cha65-0801e zochitika zimamveka bwino ndi...

42
ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI Tiyeni tiweramitse mitu yathu tsopano tipemphere. Ambuye wathu Mulungu, Mlengi wamkulu wa Miyamba ndi dziko lapansi, Yemwe munamubweretsa Yesu kachiwiri kuchokera kwa akufa, ndipo ali moyo ndi ife kwa zaka zikwi ziwiri izi, wamoyo nthawizonse kuti azitsimikizira Mawu Ake ndi kuwapangitsa Iwo kukhala owona kwa m’badwo uliwonse. Ife tiri othokoza kwambiri chifukwa cha Kukhalapo Kwake Kwauzimu pakali pano, podziwa ichi, kuti ife tiri nacho chitsimikiziro chachikulu ichi, kuti moyo uno ukadzatha, ife tidzakakhala nawo Moyo Wamuyaya mu dziko limene liri nkudza. Zikomo Inu, chifukwa cha ichi, Ambuye. Ndi chiyembekezo icho, nangula kwa moyo, yemwe ali wokhazikika ndi wotsimikizika mu nthawi ya mkuntho. Ndipo pamene mikuntho idza, mafunde aakulu akutembenuzika, ife tikumverera kuti ndi chikhulupiriro mwa Iye ife tikhoza kudutsa funde lililonse. 2 Mulungu, mutithandize ife usikuuno pamene ife tikubwerera kuti tidzatumikire kwa odwala ndi osowa. Ife tikupemphera, Mulungu, kuti pasakhale munthu wodwala pakati pathu pamene ife tizichoka usikuuno. Mulole munthu aliyense achiritsidwe ndi Mphamvu Yanu Yauzimu, onse kuno ndi kudutsa fuko, kwa olumikizidwa, mulole pasakhale munthu wofooka ati atuluke mu nyumba iliyonse kapena kusonkhana kulikonse usikuuno. Mulole Mzimu Wanu uwachiritse iwo. Mulole Dzuwa lalikulu la chilungamo, liri ndi machiritso mu mapiko Ake, litulukire, litumize mafunde a chikhulupiriro mu mtima uliwonse pamene iwo akumvetsera kwa Mawu, awone mawonetseredwe a Mzimu Woyera akuwakhutitsa iwo kuti Iye akanali wamoyo. Ife tikupempherera madalitso awa, Atate, mu Dzina la Yesu. Ameni. Inu mukhoza kukhala. 3 Ife ndithudi tikuutengera uwu mwayi wawukulu kuti tiri pano usikuuno, kachiwiri, ku—kuti tiyankhule kwa anthu ndi kuwapempherera odwala. Ife tikufuna kuti tiwalonjere onse awo omwe ali kunja mu dziko la—kulumikiza kwa lamya kudutsa fukoli, kachiwiri usikuuno. Ndipo kotero ife tikupemphera kuti Mulungu adalitse aliyense wa inu, tikudalira kuti onse omwe amulandira Khristu mmawa uja adzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo azikakhala okhulupirika nthawizonse ndi owona kwa Iye mpaka moyo utatha kuno pa dziko lapansi, moyo wachivundi

Upload: lydat

Post on 26-Mar-2018

297 views

Category:

Documents


14 download

TRANSCRIPT

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA

BWINO NDI UNENERI

Tiyeni tiweramitse mitu yathu tsopano tipemphere.Ambuye wathu Mulungu, Mlengi wamkulu wa Miyamba

ndi dziko lapansi, Yemwe munamubweretsa Yesu kachiwirikuchokera kwa akufa, ndipo ali moyo ndi ife kwa zakazikwi ziwiri izi, wamoyo nthawizonse kuti azitsimikiziraMawu Ake ndi kuwapangitsa Iwo kukhala owona kwam’badwo uliwonse. Ife tiri othokoza kwambiri chifukwa chaKukhalapo Kwake Kwauzimu pakali pano, podziwa ichi,kuti ife tiri nacho chitsimikiziro chachikulu ichi, kuti moyouno ukadzatha, ife tidzakakhala nawo Moyo Wamuyaya mudziko limene liri nkudza. Zikomo Inu, chifukwa cha ichi,Ambuye. Ndi chiyembekezo icho, nangula kwa moyo, yemwe aliwokhazikika ndi wotsimikizika mu nthawi ya mkuntho. Ndipopamene mikuntho idza, mafunde aakulu akutembenuzika, ifetikumverera kuti ndi chikhulupiriromwa Iye ife tikhoza kudutsafunde lililonse.2 Mulungu, mutithandize ife usikuuno pamene ifetikubwerera kuti tidzatumikire kwa odwala ndi osowa. Ifetikupemphera, Mulungu, kuti pasakhale munthu wodwalapakati pathu pamene ife tizichoka usikuuno. Mulole munthualiyense achiritsidwe ndi Mphamvu Yanu Yauzimu, onse kunondi kudutsa fuko, kwa olumikizidwa, mulole pasakhale munthuwofooka ati atuluke mu nyumba iliyonse kapena kusonkhanakulikonse usikuuno. Mulole Mzimu Wanu uwachiritse iwo.Mulole Dzuwa lalikulu la chilungamo, liri ndi machiritso mumapiko Ake, litulukire, litumize mafunde a chikhulupiriro mumtima uliwonse pamene iwo akumvetsera kwa Mawu, awonemawonetseredwe a Mzimu Woyera akuwakhutitsa iwo kuti Iyeakanali wamoyo. Ife tikupempherera madalitso awa, Atate, muDzina la Yesu. Ameni.

Inu mukhoza kukhala.3 Ife ndithudi tikuutengera uwu mwayi wawukulu kuti tiripano usikuuno, kachiwiri, ku—kuti tiyankhule kwa anthu ndikuwapempherera odwala. Ife tikufuna kuti tiwalonjere onse awoomwe ali kunja mu dziko la—kulumikiza kwa lamya kudutsafukoli, kachiwiri usikuuno. Ndipo kotero ife tikupemphera kutiMulungu adalitse aliyense wa inu, tikudalira kuti onse omweamulandira Khristu mmawa uja adzazidwa ndi Mzimu Woyerandipo azikakhala okhulupirika nthawizonse ndi owona kwa Iyempaka moyo utatha kuno pa dziko lapansi, moyo wachivundi

2 MAWU OLANKHULIDWA

uwu. Ndiyeno iwo, pochita izo, iwo ali nawo Moyo Wamuyaya.Iwo sadzafa nkomwe mu m’badwo umene uli nkudza, kuM’badwowaukulu umene ife tonse tikuwuyembekezera.4 Tsopano ife tinena, pamene ine ndikuganiza za izi, osati kutindisokoneze. M’bale Vayle ali pano, ndipo ine mwina sindifikapomuwona iye. Ine ndidza…Kodi ine ndingakakutumizirenizolemba zija pamene ine nditi ndikafike ku Tucson? Inendikuyang’ana pa izo, sindinaziwerenge zonsezo pakali panobe,ndipo ine ndikatumiza izo kwa inu mwamsanga ine ndikakafikaku Tucson.5 Tsopano ine ndikufuna kuti ndilengeze. Izi makamakandi za kwa mipingo kulikonseko, makamaka Kumadzulo,kapena kulikonse omwe akufuna kuti abwere. M’bale wathuwolemekezeka, M’bale Pearry Green, ndi…Ndi munthuyemwe ali woyambitsa kulumikiza uku kwa lamya kuno.Ambuye akhala akuchiyika icho pa mtima wake kuti abwereadzatichezere ife ku Tucson, ndi kudzayambitsa chitsitsimutsoku Tucson, chomwe ife tikuchisowa kwenikweni. Ndipo M’balePearry adzakhala ali mu Tucson. Ngati inu mukufuna kutimumupeze iye, mudzangofika ku office yathu kumeneko. Izozidzakhala mu Ogasiti pa 10, pa 11, pa 12, ndi pa 13. Iyewakhala ali nazo izo pa mtima wake kwa nthawi yaitali, ndipoine ndinamuuza iye pali “njira yokha yozichotsera izo pa mtimawako, pita ukachite izo.” Ndipo iye ndi m’bale wa Chikhristu,wantchito weniweni wa Mulungu. Ndipo anthu inu, mu Tucson,ine ndikudziwa mudzadalitsidwa pamene iye azidzatumikirakumeneko kwinakwake, mwinamwake ku Ramada Inn kapenakulikonse komwe Ambuye ati apereke malo, iye sanawapeze iwopanobe. Koma ine ndikudziwa inumudzadalitsidwa pakubwera,kudzamumvera M’bale Green pamene iye azidzafotokoza kwaife Mawu a Mulungu, mwina kupempherera odwala, kapenachirichonse chimene chiti chidzakhale mu ntchito ya kudzodzakwa Mulungu kuti achite.6 Ife panonso tikufuna kuti timuthokoze M’bale OrmanNeville, M’bale Mann, chifukwa cha nthawi yodabwitsa iyi yachiyanjano ndi iwo. Momwe ine ndiriri woyamikira kukhalanaye, kuyanjana ndi munthu wotere monga M’bale Neville,M’bale Mann, ndi azitumiki ena onse awa azungulira pano. Inendikuganiza iwo azindikiridwa kale. Ngati inu simunatero, gululathu ndi mpingo wathu pano, ine ndikutsimikiza kuti Mulunguakukuzindikirani inu pano ngati antchito Ake. Mulole Ambuyenthawizonse azikudalitsani inu.7 Tsopano, ine ndinafunsidwa chinachake chaching’ono pano,pa kolembedwa kakang’ono kamene kanapatsidwa kwa ine,ku…Iwo anali ndi msonkhano wa matrasti usiku wina kuno,pa gulu la matrasti ndi madikoni, ndipo ine ndikuganizazolembedwa zake zinawerengedwa mmawa uno pamaso pampingo. Chomwe, ndi mwambo wake kuti ife tizichita zimenezo.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 3

Mu zolingaliridwa zomwe zinapangidwa ndi gulu la matrastindi madikoni pano pa mpingo, ndithudi, izo sizingakhozekumukondweretsa aliyense. Ife sitingakhoze kutero. Ine ndilibechinthu chimodzi chochita ndi gulu la matrasti kapena gulu lamadikoni. Ine ndilibe ngakhale voti kupatula ngati patakhalakufanana. Ndipo ine ndiyenera kuti ndikhale pano kutindizichita motero ndiye, M’bale Orman Neville amatenga votiyachiwiri imeneyo. Ndiye ife timayenera kuti ife tisayinire izi,chifukwa ndife gawo la mpingo. Koma malingaliro amene gulula matrasti ndi magulu awo amawapanga, ife ndithudi timayimakumbuyo kwa iwo zana pa zana, chifukwa ndi chomwe iwo aliripano. Ndipo zolingalira zawo ziri pakati pa iwo ndi Mulungu.Ine sindingakhoze, sindingakhoze ndipo sindikanakhoza ayi,mwa njira ina iliyonse, kutsutsana ndi lingaliro limenelo. Ndipochinthu china, ine ndimaletsedwa ndi Boma laUnited States kutindizipanga lingaliro lirilonse lokhudzana ndi zimenezo, choterochonde musati mundifunse ine kuti ndikhoze lingaliro lawo. Inesindingakhoze kuchita zimenezo, ndipo ine sindimvera kanthukokhudza izo. Mukuona? Chotero musati mundifunse ine kutindikhoze malingaliro awo. Inu muliwone gululo, ndi iwo omweanapanga malingalirowo. Chabwino.8 Tsopano mu chochitika cha msonkhano ukudzawu, ndizotheka, ngati, Ambuye alola, ine ndikhala ndikubwererakuno pafupi masabata foro mpaka sikisi, kapena chinachakechonga icho, kwa mwina msonkhano wina wa Lamlungu.Ndipo ine ndinalengeza mmawa uno kuti ine ndikufunakuyankhula paMulungu KuwonetseredwaMuMawuAke, ndipoine sindikhala nayo basi nthawi usikuuno, ndipo, moona, inendiribe nkomwe mawu okwanira kuti ndichite izo. Ndiyenounyinji, alipo pafupi ochuluka kunja monga iwo ali mkati muno,ndipo, mwina ochulukirapo, kuwerenga mabasi amenewo ndimagalimoto ndi zinthu zomwe ziri uko ndi anthu. Atsegula,kuwulutsa kwakung’ono akukweza iko pang’ono, ife tikhozakuzimva izo. Wevi yaing’ono iyi, shoti wevi kuchokera kukachisi, ife tikukhoza kuigwira iyo utali wa mdadada wamu mzinda. Ndipo ena a magalimoto ali utali wa midadadaingapo ya mu mzinda, mizere ya galimoto, chokwera ndichotsika, ndi kuzungulira ndi kudutsa misewu, kuzungulirakachisiyu usikuuno. Ine sindikukhulupirira pa nthawi iliyonse,mwakuwoneka, ife tinayamba takhala nao anthu kuposa omweife tili nawo usikuuno. Chotero ife tiri…Ndipo ochuluka,ochuluka, ochuluka akungoyendetsa ndi kumapita.9 Chotero izo zikungosonyeza, “Kumene kuli Nyama,mphungu zikasonkhanako.” Ndipo mulole ine ndinene kwa inuusikuuno, mu gulu laling’ono ili la anthu, uku ndi kusonkhanakwa maiko ambiri. Mwakuchitika kuposa magawo awiri paatatu a mafuko a mgwirizano aimiriridwa pano, pambalipa mafuko asanu akunja, ngakhale mpaka ku Russia, ndi

4 MAWU OLANKHULIDWA

konsekonse magawo osiyana a dziko. Kutali uko mpaka kuVenezuela, kupita mpaka ku Jamaica, konsekonse magawoosiyana a fuko, anthu ali pano, anjala ndi aludzu lofunaMulungu. Ndi nthawi yodabwitsa bwanji!10 Tsopano ine ndikufuna, ndisanawerenge Baibulo, ndipokodi inu mungamandipempherere ine tsopano. Ine—inendiyesera kuti ndibweretse Uthenga waung’ono, Ambuyeakalola, pa zofunikira za machiritso Auzimu. Pakuti, mmawauja ife tinayankhula pa zachipulumutso. Ndipo usikuunoife tiyankhula maminiti pang’ono pa zamachiritso Auzimu,ndiyeno tiitanira mzere wa pemphero ndi kuwapemphereraanthu. Pamene ife tikuchita izi, kunja pa zolumikiza, kulikonsekumene inu muli, ngakhale kunja mu mabasi ndi magalimotokozungulira, mkati mwa mdadada kapena iwiri kutalikirakachisiyu; pamene ifika nthawi yoti tizipempherera odwala,ngati inu simungakhoze kulowa mu nyumbayi…Chomwe,inu simungakhoze, ine ndikutsimikiza tsopano, chifukwanjira za mmakomo monse zadzadza mothinana, kupitirira,ndipo palibe malo paliponse, chotero inu muzipemphererandi kuyika manja anu pa wina ndi mzake kunja uko. Ndipomulole mtumiki aliyense yemwe walumikizidwa kuno usikuuno,nayenso azipempherera osonkhana ake pamene mautumikiamachiritso akuchitika. Ife tikukhulupirira kuti Mulungu ndiwopezeka ponseponse, kulikonse. Tsopano ife tisanawerengekapena…11 Ife tisanati—ife tisanapemphere, ife tikufuna kuti tiwerengeena a Mawu a Mulungu. Ndipo ine ndinasintha anga—Malembaanga kanthawi kapitako, chifukwa chofuna kusinthamtunduwamsonkhano umene ine ndinali nditaukonzekera mu malingaliroanga kwa usikuuno, chotero ine ndausintha iwo pang’ono pokha;ndipo chotero ine ndimayenera kuti ndisinthe Malemba anga,osati kuwasintha iwo, koma kuwaika iwo mu dongosolo lina, lamachiritsoAuzimu, chotero kuti—kuti anthu akhoze kumvetsa.

Tiyeni titembenuzire ku Luka Woyera, mutu wa 24. Ndipoife tiyambira pa ndime ya 12 ya mutu wa 24, ndipo tiwerengechotsika mpaka ku pafupi 34. Izi ziri pa chiukitsiro chaAmbuye Yesu.

Ndiye Petro, ananyamuka Petro, ndipoanathamangira ku manda; ndipo ataweramira pansi,ndipo iye anaona nsalu za bafuta…akudabwa mwayekha pa icho chimene chinali chitachitika.

Ndipo, taonani, awiri a iwo ankapita tsiku lomweloku mudzi wotchedwa Emau, umene uli kuchokera kuYerusalemu pafupi mastadiya sikisite.

