya. Kucita cifunilo ca Mu-lungu kumaonetsa kuti ndimwe wophunzila wa 

     Yesu Khristu.—Mateyu 11:29.

    Ubatizo. ‘Ubatizidwe ndi kusamba kucotsa ma-cimo ako, nuitane pa dzina lake.’—Macitidwe22:16.

    Tumikilani Mulungu na mtima wonse.   ‘Cili-conse mukacicita, gwilani nchito mocokela mu-mtima, monga kwa Ambuye [Yehova,  NW ], osatikwa anthu ayi.’—Akolose 3:23.

    29

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    30/32

    Kuti mupeze mnzanu wapamtima mufu-nika kulimbikila, ndipo kuti ubwenziwanu ukhalitse mufunikanso kulimbi-kila.   Ngati mulimbikila kukhala mzakewa Mulungu, mudzapeza madalitso ambi-li. Yesu anauza anthu amene anakhulupili-la mwa iye kuti: “Coonadi cidzakumasulani.”(Yohane 8:32) Kodi zimenezi zitanthauza ci-yani?

    Coonadi cingakumasuleni panthawi ino.Cingakumasuleni ku viphunzitso vonama na mabodza amene Satana amafalitsa. Mu-ngakhalenso osiyana na anthu ambili ame-ne sadzi

      ˆ wa Yehova. Anthu amenewo alibe

    ciyembekezo. (Aroma 8:22) Anzake a Mulu-ngu anamasuka ngakhale ku mantha ‘akuo-pa imfa.’—Ahebri 2:14, 15.

    Mungapeze ufulu mu dziko la Mulungulatsopano.   Ha, ati kukondweletsa ufuluumene uli mtsogolo! Mu Paladaiso padzikolapansi simudzakhala nkhondo, matenda,kuphana, na vinthu vina voipa. Simudza-khalanso kusauka kapena njala. Mudzakha-la mulibe kukalamba kapena kufa. Ndiposimudzakhala mantha, kapena kupondeleza-na, ngakhale zosalungama zilizonse. Kunena 

    za Mulungu, Baibo imakamba kuti: “Muolo-wetsa [kufe

      ˆ wetsa] dzanja lanu, nimukwanili-

    tsa zamoyo zonse cokhumba cawo.”—Sa-lmo 145:16.

      P H U N Z I L O 1 8  

    K HALANI  MNZAKE WA MULUNGU K  WAMUYAYA!

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    31/32

    Anzake a Mulungu adzakhala na moyowosatha.  Moyo wosatha ni mphatso ya-mtengo wapatali imene Mulungu adzapa-tsa anthu onse amene akulimbikila ku-khala anzake. (Aroma 6:23) Ha, ganizani

    cabe zimene mungakwanitse kucita mu-kakhala na moyo wosatha!

    Mudzakhala na nthawi yokwanila ku-cita zinthu zambili.  Mwina mungafunekuphunzila kuliza cida coimbila nyimbo.Kapena mungafune kuphunzila kuja-mbula zithunzithunzi kapena kukhala kalipentala. Mungafunenso kuphunzila 

    za zinyama na zomela. Kapena munga-fune kuyenda kumalo osiyanasiyana ku-kaona malo na anthu. Mukadzakhala na moyo wosatha, mudzakwanitsa kucita zi-nthu zonse zimenezi.

    Mudzakhala na nthawi yokwanila yo-panga mabwenzi ambili.  Mukadzakha-

    la na moyo wosatha mudzadzi

      ˆ 

    wana na anthu ena ambili amene ni anzake a Mu-lungu. Mudzadzi  ˆ wa maluso awo na ma-khalidwe awo abwino, ndipo na imweadzakhala anzanu. Adzakukondani, ndi-po na imwe mudzawakonda. (1 Akorinto13:8) Mukadzakhala na moyo wosatha,mudzakala na nthawi yokwanila yopanga ubwenzi na munthu aliyense padziko la-

    pansi! Koma copambana vonse ni cakuti,ubwenzi wanu na Mulungu udzalimbila-limbila m’kupita kwa zaka. Tikufunilaniubwenzi wamuyaya na Mulungu!

    31

  • 8/19/2019 Na imwe mungakhale mnzake wa mulungu!

    32/32

    s

    Kodi mufuna kudzi   ˆ wa zambili?Dzi

      ˆ witsani Mboni za Yehova pa  www.jw.org.

    http://www.jw.org/finder?wtlocale=CIN&srcid=pdfhttp://www.jw.org/http://www.jw.org/finder?wtlocale=CIN&srcid=pdf