Tsopano, zimatenga mastadiya teni kuti mupange—kutimupangemailo, chotero iwo anali pafupimamailosi sikisi.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 5

Ndipo pamene iwo ankakambirana limodzi za…zinthu izi zomwe zinali zitachitika.

…zinafika pochitika, kuti, pamene iwo analikukambirana limodzi ndi kusinkhasinkha, Yesumwiniwake anayandikira pafupi, ndipo ankapitalimodzi nawo.

Komamaso awo anagwidwa kuti iwo asamudziwe iye.

Ndipo iye anati kwa iwo, Nkuyankhulana kwamtunduwanji uku muli nako wina kwa mzake, pamene inumukuyenda, ndipo muli achisoni?

Ndipommodziwa iwo, amene dzina lake anali Kleopa,anayankha nanena kwa iye, Kodi ndiwe mlendo yekhamu Yerusalemu, ndipo kodi iwe sunadziwe zinthu izizinachitikazi…mu masiku awa?

Ndipo iye anati kwa iwo, Zinthu zanji?

Tsopano kumbukirani, uyu ndi Yesu Mwiniwake, atawuka,akulankhula.

Ndipo iwo anati kwa iye, Zokhudza Yesu wakuNazareti, yemwe anali mneneri wamphamvumu ntchitondi mu mawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse:

…momwe ansembe aakulu ndi olamulira athuanamuperekera iye kuti…kuti—kuti aweruzidwe kuimfa, ndipo anamupachika iye.

Koma ife tinali kudalira kuti iye akanakhala ali iyeyemwe akanati adzaombole Israeli: ndipo pambali pazonse izi, lero ndi tsiku lachitatu kuyambira pamenezinthu izi zinachitika.

Eya, ndipo akazi enanso a mu gulu lathuanatidodometsa ife, amene analawirira kumanda;

Ndipo pamene iwo sanalipeze thupi lake, iwoanabwera, nanena, kuti iwo anali atawonansomasomphenya a angelo, amene anati…iye analiwamoyo.

Ndipo ena a iwo omwe anali nafe anapita kumandako,ndipo anakazipeza izo monga momwemonso akaziadanena: koma iyeyo iwo sanamuone ayi.

Mvetserani tsopano; Yesu.

Ndiye ananena iye kwa iwo, O opusa,…ochedwamu mtima kukhulupirira zonse zomwe anenerianaziyankhula:

Kodi samayenera Khristu kuti amve zowawa izi, ndikulowa mu ulemerero wake?

6 MAWU OLANKHULIDWA

Ndipo kuyambira kwa Mose ndi aneneri onse, iyeanalongosola kwa iwo zonse, mu malemba onse zinthuzokhudza za iyemwini.

Ndipo iwo anayandikira ku mudzi, komwe iwo analikupita: ndipo iye anachita ngati kuti iye amati azipitamopitirira.

Koma iwo anamukakamiza iye, kuti, Khalani ndiife: pakuti kuli cha kumadzulo, ndipo tsiku lapitakwambiri. Ndipo iye analowa umo kuti akakhale ndiiwo.

Ndipo zinafika pochitika, pamene iye anakhalapa chakudya ndi iwo, iye anatenga mkate, ndipoanaudalitsa iwo, ndipo anaunyema iwo, ndipoanaupereka iwo kwa iwo.

Ndipo maso awo anatseguka, ndipo iwoanamuzindikira iye; ndipo iye anawasowera pamasopawo.

Ndipo iwo anati wina kwa mzake, Kodi mitima yathusiinatenthe mkati mwathu, pamene iye amayankhulanafe mnjiramo, ndi pamene iye amatsegula malembakwa ife?

Ndipo iwo ananyamuka ora lomwelo, ndipoanabwerera ku Yerusalemu, ndipo anakapeza khumindi mmodzi atasonkhana palimodzi, ndipo pamene iwoanali nawo,

Anati, Ambuye awuka ndithudi, ndipo anawonekerakwa Simoni.

Ndipo iwo anawauza zinthu zomwe zinachitika munjira, ndi momwe kuti iye anadziwikira kwa iwo pakunyema kwa mkate.

12 Tsopano tiyeni tipemphere. Wokondedwa Atate achisomo,ife tikukuthokozani Inu chifukwa cha Mawu Anu, pakutiMawu Anu ndi Choonadi, Mawu Anu ndi Moyo. NdipoInu, O Ambuye, ndi Mawu Anu muli Mmodzi. Chotero ifetikupemphera usikuuno, Ambuye, kuti Inu mubwere pakatipathu mu mphamvu ya chiukitsiro Chanu ndipo musonyezekwa ife usikuuno, monga aja omwe anabwera kuchokera kuEmau, kuti ifenso tibwerere ku manyumba kwathu, tikuti,“Kodi mitima yathu siinatenthe mkati mwathu?” Perekani izi,Ambuye, ikuyandikira nthawi yamadzulo kachiwiri. Pakuti ifetikupempha izi muDzina la YesuKhristu. Ameni.13 Tsopano ine ndikufuna kuti ndiyankhule zokhudza Baibuloili. Ndipo phunziro langa usikuuno,mwamutu, ndiwo:ZochitikaZimamveka Bwino Ndi Uneneri. Zochitika Zimamveka BwinoNdi Uneneri.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 7

14 Tsopano, Baibulo ndi Bukhu losiyana kwa mabukuopatulika ena onse. Baibulo ndi Bukhu losiyana. Ilo ndi Bukhula uneneri, limaneneratu zodzachitika mtsogolo. Ndipo Ilolirinso Vumbulutso la Yesu Khristu. Njira yonse kuchokeraku Genesis mpaka ku Chivumbulutso, limamubweretsa Iyepoyera mu chidzalo Chake, chimene Iye anali ndipo ali. NdipoBukhu lonse lamphumphu, Chivumbulutso 1:1 mpaka 3, limatiBukhuli ndi Bukhu la “Vumbulutso la Yesu Khristu,” lomweliri Mawu a Mulungu. “Vumbulutso la Yesu Khristu,” Mawu aMulungu!15 Tsopano, mabuku ena onsewa, mabuku opatulika, ali kokhandondomeko ya malingaliridwe, ndondomeko ya makhalidwe,kapena ndondomeko ya zamulungu. Chinachake chimene…Ndi angati amene anayamba awerengapo Korani, Baibulo laChimuhamadi, ndi—ndi bukhu la Chibudda, ndi ena otero?Iwo ali kokha ndondomeko ya malingaliridwe, chimene anthuayenera kumachikhala moyo, momwe iwo ayenera kumakhaliramoyo, koma iwo samanenera, samanena chirichonse cha zinthuizi kapena za mphatso zapadera zina zirizonse kukhalazikuperekedwa kwa aliyense, chirichonse choti chichitike. Basimonga kujowina mphanga kapena chinachake. Chotero, pamenemipingo yafika pa malo pamene iyo ikupanga mpingo wawokungokhala mphanga kuti uzijowina, ndiye iwo ali kutaliachokeratu ku Mawu a Mulungu.16 Pakuti Baibulo ndi umboni wamoyo, wonenedweratu waYesu Khristu. Ndipo monga dziko lapansi lakula kufika muchidzalo chake, ndiponso mipesa yakula kufika mu chidzalochake, tsiku likukula kufika mu chidzalo chake, Baibulolinawonetseredwa mwa chidzalo Chake mu Umunthu wa YesuKhristu. Iye anali Mawu a Mulungu owululidwa, Bukhulonse lamphumphu la Chiwombolo. Baibulo ndi Mawu aMulungu, akuneneratu zodzachitika mtsogolo. Okhulupiriraake amalamuliridwa ndi Mlembi Wake kuti aziwerenga ndikukhulupirira Mawu aliwonse a Ilo, osati gawo lokha la Ilo.Mawu amodzi, kusawakhulupirira Iwo, inu mukhoza kungosiyakuyeserampaka inumutawakhulupiriraMawu amenewo.Mawualiwonse ali mtheradi gawo la Mulungu Wamphamvuzonse;Mulungu atawonetseredwa, atazikurungiza mu Mawu Ake,kuti asonyezemo Yemwe Iye ali. Ife talamulidwa, mongaokhulupirira kuti tizikhulupirira Mawu aliwonse a Ilo. NdipoIlo linalembedwa ndi Mlembi wa Mulungu Mwiniwake. Palibealiyense yemwe angakhoze kuwonjezera chirichonse kwa Ilokapena kuchotsera chirichonse kwa Ilo. Ngati inu mungatero,ilo lingakhale thupi lonyengezera la Mulungu. Ilo likanakhala,mwina ngati zala sikisi pa dzanja limodzi, kapena—kapenamikono itatu, kapena chinachake, kuti awonjezere chinachake,kuti uchotsere chinachake kwa iwo likanakhala liri ndimkono umodzi palibe, chala chimodzi palibepo. Ilo ndi thupi

8 MAWU OLANKHULIDWA

lamphumphu la Yesu Khristu. Ndipo mwa Khristu, pokhalaMwamuna, Mkwati, Mkwatibwi akuyimirira mwa Iye aponso.Ndipo awiri awa aliMmodzi. “Pa tsiku limenelo inumudzadziwakuti Ine ndiri mwa Atate, Atate mwa Ine, Ine mwa inu ndi inumwa Ine.” Ndi chithunzi champhumphu bwanji!17 Ndipo okhulupirira owona mu Mawu awa, omweamawalandira Iwo mwanjira imeneyo, amawakhulupiriraIwo, ndipo ndi chipiriro amayembekezera malonjezo Akeoneneredweratu, limodzi lirilonse la iwo kuti liwonetseredwemu m’badwo wake. Wokhulupirira aliyense yemwe wakhalaakuyang’anira izo. Wokhulupirira aliyense yemwe wakhala alipa zala, akuyang’anira, ndim’modzi yemwe zaululidwirako.18 Tsopano penyani mu masiku a kudza kwa Ambuye Yesu.Nchifukwa chiyani anthu amenewo sanamuzindikire Yohane,pamene Baibulo linali litanena mwachimvekere ndi Yesaya,“Padzakhala liwu la wina wofuula mchipululu, ‘Konzani njiraya Ambuye’”? Mneneri wawo wotsiriza yemwe iwo analinaye, yemwe ali Malaki 3, anati, “Tawonani, ine ndidzatumamtumiki Wanga patsogolo pa nkhope Yanga kuti adzakonzenjira.” Nchifukwa chiyani iwo sanaziwone izo? Chifukwa iwoanali kuyang’ana pa chinachake chimene chinali chitachitidwakale, ankakhazikitsa maganizo awo pa uthenga wina umeneunali utapitapo zisanachitike izi, ndipo analephera kuti awonemawonetseredwe atsopano a Mulungu mu tsiku lomwe iwo analikukhalamo.19 Ndipo Akhristu, kulikonse, apo ndi ndendende pamenedziko likuima usikuuno. Mopanda kusiyana, icho ndi choonadi!Akhristu, kulikonse, akuyesera kuti aziyang’ana mmbuyo kundondomeko ina ya malingaliridwe yomwe Bambo Luteraanalemba, kapena BamboWesley, Sankey, Finney, Knox, Calvin;zomwe, palibe mmodzi wa ife angakhoze kuyankhula choipa paizo, koma izo zinali mu tsiku linapitalo.20 Afarisi ankayang’ana mmbuyo kuti awone zomwe Moseananena, ndipo iwo ankati, “Ife tiri naye Mose. Ife sitikudziwakomwe Iwe ukuchokera.”21 Koma kumbukirani, pamene Mose apa, iwo sankadziwakumene iye anali kuchokera. Mukuona? Ndipo tsopano iwo…Nzosadabwitsa Yesu ananena kwa iwo, “Inu mumakongoletsamanda a aneneri, ndipo inu ndi omwe mumawaika iwommenemo.” Uthenga wawo ukatha! Uthenga ukamadutsa,anthu amawuona Iwo, iwo amauseka Iwo (dziko limatero).Ndiyeno mtumiki akatsiriza ndipo Uthenga wachitidwa, ndiyeiwo amamanga chipembedzo cha Uthengawo. Ndipo pamenepoiwo amafa, pomwepo, samabwereranso nkomwe ku Moyokachiwiri.22 Tapenyani mphindi yokha, kwa anthu ena inu, ndipomakamaka ine ndikuyankhula kwa inu anthu Achikatolika.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 9

Kodi inu mukuzindikira, kodi inu munayamba mwawerengapombiriyakale yeniyeni, mbiriyakale ya mpingo wa ChiromaKatolika? Momwe kuti pa ofera anu, kuyambira pa OgastiniWoyera waku Hippo, ndi mamilioni angati a anthu osalakwaamene mpingo unawapha! Ine ndaiwala, sindingakhozekukumbukira chiwerengero chenicheni, koma icho ndi chofikamamiliyoni, kuyambira pa Hippo Woyera waku…OgastiniWoyera waku Hip-…waku Hippo, Afrika, anapanga kulengezakuti mwamtheradi chinali chifuniro chaMulungu kuti azimuphaaliyense yemwe akuwutsutsa mpingo wa Roma Katolika.Kodi inu mukuzindikira kuti mmenemo, kuti Patreki Woyerasamazindikiridwa konse mpaka pambuyo pa imfa yake, mongawa Chiroma Katolika? Iye anamutsutsa papa ndi zochita zakezonse, ndipo mpingo wa Katolika iwoweni unawapha matenia masauzande a ana ake. Kodi inu mukudziwa kuti mpingowa Katolika unamuwotcha Joan waku Arc, mkazi wamng’onowoyera uja, pa nkhuni, chifukwa cho-…ankati iye anali mfiti.Zaka thuu handiredi mtsogolo, anafukula matupi a ansembe,pamene iwo anapeza kuti analakwitsa, ndipo anawaponyera iwomu nyanja, mopanda kuwakwirira iwo mu nthaka yopatulika,kuti achite za kutunduza.

Musalole kuti tsiku likudutseni pa mutu wanu, ndi kukhalaopusa.

23 Momwe ansembe awo akanafunira, usikuuno, kuti abwere,omwe anamunyoza Yesu. Chinthu chokhacho, iwo sanakuwonekonse kuneneratu kwa ora limenelo. Ngati iwo…Yesu anati,“Fufuzani Malemba, pakuti mwa Iwo inu mukuganiza,” kapena,kani, “mukudzinenera kuti inu muli nawo Moyo Wamuyaya,ndipo Malemba ndi omwe amakuuzani inu Yemwe Ine ndiri,” aora limenelo.

24 Zindikirani, Baibulo silingathe kulephera. Icho ndi chinthuchimodzi chimene Ilo silingakhoze kuchita, Mawu a Mulungu,kulephera, pakuti Ilo limaneneratu zochita za Mlembi Wake Iyeasanachite zimenezo.

25 Tsopano, pali mwayi umodzi pa chikwi kuti munthu akhozakuneneratu kuti chinthu china chimzake chidzachitika, ndipoicho nkudzachitika. Komano ngati iye ayika kumene ichochiti chidzachitikire, izo zimamudulira iye pansi kufika mwinapa mwayi umodzi pa zikwi khumi. Ngati iye anena tsikulomwe izo ziti zidzachitike, izo zimadulira izo pansi, mwayiumodzi mu pafupi milioni. Ndi yemwe ziti zikamuchitikire, izozimabweretsa izo pansi ku pamwayi mabilioni.

26 Koma Baibulo ili limakuuzani inu ndendende ndani, liti,kuti, ndi choti muziyang’anira, ndipo silinayambe lalepherakonse nthawi imodzi. Chotero, mu kukambirana pang’onoosati kale litali, ndi wamsembe wa mpingo ku Mtima Woyera

10 MAWU OLANKHULIDWA

kumtunda kuno; iye anati, “Bambo Branham, inu mukuyeserakulitsutsa Baibulo.” Anati, “Ilo ndimbiriyakale yampingo.”

Ine ndinati, “Ilo si mbiriyakale. Ilo ndi Mulungu,Mwiniwake, mu zodindidwa.”

Iye anati, “Mulungu ali mumpingoWake.”27 Ine ndinati, “Mulungu ali mu Mawu. Ndipo chirichonsechotsutsana ndi Iwo, muchisiye icho chikhale chabodza.Chifukwa Iye anati, ‘Mulole Mawu Anga akhale owona ndipomawu a munthu aliyense abodza.’”

Iye anati, “Ife sikuti tizitsutsana.”28 Ine ndinati, “Ine sindinakufunseni inu kuti titsutsane,koma Baibulo limanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni ife tilingalirepalimodzi.’”29 Ilo limaneneratu zochita za Mlembi Iye asanazichite izo.Chotero, kukuuzani zimenezo, ndiye izo zikumuyika mwamunaaliyense ndi mkazi, paMalo Achiweruzo, mopanda chowiringulachirichonse. Ngati inu mutatenga chimene Amethodistiamanena za Ilo, chimene Abaptisti amanena za Ilo, zimeneAkatolika amanena, zimene Achipentekoste amanena, kapenampingo wina uliwonse, inumukhoza kudzapeza zokhumudwitsazina pa Chiweruzo. Koma ngati inu mutangoti mungosamalitsazimene Baibulo likuti zidzachitika, ndi pamene izo zidzachitike,ndiye inumudzazindikira zimene zikuchitikazo.30 Tsopano, izo siziri pa mbalambanda kuti anthu onseakhoza kumaziwona izo, pakuti Yesu anamuthokoza Mulunguchifukwa chozibisa izo ku maso a anzeru ndi aluntha, ndi kutiadzaziululire izo kwa makanda omwe akanakhoza kuphunzira.Talingalirani zaMulunguWamphamvuzonse atakhalamuMawuAke Omwe, ali ndi mphamvu yochititsa khungu olemera ndianzeru ndi—ndi aluntha mmaphunziro, kuchititsa khungu masoawo kuti iwo asakhoze kumuwona Iye, ndi kutsegula maso aosauka ndi osaphunzira.31 Zindikirani anthu awa ochokera ku Emau, Iye anatikwawo—kumvetsa kwawo kwa Iye kunali kutatchingidwa. Iwoankayankhula kwa Iye ndipo iwo sankadziwa konse Yemwe iyeanali, utali wa tsiku lonse. Mulungu akhoza kuzichita zimenezo,pakuti Iyeyo ndi Mulungu.32 Izo ndi ndendende zomwe Iye anachita kwa ansembeaja, alembi aja, chifukwa Izo zinali zitalembedwa kuti Iyeankayenera kuti achite zimenezo. Mulungu anachititsa khungumaso awo kuti ife tikhoze kukhala nawomwayi. Zindikirani, iwosanakhoza kuziwona, ziribe kanthu ndi aluntha mmaphunziromochuluka bwanji, iwo anali ndi unsembe wochuluka bwanji,zomwe iwo anali atazichita, iwo sakanakhoza kuwawonaIwo apobe, chifukwa iwo anali akhungu. Kupenya kwawo

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 11

mwina kunali twente-twente, mwathupi. Koma kupenya kwawokwauzimu!33 Chinthu chomwecho ine ndinali kuyesera kuti ndichinenemmawa uno za chigololo cha akazi, pomavala momwe iwoakuchitiramu tsopano. Iwo ndi azigololo. Mu Bukhu la Mulunguiwo ndi olakwa pa chigololo nthawi iliyonse pamene iwo avalazovala zowoneka mwachigololo. Moyo wawo, mosazidziwatu izi.Ine ndikukhulupirira akazi amenewo, ochuluka a iwo, zikwi zaiwo, ndi osalakwa, ndipo sakanati mwanjira ina iliyonse achitechigololo. Ndipo akazi osaukawo, ndi wina yemwe angawaloleiwo kumapitirira nazo, popanda kuziyalutsa izo ndi kuwauzachoonadi, amachita chigololo. Chimene, Baibulo limati, “Huleyemwe anakhala pamadzi ambiri, yemwe mafumu onse apadziko lapansi ndi anthu apa dziko lapansi, mipingo ndi zinazotero, anachita ziwerewere zauzimu ndi iye. Ndipo iye analiMAYIWAAZIWEREWERE,” zipembedzo.34 Ife timaliyang’ana Baibulo, pakuti Mulungu samatisiya ifemu mdima. Iye anatumiza Baibulo kuti litiuziretu zochitika izozisanachitike, ndi chikhalidwe kumene ndi nthawi yomwe izozikanati zidzabwere.35 Tsopano, ndicho chinachake chonga kuyang’ana pakalendara kuti uwone tsiku lomwe liri. Ngati iwe ukuganiza, titiili ndi lero Loweruka, Lamlungu, ndi chiyani ilo? Kayang’anenipa kalendara. Kalendara ikuuzani inu tsiku lomwe liri. Pameneinu mukuwona zochita za anthu, mwina mukapita ku tchalitchi,inu mumakawona—a…mukamva mabelu akuwomba, iweumadabwa kuti ili ndi tsiku lanji. Kayang’aneni pa kalendara,iyo ikakuuzani tsiku lomwe ilo liri.36 Ndipo pamene inu mukuwona mpingo ukuyamba kukhalamwachidziko, monga zinaliri mu masiku a Sodomu, kuliwonadziko la mpingo lonse likupita mu…kupembedza “mulunguwa m’badwo woipa uno,” ndi kumaziwona zimenezo; ndiyenkumawona gulu lapang’ono la ochepa litasonkhana kunja pansipa kudzodza kwa Mulungu, kumabala kachiwiri Moyo wa YesuKhristu, mwa Malemba zomwe zikuyenera kuti zizichitika, inumumadziwa ora limene inu mukukhalamo.37 Baibulo ili limaneneratu, mwa uneneri, tsiku limene ifetiri kukhalamo, ndi nthawi yomwe ife tiri kukhalamo, ndimtundu wa zochitika zomwe zikuyenera kuti zizichitika.Ilo limaneneratu izo ndendende mpaka ku lemba, ndiposilinayambe laphonya m’badwo umodzi, nthawi zonse. Palibenthawi imodzi yomwe Ilo linaphonyako konse, ndipo Ilosilidzatero, pakuti omwe anakonzedweratu kuti aziwone izoadzaziwona zimenezo. Yesu anati, “Palibe munthu angakhozekudza kwa Ine, kupatula Atate Anga atamukoka iye, ndipoonse omwe Atate andipatsa Ine adzabwera.” Awo ndi Mawukulumikizana ndi Mawu. Iwo sangakhoze kuchita kanthu

12 MAWU OLANKHULIDWA

kena kalikonse. Ife tikuzidziwa zimenezo, tsiku lomwe ife tirikukhalamo.

38 Koma monga izo zakhala ziri mu m’badwo uliwonse, anthuamalola anthu kuti aziika kutanthauzira kwawo ku Mawuawa, ndi kuwapangitsa iwo kuti achite khungu kwa chochitikachimene chachitika. Chinthu chofanana chinachitika ndi Afarisindi Asaduki. Ngakhale pamene Paulo anaima pamenepo ndikuyesera kuwerenga mobwereza Lemba, ndipo munthu winaanamuomba iye khofi chifukwa iye anamutcha wamsembewamkulu khoma lokongoletsedwa. Ndiyeno iwo anaphonyakumuwonaMulungu akutsimikiziraMawuAke oneneredwa.

39 Mukuona, Baibulo silimadzitsutsa Lokha; Baibulo ndiMulungu. Mulibe kudzitsutsa mwa Mulungu; Iyeyo ndiwangwiro.

40 Koma anthu, ndi kutanthauzira kwawo kwawo! Tsopanozindikirani, mundilole ine ndikusonyezeni inu, abwenzi.Mipingo siingakhoze kugwirizana iyoyokha pa kutanthauzirakwa Iwo. Amethodisti sangakhoze kugwirizana ndi Abaptisti,Abaptisti a Presbateria, Apresbateria a Pentekoste. Ndi pafupimabungwe osiyana fote a Chipentekosite, iwo sangakhozekugwirizana wina ndi mzake. Chotero inu mukuona, izozingakhale Babeloni kachiwiri, kusokoneza.

41 Koma Mulungu amachita kutanthauzira Kwake Kwake paMawu Ake. Iye analonjeza chinthu ichi, ndiyeno amachichitaicho Mwiniwake. Iye amapereka, Iyeyekha, kutanthauzira kwaiwo, chifukwa Iye amadzipanga Yekha kudziwika mu oralimenelo. Utali wake—Thupi la Khristu likupitirira, kuyambiraku mapazi mpaka ku mutu!

42 Zindikirani, ndiye ndicho chifukwa chimene anthu awaamalephera kuti azimvetse izo, chifukwa iwo amamvetsera kuzomwe winawake akunena za Iwo, mmalo moti akawerengeMawu monga momwe Yesu anawauzira iwo kuti azichitira,“Ndipo Iwo ndi Omwe amachitira umboni za Ine. FufuzaniMalemba, mwa Iwo inu mukuganiza kuti muli nawo MoyoWamuyaya, ndipo Iwo ali Iwo omwe amachitira umboni zaIne.” Mwa kuyankhula kwina, mvetserani, “Chiani? MuwerengeMalemba ndipo muwone chimene Mesiya ankayenera kutiadzachite. Mukawone nthawi imene Mesiya akanadzabwera.Mukawone yemwe anali woti adzamtsogolere Mesiya.Yang’anani pa oralo. Payenera kuti pakhale liwu la mmodziakufuula mu chipululu, Yohane. Ndipo inu mwachita kwaiye ndendende zomwe inu mumazifuna. Penyani zomwe Inendinkayenera kuti ndizichite pamene Ine ndibwera. Ndipotsopano kodi inu mwachita chiyani? Kodi ine ndalepherakuzikwaniritsa Izi?” Mwaona, Yesu akulankhula, “Kodi Inendalephera kuzikwaniritsa Izi?”

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 13

43 Zindikirani, pamene ife tikubwera mpaka mmusi kupyolamu Malemba madzulo ano, momwe kuti chirichonse chimenechinaneneredwa za Iye chinadzachitika ndendende basi momweizo zinkayenera. Iwo akadayenera kuchidziwa chochitika ichi.“Wotentheka uyu, Munthu wamng’ono yemwe anauka, wapafupi usinkhu wa zaka sate-firii ndi…kapena wa usinkhuwa zaka sate, ndipo anapita kumeneko ndipo ankadzineneraza mitundu yonse ya Kuwala, ndi Nkhunda zikutsika. Ndipo,bwanji, izo zinali basi za—zamanyazi.” Iwo anati, “Iye anabadwandi makolo apathengo, nkumadzinenera kuti Iye anabadwangati wobadwa kwa namwali.”44 Sanayenera iwo kudziwa kuti Yesaya ananena, mu Yesaya9:6, “Kwa ife Mwana wabadwa”? Sanayenera iwo kudziwansokuti Yesaya mneneri anati, “Namwali adzaima”? Iwo amayenerakuzidziwa zinthu zimenezi. Koma, inu mukuona, chinthu chakechomwe chinali, iwo anali kuziika izo penapake chamtsogolo.Ndipo Munthu uyu, kwa iwo, sanali kukwanira zofunikirazo.Koma Iye anawafunsa iwo, “Kafufuzeni Malemba, pakutiinu mukuganiza kuti mwa Iwo inu mumakhala nawo MoyoWamuyaya, ndipo Iwo ali Chinthu chomwecho chimenechikuchitira umboni kwa Uthenga Wanga.” Osati zomwewazamulungu wina ananena; koma zomweMulungu, Mawu AkeOmwe, anati zikanati zidzachitike! Ameni!45 Chomwecho izo ziri tsopano! Fufuzani Malemba, pakutiIwo ali Omwe amatiuza ife ora lomwe ife tiri kukhalamo,amatiuza ife ndendende zomwe zikanati zidzachitike mu tsikulino. Iwo ndi Omwe inu muyenera kumadalirapo, pakuti Iwoali Omwe akuchitira umboni wa Umunthu wa Yesu Khristu.Pakuti Baibulo linanena, kuti, “Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndikwanthawizonse,” chifukwa Iye ali vumbulutso la Mawu mum’badwo. Sizingakhoze kukhala zosiyanasiyana ayi.46 Chotero pa kumvetsera kutanthauzira kwa munthu,iwo akuwona kutsimikizira kwa Mawu a Mulunguakukwaniritsidwa, iwo amalephera kuti awawone Iwo.Chifukwa, izo zikumachitika nthawi yonseyo, koma chifukwaiwo akumvetsera…Ndipo Yesu anati, “Iwo ali atsogoleriakhungu.” Ndipo ngati wakhungu atsogolera wakhungu,nchiyani chimachitika kwa iwo? Tsopano kumbukirani, Baibulolinaneneratu kuti m’badwo wachipembedzo uno wa M’badwowa Laodikaya uwu unali wa khungu. Iwo anali atamusiya Iyekunja kwa mpingo. Palibe m’badwo wina, m’badwo wa mpingowina, umene Yesu anali kunja kwa mpingo. Koma m’badwo wampingo wa Laodikaya, Iye anali kunja, akuyesera kuti abwereremkatimo, “Ine ndayima pakhomo ndipo ndikugogoda.” Iyeamayenera kuti akhale ali mkatimo. Koma Iye anati, “Chifukwainu mukuti, ‘ine ndine wolemera, wochulukidwa katundu,sindikusowa kanthu,’ ndipo simukudziwa, simukudziwa kutiinu ndinu akhungu, kutsogolera akhungu, osauka mu mzimu,

14 MAWU OLANKHULIDWA

atsoka, omvetsa chisoni, amaliseche, ndipo simukudziwa izo.”Ndi chi-…Ngati munthu akanakhala wamaliseche pa msewu,womvetsa chisoni, wakhungu, ndipo inu nkumadziwa kuti alindi kuganiza kokwanira kuti inu mukhoza kumuuza iye kutiiye ali wa maliseche, iye akanayesera kuchita chinachake paizo. Koma pamene iye agwedeza mutu wake, nkumati, “Inesindilandira Zimenezo. Ndiwe ndani kuti undiwuze ine chotindichite? Ine ndikudziwa pamene ine ndaima.” Tsopano, ngatiawo si maonekedwe omvetsa chisoni, ine sindikudziwa. Ndipondizo ndendende zomwe Mulungu wa Baibulo ili ananenakuti mpingo ukanadzakhala ulimo, mu m’badwo woipa unopakali pano, mu m’badwo wa mpingo wotsiriza umene ife tirikukhalamowu.47 Zindikirani, koma kwa anthu, “Onse amene Inendimawakonda, Ine ndimawadzudzula.” Tsopano, ngati inumukudzudzulidwa ndi Ambuye, pa zomwe inu mukuchita,tulukani mu izo ndiye! Chokaniko ku zimenezo. “Onse ameneIne ndiwakonda, Ine ndimawadzudzula.”48 Tsopano, powona Mulungu, tsopano, bwanji ngati Afarisiawo akanati, “Dikirani miniti. Munthu ameneyo watipatsaife chitsutso ndithu, Iye anati, ‘Kafufuzeni Malemba, pakutimwa Iwo inu mumaganiza kuti inu mumakhala nawo MoyoWamuyaya; Iwo akuchitira umboni za Ine.’ Ziribwino kutiine ndiyang’anenso mu Malemba ndi kukapeza chimene Iyeakuyenera kuti azichita, Yemwe Iye ali, zomwe zikuyenera kutizizichitika. Ine ndiyenera kukayang’ananso ndi kukazipeza”?Mmalo mwa izo, iwo anapita kwa ansembe ndipo anawafunsaiwo, “Nanga bwanji Izi?” mukuwona kusiyana kwake? Iwoakanakhala ali kuwerenga Mawu.49 Mu Ahebri 1:1, Baibulo linati, “Mulungu, mu nthawizamakedzana,” ndizo, “nthawi zakale ndi mu makhalidweosiyana analemba Baibulo ndi aneneri.” Tsopano zindikirani,Iye analemba Baibulo mwanjira Yake Yake yosankhidwa.Mukuona? Tsopano, Iye sanasowe kuti achite kulilembaIlo mwanjira imeneyo, ngakhale kuti Iye azimupulumutsamunthu ndi Magazi. Iye sanasowe kuti azilalikira Uthenga ndimunthu; Iye akanakhoza kulola dzuwa kapena mwezi kapenanyenyezi zizilalikira Uthenga, Iye akanakhoza kuisiya mphepoziziung’ung’uza Uthenga. Koma Iye anasankha munthu! NdipoIye anasankha njira yomweMawuAke anadzera, ndipo izo zinalindi aneneri Ake omwe anakonzedweratu ndi kudzodzedweratu,pokhala gawo la Mawu a Mulungu, akulengeza vumbulutsola Mawu Ake kwa m’badwo umenewo ndi nthawi imeneyo.“Pakuti Mawu a Mulungu ankadza kwa aneneri okha.” SikutiIwo amabwera kwa wazamulungu. Ndisonyezeni ine Lemba.Iwo amabwera kwa aneneri okha. Mulungu sangakhozekunama. Chotero Mulungu analemba Baibulo mwanjira Yakeyosankhidwa, ndi aneneri Ake Ake osankhidwa; osati aneneri

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 15

omwe munthu anawasankha, koma aneneri omwe Mulunguanali atawasankha.50 Ndiye okhulupirira Ake ankayang’anira kukwaniritsikakwa zomwe mneneri wawo ananena, ndipo ndikokuzindikiritsidwa kuti iwo ndi aneneri a Mulungu. Chifukwa,choyamba, iwo anali odzodzedwa. Chotsatira, iwo ankakhalandendende ndi Mawu a ora. Ndiye ndizo nyota zake. Mwawona,ife tinadutsa zimenezo Lamlungu lathali. Aneneri ambiriabodza adzauka. Ndipo ife tinapereka kulongosola kwa momwekuti Balaamu ndi Mose, iwo onse atadzodzedwa ndi Mzimuwomwewo, mmodzi wa iwo anati, “Ndife tonse amodzi.Tiyeni tibwere tidzajowine, tiwayike asungwana athu ndi onsepalimodzi. Ife tiri nawo asungwana okongola kuno, ndipoanyamata inu mubwere kuno ndi kumadzazitengera nokhamkazi wabwino. Izo nzabwino, ndife tonse anthu amodzi,mulimonse, mtundu wofanana.” Mulungu sanawakhululukirekonse iwo chifukwa cha izo. Iwo anamvetsera kwa izo.51 Mukuona, dziko ndi—anthu akuyang’anira mpita winawotulukira waung’ono, cholambalala china chaching’ono,chidule china chaching’ono, koma mulibe zidule mu Mawua Mulungu. Liripo Dongosolo limodzi. Inu muyenera kutimuzidule nokha ndi kukwanira mu Dongosolo limenelo, osatikuyesera kuti mudule Dongosolo kuti likukwanireni inu.Aliyense ayenera kuti azichita zimenezo. Ndi njira yokha yomweMulungu ali nayo yochitira izo.52 Zindikirani tsopano, okhulupirira amawayembekezeraMawu amenewo kuti atsimikiziridwe. Mwawona, Iwosanalembedwe ndi munthu, koma ndi AmbuyeMulungu, choteroIlo si bukhu la munthu.53 Wina anati, “Izo ndi zolemba zina chabe za Chihebri.”Kodi Ahebri akanalemba kalata yomwe imawatsutsa okha?Kodi fuko labwino lija la Ayuda, ochita-mwaokha ndiopukutidwa, kodi iwo akanati alembe kusaeruzika kwawokomwe, kumadziweruza okha? Ndithudi ayi. Kumanena zamachimo ake omwe, momwe iwo analowerera mu kupembedzamafano, momwe iwo amachitira ziwerewere motsutsa Mawu aMulungu?Ayi, ayi. Iwo sibwenzi atanena izo, fuko lonyada ilo.54 Ilo si bukhu la munthu. Ilo ndi Bukhu la Mulungu.Ndipo munthu yemwe amawona masomphenya kapena amamvaLiwu la Mulungu, sankalimvetsa konse ilo (nthawi zochuluka)eniake, mu zochitika zambiri. Mwaona? Munthu sanalembeBaibulo, Mulungu analemba Baibulo. Ilo si liri…Ilo si Bukhula munthu. Ilo ndi Bukhu la Mulungu. Ilo ndi maganizo aMulungu akulongosoledwa kupyolera mu milomo ya munthu.Ndicho chimene chimalipangitsa Ilo kukhala Baibulo. Lingalirololongosoledwa ndi mawu. Ndipo pachiyambi panali Maganizoa Mulungu, Iye anawafotokoza Iwo kupyolera mu milomo ya

16 MAWU OLANKHULIDWA

aneneri Ake ndipo anawatsimikizira Iwo ndi antchito Ake.Mukuona? Zindikirani.55 Mulungu amachita kusankha Kwake Komwe, mwakukonzedweratu, anasankha aneneri a m’badwo uliwonse.Zindikirani izo. Iye amakonza chikhalidwe cha mneneriameneyo kuti chikwanirane ndi m’badwo umenewo. Mwawona,Iye amakwanira kachitidwe kake, chirichonse chimene iyeamachichita. Iye amakwanira ngakhale iye ali wophunzirakapena wosaphunzira. Iye amakwanirana nayo mphatsoyo,momwe ati azidzalalikira, mphatso zomwe iye ati adzakhalenazo. Ndi Uthenga wa m’badwo wake uwo, Mulunguanakonzeratu chinthu chinachake icho kuti chidzachitikandipo palibe chinthu china chingakhoze kutenga malo ake.Sindikusamala chomwe icho chiri, phindu lopangidwa ndianthu lingati, palibe chimene chingati chitenge malo ake.Iye anamukonzeratu munthuyo, mwina munthu waumbuli.Iye akanati amukonzeretu iye mtundu wina wa munthu.Chirichonse chomwe iye ali, Iye amamupatsa iye gulu lake,zake—mphatso zake, amamupatsa iye chikhalidwe chake,kachitidwe kake, ndi chirichonse chomwe chiri, momwe iyeamadzifotokozera yekha, ndi chirichonse chimene iye amachita.Iye amamupanga munthu wa oralo kuti aziwagwira anthu aoralo. Kulondola. Iye amachita zimenezo.56 Pa mapeto a m’badwo uliwonse, pamene mpingowatembenukira kwa dziko ndi tchimo, ndi kumatsamirapa kutanthauzira kwa munthu pa Mawu. Monga zakhalira,iwo nthawizonse, pa mapeto a m’badwo, amafika muchisokonezo chotero ndi azamulungu awo ndi ansembempaka izo nthawizonse zimakhala zosokonezeka. Nthawizonsekutanthauzira kwawo ndi kolakwika, palibe nthawi imodzi izozinayamba zalephera kukhala zolakwika. Ndipo palibe nthawiimodzi yomwe Mawu a Mulungu anayamba alepherapo kukhalaolondola. Ndiko kusiyanitsa kwake.57 Tsopano inu mukuwona, Mulungu analemba Baibulo,Mwiniwake. Tsopano, Mulungu akhoza kuyankhula. Moseanati Iye anayankhula kwa iye. Yeremia anati, “Iye anayikaMawu mkamwa mwanga.” Ndipo Mulungu akhoza kulemba.Iye analemba malamulo khumi ndi chala Chake Chomwe.Iye analemba pa makoma a Babeloni. Ndipo, kumbukirani,ku Chipangano Chakale chokha, nthawi thuu sauzandeaneneri amati, “PAKUTI ATERO AMBUYE!” Mulungu akhozakulankhula, Mulungu akhoza kulemba. Zedi. Pafupi nainte pazana a Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane, ndi Mawu kumenea Mulungu Mwiniwake, Yesu Khristu akulankhula. Chotero,ngati Mulungu angakhoze kulemba, ngati Mulungu angakhozekuwerenga, ngati Mulungu angakhoze kulankhula, Iye sangathekuwapangitsa ena kuti achite zomwezo? Kodi Iye sananenekwa Mose, “Ndi ndani amamupangitsa munthu kusayankhula

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 17

kapena ndi ndani amamupatsa iye kuyankhula?” MulunguanalembaBaibulomwa aneneri, njira Yake yochitira izo.58 Tsopano nthawi iliyonse imene mpingo ufika posokonezeka(ndipo Mulungu anadziwiratu iwo akanadzatero, pakuti Iyeanadziwiratu zinthu zonse), chotero Iye amakhala naye mneneriwinawake wokonzekeredwa kwa m’badwo umenewo, kutiayitanire osankhidwa Ake ndi Mawu Ake otsimikiziridwa azizindikiro ndi zodabwitsa, ndi kutsimikizira kwa Mawu Ake,“kuwatsimikizira Mawu ndi zizindikiro zotsatirapo,” momweIye analonjezera. Iye amapereka kutanthauzira koona mnenerimwiniwakeyo atatsimikiziridwa kale.59 Onse kupatula iwo, osankhidwa omwe iye watumizidwirako,amamuda iye. Tsopano,mufufuze nthawi iliyonse ndipomuwonengati uko kuli kulondola kapena ayi. Iwo okha omwe Iyewatumiziridwirako! “Iye anadza kwa Ake Omwe, ndipo AkeOmwe sanamulandire Iye ayi. Koma onse omwe anamulandiraIye, kwa iwo Iye anawapatsa mphamvu kuti akhale anaa Mulungu.” Zindikirani, palibe…kufufuza kulikonse kwaMawu, mu chochitika chirichonse, ndiponso pamapeto am’badwo uliwonse kapena pachimake, kapena mphambano,monga ine ndalalikira pa izo nthawi zambiri.60 Tayang’anani pa m’badwo wa Nowa, pachimakechisanachitike chiweruzo. Nchiani chinachitika? Nowa, linalibanja lake lokha limene linamukhulupirira bamboyu. Ena onsea iwo anamutsutsa iye. Ndipo analiwononga dziko lonse.61 Mu masiku a Abrahamu, gulu la Abrahamu lokha ndilimene linakhulupirira. Pamene angelo anapita nakalalikira kuSodomu, Loti yekha ndi mkazi wake ndi ana aakazi awirianatulukamo, ndipomkaziyo anasanduka chulu chamchere.62 Mumasiku a Mose, osankhidwa okha a Israeli anatulukamo.Ndipo Farao ankamuda iye.63 Mumasiku a Eliya, chirichonse (pafupifupi) kupatula amunaseveni sauzande, aliyensewa iwo ankamuda iye, fuko lonselo.64 Mu masiku a Yeremia, bwanji, iwo anaponyera chipatsochosacha pa iye, ndipo anamutcha iye wotentheka, chifukwaiye anagona mu mmbali yake kwa masiku ochuluka chotero,ndi mbali inayo, ndipo—ndipo anatenga zinthu ndipo anapangazophiphiritsa. Iwo ankamuda iye.65 Yesaya mneneri, iye anawutsutsa mtundu umenewomochuluka kwambiri mpaka iwo anamucheka iye pawiri ndimacheka. Zoona.66 Yohane M’batizi. “Iye anali munthu wamtchire kumusikumeneko, wopenga wina wofuula.”

Onse kupatula—kupatula ophunzira awo omwe iyeanawapereka kwa Yesu Khristu ngati mpingo! Ndi zimenezotu.Yohane anawapangitsa anthu kukonzekera. Ndi angati omwe

18 MAWU OLANKHULIDWA

iye anali nawo? Inu mukhoza kuwawerenga iwo pa zalazonse…manja onse, zala zanu, kuchuluka kwake omwe Yohaneanawapereka kwa Yesu pamene Iye anadza. Tsopano, nangabwanji KudzaKwake kwachiwiri?Muganizire zimenezo.67 Koma pamene okhulupirira Baibulo owona awawonaMawu akutsimikirizidwa poyera kwa m’badwowo, iwoamawakhulupirira. Palibe njira yowachotsera iwo kwa Iwo,kuwakhulupirira Iwo. Iwo amasindikiza ngakhale umboni wawondi magazi awo. Iwo amawakhulupirira Iwo. Ndi pamene zirikwa iwo, okonzedweratu, iwo a m’badwo winawake uwo ameneamawaona nakhulupirira.68 Enawo sangakhoze basi kuwaona Iwo; iwo achititsidwakhungu. Tsopano, inu mukuti, “Iwo sangakhoze kuwaonaIwo.” Tsopano, monga Balaamu, nchifukwa chiani Balaamusankakhoza kuwaona Iwo? Iye anali mneneri, wodzodzedwa.Nchifukwa chiyani Farao sankakhoza kuwawona Iwo? Pameneiye anawona dzanja la Mulungu litabwera pansi ndipo nkuchitazozizwitsa mmenemo, izo zinangowuumitsa mtima wake. Ndikulondola uko? Nchifukwa chiani Datani sankakhoza kuwaonaIwo, Myuda mwiniwake? Pomwe apo, anali atabwera kupyolamu Nyanja Yakufa, ndipo ankadya mana usiku uliwonse, omweankagwa mwatsopano, ndipo apobe sankakhoza kuwawonaIwo. Nchifukwa chiani Kora sankawawona Iwo? Nchifukwachiyani Kayafa sanawawone Iwo? Iye anali wamkulu wachipembedzo cha dziko lapansi pa nthawi imeneyo. Nchifukwachiani iye sanaone kuti ameneyo anali Mesiya? Nchifukwachiani Yudasi sanawawone Iwo? Yudasi anali pomwepo ndi iwo,kumayenda ndi iwo, kumachita zozizwitsa ndi iwo. KomaMawuankayenera kuti akwaniritsidwe. Baibulo limati iwo analeredwakuti adzatenge malo amenewo. Iwo analeredwa kwa cholingachimenecho. Izo nzoona. Aroma 8 amanena choncho.69 Tsopano okhulupirira akhoza kuwaona Mawu akupangidwathupi mu kam’badwo kawo, Mulungu akulankhula. Tsopano,okhulupirira owona enieni awo, zikwi seveni awo (kapena kodiiwo anali seveni handiredi?) mumasiku a Eliya. Seveni sauzandendiko kulondola. Mu masiku a Eliya, analipo anthu sevenisauzande kwa pafupi mamilioni awiri kapena atatu, omweanawaona kuti Iwo anali olondola. Osati ngakhale kahandiredika anthu, nkomwe. Koma iwo anawona kuti Iwo anali olondola.Iwo anamuwona Mulungu akuwonetseredwa. Wamasiye wakaleuja yemwe Elisha anatumizidwako, iye anapita kuti akatengetinkhuni tija, kuti akapange mkate, ndi wongokwanira basikuti adzipangire iye mkate ndi mwana wake, ndiyeno afe.Koma penyani Eliya, iye anati, “Ndipangire ine umodzi,choyamba. Chifukwa, PAKUTI ATERO AMBUYE, mtsukosudzatha ndipo ngakhale msupa sidzauma mpaka tsiku lomweAmbuye Mulungu ati adzatumize mvula pa dziko lapansi.”Mopanda funso, iye anauyamba apo pomwe kuti akapange

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 19

mkate ndipo anakaupereka iwo kwa iye. Anati, “Panga wangapoyamba, ndiyeno upite ukapange wina wa iwe ndi mwanawako.” Pakuti, iye anamumva bambo uyo, ndipo anayang’ana paiye; iye anali mbewu yokonzedweratu.70 Ochuluka a iwo ankati, “Chabweranso chidempetechokalamba chija. Mulungu watitemberera ife chifukwa chaiye,” kumbukirani, Eliya. Atati, “Iwe ndiwe yemwe ukuvutitsaIsraeli.”71 Iye anati, “Iwe ndiwe yemwe ukuvutitsa Israeli.” Mukuonayemwe Mulungu…Mawu a Yemwe Iye anali kuwatsimikizira?Mawu Ake omwe.72 Tsopano Baibulo limati iwo analeredwa kwa cholinga ichi,koma pamene…wo—wosakhulupirira. Koma tsopano pamenewokhulupirira owona akhoza kuwawona Mawu a m’badwoumenewo akupangidwa thupi, Mulungu akulankhula kupyoleramumilomo yamnofu ndiyeno nkumachita ndendende zomwe Iyeanati Iye akanadzachita, izo zimachikhazikitsa icho!73 Tsopano muzipenya zonse za izo. Musamapenye zizindikiro.Ngati inu mupenya zizindikiro, inu mupusitsidwa motsimikizabasi monga dziko. Aneneri abodza aziuka ndipo azisonyezazizindikiro ndi zodabwitsa zomwe ziti ziziwanyenga osankhidwangati kukanakhala kotheka. Penyani Mawu. Tayang’anani paansembe awa, aneneri awa, mneneri wa Chihebri ataimapamenepo. Zedekia ali ndi nyanga zazikulu ziwiri, ndipo akuti,“Ine ndine mneneri wodzodzedwa-wa-Mulungu.” Ndi zoona.“Ine ndiri nawo firii handiredi ndi nainte-naini pomwe panoali ndi ine, ndipo Mzimu Woyera pa ife, ukutsimikizira ndikumati dziko limenelo ndi lathu. Tiyeni tipite ndipo tikalitengeilo. Ndipo ndi nyanga izi, Ahabu, inu mukamukankha mdanikumchotsa pa malowo, chifukwa Mulungu anatipatsa ifemalowo.”74 Mpenyeni munthu wachipembedzo uja, munthu wabwino,Yehosafati, anati, “Kodi inumulibemmodzi winanso?”75 “Mmodzi winanso? Apo pali foro handiredi akugwirizana!”Iye anati, “Inde, alipo mmodzi winanso kuno, koma inendimadana naye.” Anati, “Iye nthawizonse amatizazira tonseife ndi kumatiuza ife kuti ndife ochimwa kwakukulu, ndichirichonse.” Anati, “ine ndimadana naye iye! Iye, iye ndiMikaya, mwana wa Imlah.”76 Iye anati, “O, musalole kuti mfumu inene choncho. Pitanimukamuitane iye ndipo tiyeni timve zomwe iye amanena.”77 Chotero iwo anamubweretsa iye kumusi uko. Iye anati,“Ndipatseni ine usikuuno ndipo ine ndiwona chimene Ambuyeanganene pa izo.”78 Ahabu anati, “Ine ndikukuchenjeza iwe, usati undiuze inekanthu kena koma choonadi.”

20 MAWU OLANKHULIDWA

79 Ndipo bambo anabwerapo, anati, “Tsopano, ngati iweukufuna kuti ubwerere mu chiyanjano chabwino, ukangonenamonga ena onsewo.”

Mikaya anati, “Ine ndingonena basi mongamomweMulunguatanenere.” Mwawona?80 Mmawa wotsatira, iwo anatuluka. Mafumu anavala miinjiroyawo, anakhala ku chipata, onse apamwamba. Mneneri atayimapamenepo. Anati, “Tsopano, wotentheka iwe, iwe ukuti chiyanipa izi?”81 Anati, “Zipitani uko.” Anati, “Koma ine ndinawona Israeliatamwazikanamonga nkhosa zopandam’busa.”82 Iye anak-…anatenga dzanja lake ndipo anamubwanyulaiye pakamwa. Mneneri kumubwanyula mneneri pakamwa.Tsopano, aneneri onse odzodzedwa awo ataima pamenepo,analosera, foro handiredi kutsutsana ndi mmodzi, izozinkawoneka zamphamvu kwambiri. Tsopano, mu unyinji waupo nthawizonse simumakhala chitetezo. Zimatengera pa maloomwe iwo ali…chimene iwo akuchitira upo, chomwe upo wawouli. Panalibe chitetezo apo kwa mfumu, ndipo iye anatengaunyinji umenewo kuti upo wawo unali wolondola. Koma ngatiiye akanangoti ayime ndi kutembenuzira mmbuyo mpukutu ndikuyang’ana chimene Eliya anali atangochinena.83 Ndiye, Mikaya sakanakhoza kunena chirichonse, iyesanadziwe, pamene mwina Mulungu anamukhululukira iyechifukwa cha izo. Koma poyamba, pokhala mneneri, iyeanapita kwa Mulungu kuti akapeze chimene Mulungu ananena.Ndipo iye anakapeza chimene Mulungu ananena. Iye anati,“Ine ndinamuona Mulungu atakhala pa mpandowachifumu,ndipo Iye anati…anali ndi aphungu Ake onse Akumwambaatasonkhana momuzungulira Iye, anati, ‘Ndi ndani yemwe Ifetingamutenge kuti apite pansipo ndi kukamupangitsa Ahabukuti abwere kuno, kuti Ife tikhoze mwanjirayina kukwaniritsauneneri umene unapangidwa pa iye?’”84 Mukuona, uneneri, Eliya anali atanena kale, “Agaruadzanyambita magazi ako.”85 Ndipo chotero iye anati “anauwonamzimuwabodza ukupitammwamba kuchokera pansi, unakwera, unabwera mmwambapamaso pa Iye, unati, ‘Ine ndipita pansi ndipo ndikalowa mwaaneneri ake, aneneri a Ahabu, ndipo ndikawapangitsa iwo kutianenere zabodza.’”86 Tsopano, Mulungu ankadziwa kuti amuna aja analiodzikweza kwambiri ndi odzadza kwambiri ndi ziphunzitsozachipembedzo mwakuti iwo ankaganiza kuti anali ndi chinachirichonse molondola. Iwo sankazindikira Mawu a oralo.Chotero Mulungu anati, “Iwe ukapambana; zipita pansi.” Ndipopamene Mikaya ananena zimenezo, izo zinawapangitsa iwokulosera pansi pa mzimu woipa. Iwo bwezi atachotsa chozikira

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 21

ku lamya, kapena akanaizimitsa wailesi, kapena akanachitachirichonse; iwo atamva Icho chikubwera mowatsutsa iwo,anaimirirapo ndipo anayenda natuluka. Koma penyani chomwechinachitika. Tsopano,Mikaya anachita kufufuzamasomphenyaake ndiMawu olembedwa, chotero iye anadziwa.87 Iye anati, “Pamene ine ndizibwera…Mudzakamuikemunthu ameneyo mu ndende, muzikampatsa iye madzi achisonindi mkate wa chisoni. Pamene ine ndikabwererako, inendidzathana naye iye.”88 Iye anati, “Ngati inu muti mukabwerere konse, Mulungusanayankhule ndi ine.” Ndi pamene iye amadziwa kutimasomphenya ake ndi ndendende ndi Mawu aliwonse a oralimenelo. Iyo inali nthawi ya Ahabu.89 M’bale, mlongo, lino ndi ora ndi nthawi ya kuitana kutititulukemuBabeloni. Kuwala kwamadzulo kuli pano. Ziyendanimu Kuwala pamene kudakali kuwala. Zindikirani, okhulupiriraanawaona Mawu akuwonetseredwa ndipo anawakhulupiriraIwo. Yesu anati, “Nkhosa zanga zimalidziwa Liwu Langa,Mawu Anga, zizindikiro Zanga za m’badwo. Wabodza iwosadzamutsatira.”90 Tsopano tiyeni tifike ku nkhani yathu, chifukwa inendikuwona kuti ine ndikupita kutali. Ine ndikufuna kutinditsimikizire pa mzere wa pemphero uwo mochuluka. Tiyenitibwerere ku nkhani tsopano yomwe tiri kuilingalira, panokwa miniti. Chabwino, izo zidzachitika kachiwiri monga izonthawizonse zimachitira, mwa chizolowezi.91 Mulungu anatumiza mneneri Wake, Yohane, monga MawuAke anali atanena, analonjeza mu Malaki 3, “Taonani, Inendidzatumiza mtumiki Wanga patsogolo pa nkhope Yanga, kutiadzakonzeketsere njira.” Yohane anachitira umboni chinthuchomwecho. Ndipo ife tikupeza naponso, mu Yesaya 40:3, kutiYesaya anati, “Padzakhala liwu la mneneri, wina wofuulamu chipululu, ‘Konzani njira ya Ambuye.’” Mwaona? Maulosionse awo! Ndi—ndipo taonani, zindikirani mwamsanga, Lembalinamuzindikiritsa iye.

Pamene iwo anati, “Ndiwe ndani? Kodi ndiweMesiya?”Iye anati, “Si ndine ayi.”“Kodi ndiweYeremiya? Aneneri, kapenammodziwa iwo?”

92 Iye anati, “Si ine ayi. Koma ine ndine liwu la mmodziwofuulamu chipululu, monga ateromneneri Yesaya.”93 Inu mukuganiza kuti iwo akanazikhulupirira zimenezo? Ayi,bwana. Chifukwa? Iye sanabwere kudzera mu mpingo wawo.Iye sanali wa kwawo…Mwawona, iye anapita ku chipululu pausinkhu wa zaka naini, ndipo anachokako ali sate. Uthengawake unali waukulu kwambiri kuti apite kudzera mu sukuluya zamulungu; iye anali mmodzi woti amuwonetsere m—Mesiya.

22 MAWU OLANKHULIDWA

Ndipo aliyense akanati azimukokera iye mbali iyi ndi mbali iyo.Ndipo Mulungu anamutumiza iye ku chipululu, itachitika imfaya abambo ake, Zakaria. Ndipo iye anali wansembe, koma iyesanatsatire konse mzere wa abambo ake.94 Chifukwa, aneneri samabwera kuchokera mu zinthuzoterozo monga izo. Iwo amabwera kuchokera ku maikoovuta, chipululu. Palibe munthu yemwe amadziwa kumeneiwo amachokera, kapena momwe iwo amawukira powonekera,kapena ina iliyonse yambiriyakale yawo. Iwo amangotulukirapondi kulalikira Mawu, ndipo Mulungu amangowachotsapo iwo,ndipo amapita kutali; amautsutsa m’badwo umenewo, ndipoamasunthirabe kuMawuAke, kumayembekezera tsiku lalikulu.95 Mpingo sunamukhulupirire iye, chifukwa iye sankadziwikakwa iwo. Iwo analibe umboni wa kudzodzedwa kwake pamabuku awo, chotero choncho iwo anamukana iye. Mwawona,iwo sanawakhulupirire Mawu otsimikiziridwa a Mulungu,mwachimvekere, chilembo ndi chilembo. Mukuona? Malaki 3,Malemba awiri oti amutsimikizire iye, Malaki 3 ndi Yesaya40:3. Mwawona, Malemba onse awo ankayankhula za munthuwakudza, kuti adzakonze njira ya Ambuye. Iye anakwaniritsamafotokozedwe aliwonse a izo.96 Iye anali woti adzakhale mneneri. “Ine ndidzatumiza kwainu Elisha.” Ndipo apo iye anali, mwanjira yolimba iliyonse.Taonani momwe khalidwe lake linagwirizanira ndi Eliya. Eliyaanali munthu waku chipululu, chomwechonso anali Yohane;wokhala kunja. Iye sanali munthu wosalala, iye anali munthuwokhakhala.97 Zindikirani kachiwiri, Eliya anali wodana ndi akazi, iyeanamuuza Yezebeli zonse za utoto zake, ndi poti ayambirepondi kulekezerapo. Chomwechonso anali Yohane. Yezebelianayesera kuti amuphe Eliya, analumbira pa milungu yake kutiakanawudula mutu wake pa iye. Chomwe anachitanso Herodia.Mwawona?98 Nthawizonse muziuyang’ana uthenga wawo, muziyang’anazomwe iwo anazichita. Tsopano ife tikupeza kuti ngati iwoakanati ayang’ane mmbuyo ndi kuwona chimene Baibulolinanena, ndi kuyang’ana chikhalidwe cha munthuyo ndimomwe iye analiri wangwiro mu nthawi ndi Malemba ndichirichonse, iwo akadayenera kudziwa kuti uyo anali iye.Pafupi theka la dazeni anadziwa zimenezo. Ndiko kulondola.Osapitirira theka la dazeni anazizindikira izo. Iwo anapita kutiakamumvetsere iye, koma iwo samakhulupirira Izo. Mwawona?Chifukwa? Iwo sanakhulupirire kuzindikiritsidwa kwa unenerimu ora lawo.99 Zindikirani, iwo anamuseka iye, kumamutcha iye “wokuwawina, wakuthengo, wotentheka wosaphunzira wopandamaphunziro, ‘uyu, sindiye, mtengeni, tenga, bweretsa,’ zina

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 23

zotero.” Mwa chizolowezi iwo amamuweruza iye ndi kuphunzirakwake. Iwo amamuweruza iye ndi galamala yake, momweiye anali kuvalira. Iye anali ndi chidutswa cha chikopa chankhosa momuzungulira iye, ndipo atavala lamba wa chikopacha ngamira, iye anali yense wamanyenje. Akuyenda mmadzi;wopanda mpingo, wopanda guwa, wopanda chiyanjano; iwosakanakhoza kuzilandira zimenezo; iwo anali akupembedzamulungu wa mdziko. Mwawona?100 Ine sindikutanthauza kuti ndinene tsopano kuti kulibeaneneri abodza amene amabwerapo, monga Yambre ndiYane. Koma momwe inu mumafunira kumachitira, ndi kutimudzifufuza uthenga wapachiyambiwo ndi Mawu, ndiyeinu muzipeza izo; m’badwo womwe izo zirimo, ndi zomwezinaneneredwera kwam’badwo umenewo.101 Ndiye uneneri wa Yohane unatsimikiziridwa mu dongosoloLake la Mulungu. Penyani ungwiro wake. Baibulo linati,“Mawu a Ambuye amadza kwa mneneri.” Ndipo Yesu analiMawu. Ndipo Yohane anali kunenera za kudza kwa Mawukuti akwaniritsidwe; ndipo Yesu, Mawu, anadza kwa mneneri,mmadzi. O, zokongola bwanji! Kusalephera kwake…Mukuona?Mawu anali chinthu chosowa mu tsiku limenelo. Apa pakudzamneneri, akuti, “Ine ndine liwu la Mawu.”

Iwo anati, “Kodi ife tichite chiani?’102 Anati, “Ine sindiri woyenera kuti ndimasule nsapatoZake. Koma alipo Mmodzi waima pakati panu, penapake,Iye adzakhala Mmodzi yemwe ati adzakubatizeni inu ndiMzimu Woyera ndi Moto. Chokupizira Chake chiri m’dzanjaLake, ndipo iye adzayeretsa bwinobwino dwale Lake, ndikuwotcha mungu ndi moto wosazimitsika, kutengera njere kunkhokwe.” O, mneneri wakeyo! Yesu anati sipanayambe pakhalamunthu wobadwa mwa mkazi wamkulu monga iye, mpaka tsikulimenelo. O, mphamvu zakezo! Momwe iye ankadziwira pameneiye anali atayima! Iye ankadziwa ndendende. Iye anamvakuchokera kwa Mulungu, ndipo izo zinali chimodzimodzindi Mawu, kotero iye samasamala zimene anthu ankanena.Iye analalikira Iwo ndipo analosera Iwo, mulimonse. Ndipopenyani, pamene munthu ayima ndi chomwe chiri Choonadi,ndiye Mulungu amakhala wokakamizidwa kuti amutsimikiziremunthu ameneyo kukhala Choonadi.103 Pamene Mose anabwera kumeneko mu Igupto, ndipo anati,“Ine ndinali ku chipululu kutaliko, ndipo ine ndinawonamtengo uli kuyaka, ndipo iwo sunanyekepo. Ine ndinapitampaka ku mtengowo, ndipo, pamene ine ndinatero, apopanali Lawi Lamoto lalikulu litapachikika mmenemo. NdipoLiwu linati, ‘INE NDINE YEMWE NDIRI.’ Ndipo Iyeanandiuza ine kuti nditenge ndodo iyi ndi kubwera kunokondi kumadzachita zozizwitsa izi, ndipo Mulungu azitsimikizira

24 MAWU OLANKHULIDWA

Mawu Ake.” Anatambasula ndodo yake, pamenepo panadzautitiri ndi ntchentche, ndi mdima ndi zina zotero. Ndiyenokuti amutsimikizire mneneri ameneyo, Iye anawabweretsaokhulupirira awo mmbuyo mpaka ku phirilo, ndipo Mulunguanabwera pansi mu Lawi Lamoto lomwelo, pa phiri lomwelo,ndipo anatsimikizira kuti zimenezo zinali zolondola.

Tsopano taonani zomwe Iye wachita mu tsiku lino.Ndendende.104 Tsopano, Mawu amadza kwa mneneri ndipoamamutsimikizira iyeyo kuti ndi munthu woona, munthuyemweyo amene Malemba anati iye akanadzakhala ali.Mwamsanga tsopano. Koma, kachiwiri, Yesu anadza mwamawonekedwe osiyana ndi kutanthauzira kwawo kopangidwandi anthu kwa uneneri. Munthu anali atatanthauzira zomwezikanati zidzakhale. Ndithudi. Achipresbateria amaganizakuti izo ziyenera kukhala kwa iwo. Penyani pamene Mulunguakuchita chirichonse, penyani bungwe lina lirilonse limaukandi china. Eya, nthawizonse zakhala ziri mwanjira imeneyo.Iwo ali nawo Ayambre ndi Ayane kulikonse. Zindikirani, iwoankanena gawo la Mawuwo. Koma, molingana ndi Mawu amneneri, Lemba lirilonse!105 Iwo anaziphonya izo kachiwiri, mwa chizolowezi,anamutcha Iye wambwebwe, “mdierekezi; Belezebule,”ndipo ankati Iye akudzipanga Yekha Mulungu, pamene iwoankayenera kuti adziwe, mwa Baibulo lawo lomwe, kuti Iyeanali Mulungu.

Zindikirani, Iye analoseredwa ndi Yesaya, Yesaya 9:6, anati,“Dzina Lake azidzatchedwa Mulungu Wamphamvuzonse, AtateWosatha.” Sipadzakhala Atate enanso pambuyo pake, chifukwaIye anali Atate woyamba pachiyambi, Iye ali Atate yekhayo;anati, “Inu musadzamutche munthu wina aliyense wapadzikolino, ‘Atate,’ nkomwe, pambuyo pake.” “Iye ali—MulunguWamphamvuzonse, ndi AtateWosatha,Wauphungu, KalongawaMtendere.” Ndithudi.106 Tsopano, iwo anali atachita kwa Iye zomwe aneneri onseanazindandika kuti iwo akanati adzazichite, basi momwe iwoakuchitira mu M’badwo wa Laodikaya uno womwe, kumuikaIye kunja kwa mpingo. “Akhungu, amaliseche, ndipo sakudziwaizo.” Basi zomwe mneneri ananena, mneneri wa Baibulo.Ochititsidwa khungu ndi miyambo ya anthu, iwo anamuika Iyepanja, Mawu kuwatulutsa mu mipingo yawo, mwa chizolowezi,monga zinaneneredwera kwa iwo.107 Zindikirani tsopano, mwamsanga tsopano. Musaphonyeizi tsopano. Nkhani yake ndi iyi, momwe Yesu anadzipangiraIyeyekha kudziwika kwa ophunzira awiri awa kuti Iye analiMesiya wawo! Tsopano, maso onse mbali ino. Ndi kunja mudziko, musaphonye izi tsopano. Ife tayesera kukuuzani inu

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 25

kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, analembedwa ndi MulunguMwiniwake, kupyolera mu milomo ndi uchipangizo wa munthu.Mulungu akhoza kulemba, Mwiniwake. Mulungu akhozakuyankhula, Mwiniwake. Mulungu akhoza kuchita zimene Iyeakufuna kuchita, koma Iye anamusankha munthu kuti azichitazimenezo chifukwa munthu yemwe anazilemba Izo ali gawola Mulungu. Chotero, Mulungu analemba Baibulo. Amunawosankadziwa nkomwe zomwe iwo anali kuzilemba,mwa kuganizakwawo kwawo kwaumunthu. Iwo mwina ankatsutsana ndiIwo, koma iwo analemba Iwo. Iwo sakanakhoza. Baibulolimati, “Anthu akale, pamene iwo anali kusunthidwa ndiMzimu Woyera!” Mulungu ankasuntha manja awo, ankasunthamaso awo mwa masomphenya. Iwo sakanakhoza kunenakanthu kena koma zomwe iwo anali kuziyang’ana apo. Iwosankakhoza kuyankhula kanthu kena, chifukwa Iye anali ndiulamuliro wathunthu pa lirime, chala, chiwalo chirichonse chathupi chinali mu kusuntha kwathunthu ndi Mulungu. Palibezodabwitsa Baibulo limati iwo anali amulungu, iwo anali gawolaMulungu! Iye anali chidzalo chaMulungu.108 Zindikirani momwe Yesu, Mawu, anapangira ophunziraawiri osweka mtima awa kudziwa kuti Iye anali Mesiya wawo,Mesiya, Mawu olonjezedwa. Zindikirani zomwe Iye anachita,Iye anazitengera ku uneneri. Zindikirani. “Opusa, ochedwakukhulupirira zonse zomwe aneneri analemba.” Tsopano, Iyesananene konse, “Chabwino, chiani, kodi mpingo ukuti chianipa izi?”109 Iwo anamupatsa Iye nkhaniyo. Iwo ankadziwa zochitikazonse zomwe zinachitika. Iwo onse anali achisoni. Iwo anayambakumuuza Iye, “Kodi Ndinu mlendo basi kuno, kapena Inusimukudziwa zomwe zachitikamu Yerusalemu?”110 Iye anati, “Zinthu zitizo?” Ngati kuti Iye samadziwa.Mwawona, Iye amachita zinthu nthawizina kungoti awonezomwe inu muchite nazo izo. Mukuona? Anati, “Zinthu zitizo?Anali ndani ameneyo? Nchiyani chinachitika?”111 “Kodi ndinu mlendo chabe?” Ndipo anali akuyankhula nayekumene Munthu yemwe iwo anakhala naye kwa zaka zitatu nditheka, ndipo samamudziwa Iye.

“Zinthu zitizo? Chachitika ndi chiani?”112 “Chabwino,” iwo anati, “Yesu waku Nazareti, yemwe analiMneneri. Mulibe kukaikira mu malingaliro mwathu. Iye analiwamphamvu mu Mawu ndi zochita pamaso pa anthu onse. Ifetinamuwona Iye akuchita zinthu zomwe Iye anazindikiritsidwanazo ngati Mneneri wa Mulungu kwa m’badwo uno. Ifetikuzidziwa zimenezo. Ndipo ife timakhulupirira kuti Iyeakanakhala ali Muomboli, kuti Iye akanati adzawomboleIsraeli.”

26 MAWU OLANKHULIDWA

113 Ndiye Iye anatembenuka ndipo anati, “Inu opusa, ochedwamu mtima kukhulupirira zonse zomwe aneneri ananena zaIye kuti sizikanati zidzachitike?” Mwawona? Muoneni Iyetsopano akubwerera ku uneneri. Ndi chidzudzulo bwanji kwaokhulupirira, ankadzinenera kuti iwo ankamukhulupirira Iye!114 Mukuona mmene Iye anafikira pa phunzirolo. Iyesanangofika poyera pomwe ndi kuti, “Ine ndine Mesiya wanu.”Iye akanakhoza kuchita zimenezo, pakuti Iye anali. Komazindikirani Iye anazizindikiritsa Yekha mu Mawu, ndiye iwoakanadziwa. Ngati Iye akanati anene zimenezo, Iye akanakhozakunena izo ndipo izo sizikanakhoza kukhala chomwecho;koma pamene Iye anapita ndi kuyamba kumayankhula pazonse aneneri ananena za Iye, ndipo iwo anaziwona izo, ndiyeiwo akanakhoza kudziwa mwa wokha, ngati iwo anali ana aMulungu. Koma anaitanira tcheru chawo ku zomwe anenerianali atanena ndi kuti aziyang’anire mu nthawi yomwe Mesiya,m’badwoWake, ukanati udzawonetseredwe. Iye, monga Yohane,analola Mawu, Baibulo, lizindikiritse Uthenga wawo. Mneneriwoona aliyense akanachita zimenezo. Eya. Sanabwere apo ndikuti, “Ine ndine Iye. Ine ndine…” Uyo si mneneri woona waMulungu. Mwawona? Koma Iye anati, “Mubwerere mMalemba.”Mwawona, Iye samalephera konse njira Yake yochitira izo.Mwawona?

Iye anati, “Ife tikumudziwaMose.”115 Iye anati, “Ngati inu mukanamudziwa Mose, inumukanandidziwa Ine.” Iye anati, “Mose analemba za Ine.” Anati,“Fufuzani Lemba, mwa Iwo inu mukuganiza inu mumakhalanawo Moyo Wamuyaya, ndipo Lemba ndi lomwe limachitiraumboni za Ine. Mupite ndi kukayang’ana mu Lemba ndikukawona izo.”116 Pano Iye samasintha konse njira Yake yochitira izo,sanasinthe konse. Iye sangakhoze konse kusintha, chifukwa Iyendi Mulungu wosasintha. Mwawona? Zindikirani Iye anapitammbuyo momwe kwa ophunzira awiri awa, Kleopa ndi bwenzilake, pa ulendo waku Emau, ndipo anati, anazitengera kuMalemba kwa iwo, nati, “Nchifukwa chiani inu muli opusakwambiri pa kusakhulupirira kuti Mawu aliwonse anenerianalemba okhudza Mesiya anayenera kuti akwaniritsidwe?” O,tsiku lakelo!117 Yohane anachita chinthu chomwecho. “Fufuzani Malemba,muyang’ane mmbuyo, anati padzakhala pali ‘liwu la mmodziwofuulamu chipululu.’ Kodi ine ndinachokera kuti?”Mwawona?Ndizo, izo zikanapangitsa izo kumveka kwa iwo.Kulondola!118 Ziyenera kupangitsa izo kumveka lero, chinthu chimeneife tikuchiwona Mzimu Woyera ukuchichita. Iye ananenapo,“Fufuzani Malemba.” Ndipo ife…Iye akufuna kuti ife tizichitaizo lero.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 27

119 Zindikirani, Iye anayambira ndi uneneri wa Mose, Baibulolinati, “Iye, kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse,” komaIye anayamba ndi Mose. “Mneneri,” anatero Mose, “AmbuyeMulungu wanu adzaukitsa pakati pa inu anthu, pakati pa anthu.AmbuyeMulungu adzadzutsa Mneneri.”120 Tsopano Iye mwina anati, “Kleopa, ndi mzako pano,kodi Mose sananene kuti mmasiku ano Ambuye Mulunguakanadzadzutsa Mneneri? Ndipo Munthu uyu yemweiwo anamupachika, kodi Iye anakwaniritsa chiyeneretsochimenecho? Tsopano, Mose ananeneratu izi. Ndipo tsopanoinu simunakhale naye mneneri kwa mazana ndi mazana a zaka,ndipo pano Munthu uyu wauka. Ndipo kodi wotsogolera waMunthu uyu, munati anali ndani?” Mukumva izi? Ndipo anenerionse ananena za Iye, za m’badwoWake, Iye analankhula ndi iwo.Izo zedi zikanakhala zokondweretsa kuti umumvetsere Iye. Kodiinu simukanakonda kuti mumumve Iye? Ine ndikanakhumbakuti ndimumve Iye, kumumva Iye, zomwe Iye ananena kutianeneri ananena za Iyemwini, koma Iye sananene konse kuti uyoanali Iye. Iye anangowasonyeza iwo mwa uneneri. Iye anangoti,“Mneneri anati zikanati zidzachitike.”Mwawona?121 Tiyeni tingobwerera mmbuyo maminiti pang’ono, ndipotsopano tiyeni timvetsere kwa Mawu akubwerezedwamowerenga kuchokera kwa Iyemwini. Penyani pano, MawuIwoeni akubwereza Mawu a Iyemwini. Mawu IwoeniakubwerezaMawu a Iyemwini. Osati kuwauza iwo kuti Iye analiameneyo, koma kungowalola Mawu adziyankhulire Okha, ndiyeiwo anadziwa Yemwe Iye anali. Lemba la Mawu, kubwerezaMawu mu…Mawu mu thupi, kubwereza Mawu olembedwa,pokhala atatsimikiziridwa kwathunthu ndi Iyemwini. Taonanipano, tsopano tiyeni timvetsere kwa Iye akubwereza. Motani…Tsopano, ife tikudziwa kuti iwo onse anauzidwa zodzachitikamochedwa, ndizo, za kupachikidwa ndi za nkhani ya chiukitsiro,manda, monga ife tangoiwerenga. Tsopano Iye akupitamolunjika ku Mawu auneneri wa Iyemwini. Tsopano tiyenitingolingalira kuti Iye ananena izi; Iye ananena zochulukakwambiri kuposa izi, koma penyani.122 Tiyeni tinene Iye…timumve Iye akuti, “Tembenuzirani kuZakaria 11:12. Ndipo kodi sanali Mesiya woti adzagulitsidwe,malingana ndi mneneri, kwa zidutswa sate za siliva? Inumwangonena kuti Munthu uyu anagulitsidwa kwa zidutswasate za siliva. Tembenuzirani chaku…” Inu mukuwamvetsaMalemba amenewo? Zakaria 11:12. Ndiyeno Iye anati, “Kodiinu munazindikira zomwe Davide ananena mu Masalmo, Salmo41:9? Iye anaperekedwa ndi abwenzi Ake. Ndiyeno kachiwiri,mu Zakaria 13:7, Iye anasiyidwa ndi akuphunzira Ake. Ndipomu Masalmo 35:11, anatsutsidwa ndi mboni zabodza. Inumwangonena kuti Iye anali. Yesaya 53:7, Iye anali wosayankhulapamaso pa omutsutsa Ake. Yesaya 50:6, iwo anamkwapula

28 MAWU OLANKHULIDWA

Iye, mneneri anatero. Masalmo 22, Iye anali woti adzalira pamtanda, ‘Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, nchifukwa chianiInu mwandisiya Ine?’ Kodi Iye anazichita izo, dzana madzulo?Masalmo 22 kachiwiri, 18, zovala Zake zinagawidwa pakati paiwo. Kodi iwo anachita zimenezo? Ndipo Masalmo 22:7 mpaka8, ananyozedwa ndi adani Ake, mpingo. Masalmo 22 kachiwiri,panalibe fupa mu thupi Lake loti liswedwe, koma ‘iwo analasamanja Anga ndi mapazi Anga,’” Iye anatero. Atagwiriziramanja Ake kumbuyo Kwake, mosakaika, pa nthawiyo. “Yesaya53:12 anati Iye adzafa pakati pa ambanda. Yesaya 53:9 anatiIye anaikidwa limodzi ndi olemera. Masalmo 16:10 anati,‘Ine sindidzasiya moyo Wake mu gehena, ngakhalenso Inesindidzalola Mmodzi Woyera Wanga awone chivundi.’ Ndipokodi sanali Malaki 3 wotsogolera kudza kwa Munthu uyu?”O, ine ndikadakonda kumumva Iye akubwereza zimenezo.Tayang’anani pa mauneneri! Zindikirani, ndiye zoimira zonsezomwe Iye akanati anadutsamo, za Isaki, mu Genesis 22,momwe Mulungu anachitiratu mwamthunzi Isaki, momweatate Abrahamu anamutenga mwana wake yemwe, atanyamulankhuni kukwera phiri, ndipo anakamupereka mwana wakeyemwe.123 Izo zinali tsopano kuyamba kulowerera mwa iwo. Iyeanali atawauza iwo kuti anali opusa chifukwa chosayang’anapa uneneri wa tsiku limenelo. Ndipo tsopano izo zinayambakulowerera, anayamba kuwona kukwaniritsidwa kwa izi zonsezomwe zinali zitachitika mu masiku angapo apitawo, mu zakaziwiri kapena zitatu zapitazo, uneneri wotsimikiziridwa wam’badwowo. Panali apo pamene iwo anadziwa kuti Mzawowopachikidwa, Yesu, anali atakwaniritsa Mawu aliwonse a izi.O, panali apo pamene iwo anadziwa kuti Munthu uyo analiMesiya uja, kuti—kuti Iye ayenera kuti awuke kwa akufa.“Manda sakanakhoza kumugwira Iye. ‘Ine sindidzalola WoyeraWanga kuti awone chivundi.’ Palibe Mawu amodzi a uneneriomwe angakhoze kulephera konse. Ndipo Iye anaukadi.”124 “Ndiye atumiki aja ku manda mmawa uno anali kulondola.Iye wauka kwa akufa. Iye ali ndi moyo. Iye ndi Mesiya uja.”Chifukwa? Musalephere izi. “Zochita zake, utumiki Wake ndichirichonse chomwe iye anachita zatsimikiziridwa ndendendeMawu omwe mneneri anati akanadzachitika kwa tsiku lino.Izo zachitika.” Ndiye iwo anadziwa kuti uyo anali Iye, Mzawowopachikidwa. Yesu, yemwe anali atachita izo. Nzosadabwitsakuti mitima yawo inkatentha mkati mwawo pamene Iye analikuyankhula ndi iwo. Tsopano iwo anali atayenda mailosi sikisi,ndipo iyo inkawoneka ngati nthawi yaifupi.125 Ndipo pano pali chinthu china chomwe iwo anali atachita,inu mukudziwa, iwo anali atamva ulaliki wa maora sikisipa uneneri kukhala utatsimikiziridwa. Ndi zomwe Iye analikuyankhula nawo iwo munjira muja. Basi mwamsanga pamene

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 29

iwo anayamba kupita ndi msewu, Iye anapatukira umo,chifukwa Iye anali uko komwe ku Yerusalemu. Maora sikisimochedwa…kenako, mastadiya sikisite, iwo anali ali pamsewuwomwewo mailosi sikisi waku Emau. Ndicho chomwe ichochiri. Ndipo Iye anali atalalikira, uneneri wotsimikizidwa kwamaora sikisi. Musandiweruze ine pa wanga wa firii uwu,ndiye, mukuwona. Mwawona? Koma zindikirani, iwo analiatalalikira…Iye…Iwo anali atamva ulaliki wa maora sikisi pauneneri kukhala utatsimikiziridwa, utazindikiritsidwa.126 Tsopano kunali kukuyandikira cha mu nthawiyamadzulo. Inu mukudziwa, Iye ali yemweyo dzulo, lero,ndi kwanthawizonse. Panali apo pamene anatsegula masoawo kuti adziwe kuti Ahebri 13:8, Iye ali yemweyo dzulo,lero, ndi kwanthawizonse. Pa nthawi yamadzulo, zochitikazimamveka bwino ndi uneneri. Zomwe zikuchitika mu oralamakonoli zikhoza kuzindikiritsidwa mophweka ngati inumutangokhulupirira uneneri wa orali.127 “Inde, opusa, ochedwa kumvetsa, ochedwa kukhulupirira(inu mumangopitiriza kulingalira pa izi), kuti mukhulupirirezonse zomwe aneneri ananena za Mesiya, kodi izo sizikanatizichitike?” Tsopano Iye anafufuza nsonga izi mmbuyomonse ndikusonyeza zomwe mneneri ananena kuti zikanati zidzachitike.Ndiye iwo anayamba kumvetsa. Chotero Iye anati…anachitangati kuti Iye ankati azipitirira. Iwo anamukonda Munthu uyu.Iwo anati, “Inu, Inu mwatipatsa ife chinachake. Ife sitimaganizakonse izo. Iye ali wamoyo kwinakwake.” Iwo anali akulankhulandi Iye, samadziwa zimenezo. Chotero Iye…ndipo mosakaikaIye anayang’ana pa iwo mwachisoni, ndipo Iye anayambakuyenda mopitirira, koma Iye—Iye anali kuyembekezera kutiiwo amuitanire Iye. Ndicho chimene Iye akuyembekezerausikuuno, kuti inu mumuitanire Iye.128 Zindikirani, pamene ophunzira awo anamuitanira Iyeumo ku chiyanjano chawo kuzungulira gome, panali apopamene Iye anachita chinachake chimodzimodzi monga Iyeanachita kusanachitike kupachikidwa Kwake, ndipo maso awoanatseguka. Iwo anadziwa khalidwe Lake, kachitidwe Kake.Iwo anadziwa zomwe Iye ankachita, ndipo Iye anazichita izoapo chimodzimodzi monga Iye ankachitira poyamba. Ndipoiwo anati, “Ndi Iyeyu!” Ndipo mwamsanga iwo anauka kutiafuule zimenezo, ndipo Iye anasowapo. Ndipo pamene iwoanatenga maora sikisi kuti amvere kwa ulaliki uwu, mwinamaminiti twente iwo anali opepukidwa pamapazi akubwererakuti akawauze onse a iwo, “Iye wauka ndithudi. Iye ali wamoyokwenikweni.”129 Abwenzi, uku ndi kukwaniritsidwa kwa Malaki 4,Luka Woyera 17, Yohane Woyera 15, o, ochuluka kwambiri,Chivumbulutso 10, mauneneri ochuluka kwambiri omwe akhozakuzikidwa ndendende mpaka ku tsiku lino. Ndiponso mu

30 MAWU OLANKHULIDWA

Bukhu la Marko ndi Mateyu, pamene Iye anati zizindikirozazikulu izi zodabwitsa zidzawonekera mu mlengalenga,ndipo anthu akudzitcha izo mbale, mbale zowuluka, zikhoza—zikhoza kusowapo ndi mphamvu ndi liwiro la lingaliro, lunthalomwe likhoza kubweramo. Iye akhoza kulemba. Iye akhozakuyankhula, Iye akhoza kuchita china chirichonse chimene Iyeakufuna kuchichita. Lawi la Moto lalikulu, “yemweyo dzulo,lero, ndi kwanthawizonse.” Ndi zizindikiro kumabwera padziko lapansi, mapiramidi a utsi akukwera mu mlengalenga,kutali pamwamba pa kumene sikungakhoze kukhala chinyezingakhale kanthu, mailosi sate mmwamba. Ananeneratu chakandi theka izo zisanachitike, kuti izo zidzakhala mwanjiraimeneyo. Ndiye chitembenuzeni chithunzicho ndi kuwonaYemwe ali kuyang’ana pansi. Palibe Mawu amodzi omweanayamba alepherapo omwe ananenedwa, ndipo pano paliMawu olembedwa aMulungu, akutsimikizira kuti ndi Choonadi.Ndipo ndi nthawi yamadzulo kachiwiri. Ine ndikudabwangati Iye angabwere, mwa chisomo, usikuuno ndikudzachitachinachake tsopanomonga Iye ankachitira kumbuyo uko. Tiyenitipemphere ndi kumufunsa Iye. Zochitika zimamveka bwino ndiuneneri wotsimikiziridwa.130 Mulungu Wamphamvuzonse, tithandizeni ife. Tithandizeniife, wokondedwa Mulungu, kuti timvetse, kuti timvetse zinthuzomwe ife tiyenera kuti tizidziwe, kumvetsa Mawu Anu.Ndipo tsopano, Ambuye, ife tamvapo maulaliki tsopano kwapafupi zaka thuu sauzande, zolembedwa za mabuku. Ndipomu masiku otsiriza ano pano izo zazembera mmbuyo momwekachiwiri, ndipo tsopano kuli kuyandikira nthawi yamadzulo.Amethodisti, Abaptisti, Apresbateria, ndi ochuluka a iwokutsika kupyola mu m’badwo akhala akulankhula nanu Inu,ndipo mwina mu njira chabe ya tsiku lalikulu ili lomwesilinakhale liri ngakhale usiku kapena masana, monga mneneriananena, komamu nthawi yamadzulo kudzakhala Kuwala. Yesuanauka kuchokera mmanda ndipo anawonekera kwa Simonindi kwa akazi, ndipo anawasonyeza iwo kuti Iye anali wamoyo.Uwo unali mmawa. Ndiyeno madzulo Iye anabwerera kachiwiri.Koma Iye anayendera kwa iwo kudutsa tsikulo, akuwadzudzulaiwo chifukwa cha khungu lawo, komano Iye anazidziwitsaYekhakwa iwo mu nthawi yamadzulo.131 Mulungu, mubwere mu chiyanjano chathu usikuunochomwe ife tiri nacho pozungulira Mawu. Mulungu, izizikukhulupiriridwa mosowa lero pakati pa anthu anu, komaine ndiri othokoza kuti alipo ena omwe Inu mwawaitanandipo mwawadzodzera iwo ku Moyo Wamuyaya, ndipo Inumunati, “Onse omwe Atate andipatsa Ine adzadza.” Ndipotsopano pamene Kuwala kwa madzulo kukuwala, pameneInu mwaloleza, Ambuye, kuti pasakhale uneneri umodzi (mwamazana amene anaperekedwa) umene unayamba walepherapo

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 31

nthawi imodzi. Ndiye moona ngati izo zikuzindikiritsidwa,uyo ayenera kukhala Inu, chifukwa palibe munthu angakhozekukhala wolondola chomwecho. Chimodzimodzi mongaBaibulo, palibe munthu akanakhoza kulilemba, panalibealiyense mu danga la zaka sikisitini handiredi, alembi forteosiyana, akanakhoza kulilemba, ndipo mulibemo cholakwitsachimodzi mu Ilo.

Wokondedwa Mulungu, ine ndikupemphera kuti Inumudziwonetsere Nokha usikuuno, mwa Ahebri 13:8, kutiNdinu yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Ndipontchito zomwe Inu munkachita apo, Inu mukuzichita lero.Ndipo Inu munalonjeza izo, Inu munati, “Mu masiku otsirizaano, pamene dziko likukhala monga Sodomu ndi Gomora,chisokonezo.” Ife tikuyang’ana pa anyamata awa mochulukabasi ngati asungwana, akumavala zovala monga iwo, ndi—ndikuwaona asungwana akuyesera kumachita ngati anyamata, ndikuwaona akazi ndi amuna mu m’badwo wosokonezeka uno,kuwona zokhumbiritsa chigololo zakhala—kupembedza kwamafano. Uthenga wakankhiridwa kunja ku mbali imodzi, ndipoumaliseche uli mu mpingo wa Laodikaya. O Mulungu, ndi oralanji! Bwerani, Ambuye Yesu, mudzipange Nokha kudziwikakwa ife. Pakuti ife tikupempha izi muDzina la Yesu.132 Tsopano inu mukanali ndi mitu yanu chiweramire, masoanu atatsekedwa, ine ndikupemphani inu chinachake. Kodiinu mukukhulupirira kuti Mulungu ali pano? Kodi inumukukhulupirira zinthu Zomwe zikuchitika lero ndi uneneriukukwaniritsidwa? Kodi inu mukukhulupirira kuti YesuKhristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse? Kodiinu mukukhulupirira kuti pamene Iye anali kuno ndipoatawonetseredwa mu thupi kwa tsiku limenelo, ndi ntchitozomwe Iye ankachita uko, zinali zoti zibwerezedwe kachiwirimu tsiku lino? Mneneri ananena chomwecho. Baibulo linanenachomwecho. Malemba onse ayenera kuti akwaniritsidwe,iwo sangakhoze kulephera. Kodi anadzizindikiritsa Yekhachotani? Pa kukhala Mneneri uja yemwe Mose anamukamba.Ankadziwa zinsinsi za mmitima ya anthu. Mkazi anagwirachovala Chake, Iye anatembenuka ndipo anati, “Chikhulupirirochako chakupulumutsa Iwe.” Pamene Simoni Petro anabwerakwa Iye, Iye anamudziwa dzina lake, anamuuza iye yemwe iyeanali, omwe abambo ake anali. Ndipo Yesu wokondeka yemweuja sanafe, Iye ali wamoyo kwanthawizonse. Matamando akhalekwa Mulungu! Ndipo ine ndikukhulupirira, mu nthawi yamadzulo ino tsopano, Iyewatiyitanira ife palimodzi kachiwiri.133 O Ambuye Yesu, bwerani pakati pathu. Musatipitirire ife.Bwerani, mudzakhale utali wa usiku wonse ndi ife mpakausiku uno uthe, ndiye mutilole ife tidzapite ndi Inu mawa; ifetikhoze kukudziwani Inu mu mphamvu ya chiukitsiro Chanu,kuti chikondi Chanu ndi chisomo ndi chifundo zikhoze kukhala

32 MAWU OLANKHULIDWA

ndi ife. OMulunguWamuyaya, perekani zinthu izi. Ife tikudziwakuti Mulungu yekha basi angakhoze kupereka izi.134 Mu kachetechete wa ora lino, tiloleni ife tinene izi. Mulungu,Atate athu, thupi lathu ndi kachisi wosauka kwa Inu. Koma,Ambuye mulole chisomo Chanu choyeretsa, Mzimu WanuWoyera, ubwere tsopano. Utiyeretse ife ku kukaikira kulikonsendi chokhumudwitsa chirichonse, chopeneketsa chirichonse ndimzere uliwonse wa kusadalirika umene ukanati ukhale mwaife, kuti tikhoze kukhala afulu opanda kukaikira kumodzi;kubwerapo, kumavomereza molimbamtima monga Petro, “InundinuKhristu, yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse.”135 Ife tikukhulupirira kuti Mawu anu ali Choonadi, Ambuye.Tiloleni ife tingowona, ife tisanayambe mzere wa pempherouwu, Ambuye, dzipangeni Nokha kudziwika kwa ife. MongaInu munanena, “Momwe izo zinaliri mu masiku a Loti,”pamene Abrahamu, gulu loitanidwa—atuluke lija loyembekezeramwana wolonjezedwa, Loti anali kumusi uko akumvetseraBilly Graham wamakono ndi Oral Roberts kwa dongosolola chipembedzo lija uko, monga fuko. Koma Abraham analimwendamnjira wopanda bungwe lirilonse, gulu lapang’onochabe ili akuyenda kudutsa mdziko lomwe iye anali wotiadzalilandire. “Ndipo ofatsa adzalandira dziko lapansi.” Tsikulina, pansi pa mtengo wa mthunzi, pamene iwo anali atakhala,akupumula, Mulungu anabwera pansi mu mawonekedwe aMunthu. Angelo awiri anapita kumusi uko mu Sodomu. NdipoMulungu, mu mnofu wa munthu, anatsimikizira kuti Iye anali,Iye anati, “Abrahamu, ali kuti mkazi wako, Sarah?” Masikupang’ono zisanachitike zimenezo, iye anali Abramu; ndi S-a-r-r-a, Sarra; osati Sarah, “mfumukazi.” Ndipo Inu munamuitaniraiye dzina la ufumukazi lake, mwana wamkazi wa mfumu.Inu munamuitanira Abrahamu dzina lake, Abrahamu, tate wamafuko. Ndipo Inumunati, “Ine ndidzakuchezerani inu.”136 Mulungu, momwe mtima wa mneneri uyo uyenera kutiunalumphira! Iye anadziwa Yemwe Inu munali pomwepo.Nzosadabwitsa iye anatsuka mapazi Anu, anatulutsa chakudyachonse chimene iye anali nacho, ndi chopambana chomwe,anachiika icho pamaso Panu. Iye ankadziwa kuti ujayu analiMulungu apo. Ndiye Iye anati, “Alikuti Sarah?” ngati kuti Iyesamadziwa. Ndipo Inu…137 Abrahamu ananena kwa Iye, “Iye ali mu hema…iye ali muhema, kumbuyo Kwanu.”138 Ndipo Inu munanena zomwe zinali zoti zidzachitike.Ndipo iye, mu mtima mwake anakaikira Izo. Ndiyeno Inu—Inumunanena kwaAbrahamu, “Nchifukwa chiani Sarah anakaikiraizo, kunena mu mtima mwake, ‘Zinthu izi sizingakhozekukhala’? Kodi chiripo chirichonse chomuvuta kwambiriMulungu?”

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 33

139 O Mulungu! Yesu, Mulungu wowonetseredwa wa Mawu,Inu munati, “Monga izo zinaliri mu masiku a Sodomu,”dziko likanati lidzakhale mu chikhalidwe chimenecho basichisanachitike chiwonongeko cha dziko la Amitundu, nyengo yaAmitundu. Ndi ife pano, Achisodomu mpaka mkati! NdiyenoInu munanena kuti Mwana wa munthu, yemwe nthawizonseanali kulozeredwa ngati “mneneri,” akanadzaululidwa muora limenelo. Kwaniritsani Mawu Anu, O Mulungu. Ife, anaAnu okhulupirira, tikudikirira ndi mitima yodzipereka, kutimutipatse ife chikhulupiriro, Ambuye, kuti, pamene ife tititikhale mu mzere wa pemphero, anthu akhulupiririre. Ndinthawi yamadzulo, Atate. Mulole Kuwala kwamadzulo kwaMwana wa Mulungu (Iye yemwe Anali, ndi Yemwe Ali,ndipo Adzadza) adziwonetsere Yekha mwa uneneri umene Iyeanaupanga. MuDzina la Yesu Khristu. Ameni.140 Ine tsopano ndakonzeka ku—kuti ndipempherere odwala.Koma ndi chinthu chachilendo, momwe kuti pamene ife tiyimapano. Pano ine ndaima pano tsopano kupanga chitsutso kwapagulu, ndi omwe alumikizidwa kudutsa mfukoli, kuti Mulunguakadali Mulungu. Iye sangakhoze kulephera. Ndipo zomweIye analonjeza, izo Iye adzazichita. Iye sadzalephera konsekuchita zimenezo, chifukwa Iye analonjeza kuti adzachita izo.Chotero ine ndikhoza kuika chidaliro chaulemu mu zomweIye ananena. Chotero ine ndikuyang’anira Kudza Kwake, inendikumuyang’anira kuti Iye awonekere pa nthawi iliyonse,chifukwa Iye anati, “Mu ora lomwe inu simuli kuliganizira,”dziko silikuliganizira, “ndiye Iye adzawonekera.”141 Tsopano, monga momwe ine ndikudziwira…Ine ndiri mukachisi wanga pano, ndipo alipo anthu angapo omwe akhalapano omwe—ine ndikuwadziwa.M’baleWright, apang’ono a awaakhala panowa, awa pomwe pano, ine ndikuwadziwa. Komamulipo ochuluka a inu omwe ine sindikukudziwani. Ndipo inendiribe njira yonenera kuti Mulungu achita izi usikuuno. Ifetamuwona Iye akuchita izo kwa zaka ndi zaka zammbuyozi,koma Iye mwina sangakhoze kuzichita izo usikuuno. Inesindikudziwa. Izo ziri ndi Iye. Iye ndi wochita mwayekha. Iyeamachita zomwe Iye akufuna kuti achite. Palibe wina yemweangakhoze kumuuza Iye choti achite. Iye amakhalapo yekha,mu chifuniro Chake ndi njira Zake. Koma chifukwa chakuti Iyeanalonjeza izo, ine ndikumufunsa Iye kuti azichite izo. Osatichifukwa cha ife, kuti ife tikuzisowa izo, koma mwina chifukwacha alendo ena, kuti Mzimu Woyera ukhoze kudzodzedwa…tsopano kudzodza pa ife. Tsopano, ziribe kanthu kuti Iyeandidzodza ine mochuluka bwanji, Iye ayenera kuti akudzozeni,inunso, ndithudi, kuti mukhulupirire.142 Tsopano ine ndikufuna kuti ndikhale ndi mzere wapemphero, ndipo ndikufuna kuti ndipempherere odwalamochulukamomwe ine ndingathere. Tsopano, ife tikhozamwina

34 MAWU OLANKHULIDWA

kukhala ndi mzere, kuti tiwaitane anthu ndi kuwabweretsa iwopano, mzere wa pemphero ndi kupempherera aliyense panoyemwe akudwala, ine ndikulingalira, kuwapangitsa abale angaotumikira kuti abwere pano ndi ife, ndi kudzaika manja painu. Ife zedi tikhoza kuchita izo. Kapena mwina ife tikhozakuwapempha Atate athu, Yemwe ali Mmodzi yekhayo yemweangakhoze kukuchitirani inu chirichonse, chifukwa manja angaali basi a munthu monga inu anthu. Koma chimene chiri ndichakuti, si dzanja la munthu limene limachita zimenezo; ndiMawu a Mulungu. Chikhulupiriro mu Mawu amenewo ndichimene chimachititsa izo. Palibe chinthu cha sayansi pa izo,ndi palimodzi zopanda sayansi.143 Palibe chinthu chimodzi chomwe Mkhristu ali nacho muchida chake chiri chasayansi. Kodi inu mumadziwa zimenezo?Chikondi, chisangalalo, mtendere, kupirira-kotalika, ubwino,chifatso, unjonda, chipiriro, chikhulupiriro, Mzimu Woyera,chirichonse ndi chosawoneka ndi sayansi. Ndipo ndicho chinthuchokha chomwe chiri chenicheni chosatha. Chirichonse chimeneinu mumachiyang’ana chimabwera kuchokera ku dziko lapansindipo chimabwereranso ku dziko lapansi. Koma zinthu zomweinu simungakhoze kuziwona ndi diso lanu, koma mumaziwonaIzo zikudzifotokoza Zokha, ndilo dziko la Zamuyaya.144 Kodi inumungakhulupirire, ngati Mulungu atadziwonetseraYekha ndi kusonyeza kuti Iye ali pano wamoyo, akuchita zinthuzomwezo zomwe Iye ankachita pa chiyambi, utatha Uthengauwu, kodi inu mungalandire izo monga machiritso anu? MuloleMulungu apereke izo. Tsopano ine ndikumfunsa aliyense munyumba, ziribe kanthu kuti ndinu ndani kapena kumene inumukuchokera, ine ndikukufunsani inu kuti mungokhulupiriramwakachetechete Uthenga uwu kuti ndi Choonadi. Uwo ndiUthenga umene Mulungu ali nawo mu Baibulo Lake kwa oralino, kuti Yesu Khristu ali pano usikuuno ndipo ali wamoyo.Tsopano pafupifupi…145 Anthu nonse inu mukudziwa za ine, ndimakhala komwekuno mu mzinda kumene ine ndinaleredwerako. Ine ndilibengakhale maphunziro a sukulu ya galamala. Ndizo ndendendezoona. Ndipo inu mwandidziwa ine utali wokwanira, inendikuyembekeza kuti ine ndakhala pamaso pa inu kutindikusonyezeni inu kuti ndine woonamtima ndi wodzipereka.Ine si wachinyengo. Ngakhale onditsutsa anga samanenazimenezo. Iwo, iwo amangoti, “Ndinu—sindinu wachinyengo,koma inu mukungolakwitsa basi. Inu mukungolakwitsamwaumbuli, osati mwakufuna.” Ine sindikuganiza kuti inendikulakwitsa mwaumbuli, chifukwa Mawu a Mulunguakuchitira umboni za Uthenga wanga, ndipo Iwo ayenerakumakuuuzani inu Yemwe Iye ali. Ndipo inu mumandimvaine mwachimvekere ndikunena kuti Izo si ine, chotero ndiyeIzo ayenera kukhala ali Iye. Ndi kulondola uko? Khalani ndi

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 35

chikhulupiriro mwaMulungu ndiye. Yang’anani mbali iyi, ndipoinu mumukhulupirire Mulungu. Ngati inu mumukhulupiriraMulungu, Mulungu apereka izo kwa inu. Ngati Iye angakhozekuchita izo monga Iye ankachitira kale, ndiye Iye akadaliMulungu. Mukuzikhulupirira zimenezo?146 Inu mukukhulupirira izo? Dona wakhala apa patsogolopanga, akuyang’ana pa ine,misozi ili mumaso ake,modzipereka.Ine sindikudziwa yemwe iye ali, sindinayambe ndamuonapoiye. Ndine mlendo kwa inu. Kodi inu mukuganiza kutiMulungu akudziwa chinsinsi cha mtima wanu, zokhumbazanu, kapena tchimo lanu, kapena chirichonse chomwe ichochiri? Inu mukuganiza kuti Iye akuzidziwa? Inu mukuganizakuti Iye akhoza kuwulula kwa ine lomwe tchimo lanuliri, zomwe inu mwazichita, zomwe inu simumayenera kutimuzichita, kapena chokhumba chanu, chirichonse chomwe ichochiri? Ngati Iye angachite izo, kodi izo zingakupangeni inukumukhulupirira Iye, mukadziwa kuti izo ayenera kukhalaIyeyo? Kodi inu muzilandira izo kuti ndi Iyeyo? Si tchimo lanulimene likukuvutitsani inu; inu mwalivomereza ilo. Koma inumukufuna ubatizo wa Mzimu Woyera Wake. Inu muulandiraIwo. Ine ndawuona Iwo ukusunthira pansi kudutsa pa iye.147 Kuti inu mukhoze kudziwa kuti ine ndinali kuyang’anapa mkaziyo, iye anali kuyang’ana pa ine, ine ndikufuna kutindikusonyezeni inu Mzimu Woyera. Yang’anani kuno, apapomwe pa mkazi wamng’ono uyu wakhala apayu, mmusi pansipa phazi langali apa. Pamene ine ndinanena izo, ndi chinthuchomwecho chimene iye akuchifuna, ndiwo ubatizo wa MzimuWoyera. Inu mukukhulupirira kuti inu muulandira Iwo, mlongo?Kwezani mmwamba dzanja lanu, ndiye. Ine sindinayambendamuwonapomkaziyomumoyowanga,mwachidziwikire.148 Mukuwona bambo uyu wakhala apa ali ndi mutu wakepansi, wakhala pomwepoyo, ali ndi kolala yake yosamukwaniraiye, ndi zina zotero. Inu mukuvutika ndi vuto la ndulu.Inu mukukhulupirira kuti Mulungu akupangani inu kukhalabwino? Kwezani mmwamba dzanja lanu ngati mulandire Iwo.Chabwino,Mulungu akupatseni inu chopempha chanu.149 Bambo wamng’ono uyu wakhala apa pomwe, akufunaubatizo wa Mzimu Woyera. Iwe ukukhupirira kuti Mulunguapereka Iwo kwa iwe; bwana, uli ndi taye yako ya chingwechoyera chikulendewerammbuyo?Mulungu apereka izo.150 Munthu uyu pano akumupempherera mkazi wake. Iye alikwa amisala. Inu mukukhulupirira kuti Mulungu amuchiritsaiye, kumupanga iye kukhala bwino? Inu mukuzikhulupirira izo?Inu mukhoza kukhala nazo.151 Ndi dzanja lanu mmwamba mpaka pa mmero panu, inumukukhulupirira kutiMulungu akhoza kuchiritsa vuto lamtimalimene likukuvutitsani inu, vuto la mmimba ilo lomwe inu muli

36 MAWU OLANKHULIDWA

nalo? Inu mwakhala pamenepo, mukuvutika pakali pano. Ndichoncho? Inu mukukhulupirira kuti Iye akukuchiritsani inu?Ndiye inumukhoza kukhala nazo izo. Ameni.152 Inu mukuona Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndikwanthawizonse. Afunseni anthu amenewo, muwone ngati inendikuwadziwa iwo. Ine sindikudziwa, koma Iye akuwadziwa.Ameni. Penyani Kuwala uko pambali ya khoma kutaliko,kwazendewera apo pamunthuwakhala apoyo. Iye akuvutika ndichikhalidwe cha nsana kumbuyo kwake. Iye si wochokera kuno,iye ndi wochokera ku Georgia. Bambo Duncan, mukhulupirirendi mtima wanu wonse, Mulungu achiza vuto la nsana limenelo.Inu mukukhulupirira ndi mtima wanu wonse? Mulunguakudalitseni inu.153 Apa pali munthu kumbuyo komwe uko, ali ndi vuto lansana, akuyang’ana pa ine. Ine sindikumudziwa iye, koma iyendi Bambo Thompson. Inu mukukhulupirira? Imirirani, bwana,kumbuyo uko, chotero kuti…Ndine mlendo kwa inu. Ndikokulondola. Koma inu mwakhala pamenepo, mukupemphera.Vuto lanu la nsana lachiritsidwa tsopano. Yesu Khristuwakupangani inu kukhala bwino.154 Kudzakhala Kuwala cha mu nthawi ya madzulo.” Kodiinu simukuwona, Iye ali pano usikuuno! Iye ali INE NDINEwamkulu. Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse.Kodi inu mukukhulupirira zimenezo? Kodi inu mwakhutitsidwandi kukhudzidwa kuti uyu ndi Yesu Khristu akudzidziwitsaYekha, kudzizindikiritsa Yekhamwa uneneri?155 Musadandaule za diso. Mulungu amachiritsa odwala ndiosautsika.156 Ndi anthu angati omwe…Ndi angati ali muno, akudwala?Tiyeni tiwone manja anu. Zikungowoneka ngati ndi kukokakotero ndi kulemeletsa. Kodi aliyense wa anthu inu muli ndimakadi a pemphero? Ine sindikudziwamomwe ine ndingadutsireapa. Ine ndikufuna kuti ndikupempherereni inu, ndipo inesindikudziwa momwe ndingachitire izo. Inu mukuwona chiani,tayang’anani pa khomapo, ine ndiwatengera iwo chotanimmenemo? Bwanji ngati inu mutatenga kanjira kamodzinkukadzazitsa? Inu mukhala ndi kenako katatsekeredwa apopomwe, aliyense aima njii.157 Mvetserani, ndimveni ine. Kodi ine ndinayambandakuuzanipo inu chirichonse mu Dzina la Ambuye kupatulachimene chinadzachitika? Ndi kulondola uko? Chirichonsenthawizonse chakhala chiri cholondola. Ine sindinayambendakufunsanipo inu khobili limodzi la ndalama mu moyowanga, ndinatero ine? Palibe nthawi imodzi. Sindinayambendatengapo chopereka mu moyo wanga. Ine sindiri panopofuna ndalama. Ine sindiri pano kuti ndikunyengeni inu.Ine ndiri pano kuti ndiwonetsere Mawu a Mulungu a orali.

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 37

Ine ndakuuzani inu Choonadi, ndipo Mulungu wachitiraumboni kuti icho ndi Choonadi. Tsopano ine ndikukuuzaniinu, PAKUTI ATERO MALEMBA, kuti ngati wokhulupiriraayika manja ake pa odwala, Yesu anati, “Iwo adzachira!” Kodiinu mukukhulupirira izo? Ndiye, mu Kukhalapo kwa Mulungu,kodi inu simukukhulupirira kuti Iye achita izo pakali pano?158 Tsopano inu ikani manja anu pa wina ndi mzake,ndipo mungowagwira apo kwa miniti. Tsopano, musati—musapemphere, mungoika manja anu pa wina ndi mzake;kunja uko mu dziko. Ndipo ine, mwini, ine ndikudzigonekandekha pa mipango iyi. Tsopano ine ndikufuna inu kutimuyang’ane pa ine miniti yokha. Ndi chiani chomwe Mulunguwachisiya chosachitidwa? Tayang’anani momwe Iye, chimeneMawu omwe ife tawawerenga, mauneneri omwe ife tauzidwa,kuti Yesu amadzizindikiritsa Yekha mwa mauneneri. Tsopanotayang’anani pa orali, ndi masabata atatu otsiriza awa pomweife taliyika pamalo ora lomwe tiri kukhalamo. Tayang’ananipa zomwe ife taziwerenga, nanga bwanji aneneri abodza ndipafupi zizindikiro zomwe zikanati ziwanyenge osankhidwa.Momwe Mawu akhala akuwonetseredwa, momwe Mulungu wam’badwo uno wachititsira khungu mitima, yabodza ya anthu.Ndi momwe kuti Mulungu Mwiniwake wanena kupyoleramauneneri Ake kuti zinthu izi zikanati zidzachitike muM’badwo wa Laodikaya uno. Palibe chimene chasiyidwachosachitidwa. Mulungu ali pano Mulungu yemweyo basiyemwe ankayankhula kwa anthu aja akupita ku Emau,yemwe anadzizindikiritsa Yekha mwa mauneneri omweananeneredweratu a Iye, Iye ali pano usikuuno akuzindikiritsaKukhalapo Kwake mwa mauneneri onenedweratu a m’badwouno. Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Kodi inumungathe kukhulupirira izi? Ndiye ikani manja anu pa winandi mzake. Musadzipempherere nokha, koma mwanjira yanumuzimupempherera munthu uyo yemwe inu mwayikapo manjaanu, chifukwa iwo akukupemphererani inuyo. Tsopano onani,musakaikire.159 Ndipo tsopano ngati inu mungakhoze kuwona chimene inendiri kuyang’anapo! Ndipo inu mukudziwa ine sindikanatindiname kwa inu, nditaima pano. Ngati inu mungakhozekuwona, ndipo chikhulupiiro chanu chikanakhoza kuwukokaMzimu Woyera wawukulu uwo umene ukuyandama patalipommalere—mmalere, womwe sayansi inajambula zithunzi zake,ndi kuwuwona Iwo ukusuntha kudutsa mnyumba inoukungoyesera kuti upeze malo oti—oti uterepo, kuyeserakuti upeze malo a nangula. Ingokhulupirirani Iwo, m’balewanga. Iye wazindikiritsa izo mwa Lemba ndi zina zotero,kuti ndi kulondola. Tsopano mumupempherere modziperekamunthu uyo yemwe inu mwamuyikapo manja anu; iwoakukupemphererani inu.

38 MAWU OLANKHULIDWA

160 Wokondedwa Yesu waku Nazareti, pakuti ife tikudziwa,Ambuye, mwa Mawu, kuti Inu muli pano, mwa lonjezo kuti Inumuli pano, “Paliponse pamene awiri kapena atatu asonkhanamu Dzina Langa, pamenepo Ine ndiri pakati pa iwo. Ndipozizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira; ngatiiwo adzaika manja awo pa odwala, iwo adzachira.” Kunja kumafunde a lamya iyi, mulole Mzimu Woyera waukuluwo upitemwa osonkhana aliwonse. Mulole Kuwala Kopatulika komwekokumene tiri kuyang’anapo momwe muno mu tchalitchi,mulole Iko kugwere pa mmodzi wina aliyense, ndipo muloleiwo achiritsidwe pa nthawi ino. Ife tikumudzudzula mdani,Mdierekezi, mu Kukhalapo kwa Khristu; ife tikunena kwamdani, kuti iye wagonjetsedwa ndi—ndi kuvutika kolowammalo, imfa ya Ambuye Yesu ndi kuuka kwa chigonjetso patsiku lachitatu; ndi umboni Wake wotsimikiziridwa kuti Iyeali pano pakati pa ife usikuuno, wamoyo, zitatha zaka mazananaintini. Mulole Mzimu wa Mulungu wamoyo udzadze mtimauliwonse ndi chikhulupiriro ndi mphamvu, ndi ukoma wamachiritso kuchokera ku chiukitsiro cha Yesu Khristu, Yemweakuzindikiritsidwa pakali pano ndi Kuwala kwakukulu ukukukuzungulira mu tchalitchi, mu Kukhalapo Kwake. Mu Dzinala YesuKhristu, perekani izi kwa ulemererowaMulungu.161 Mulole mipango iyi yomwe ife tikupemphererapo,mulole iyo ipite kwa odwala ndi osautsika omwe iyoyakonzedwerako. Mulole Mzimu Woyera womwewo umene ulipano tsopano ukudzizindikiritsa Wokha, ukadzizindikiritseWokha pa wodwala aliyense yemwe iyi iti ikaikidwepo. MuloleKukhalapo kwa Mulungu kukadzadze chotero mtima wawo ndichikhulupiriro mpaka matenda a thupi lawo adzachizidwe. Iziife tikuzipempha, kwa ulemerero wa Mulungu, mu Kukhalapokwa Yesu Khristu ndi mu Dzina la Yesu Khristu, pamene ifeantchito a Yesu Khristu tikuzipempha izi. Ameni.162 Tsopano kuchokera mu mitima yanu, ine sindikusamalachomwe chinali chovuta ndi inu,mungakhoze inu, kuchokeramumtima wanu, kukhulupirira ndi mtima wanu wonse kuti Mawua Mulungu apereka kwa inu chopempha chanu? [Osonkhana ati,“Ameni.”—Mkonzi.] Ine ndikukhulupirira kuti dzanja lirilonse,monga ine ndikukhoza kuwonera, linapita mmwamba. Ngati inumukukhulupirira izo, tsopano kumbukirani, izo zatha.163 Inu kunja uko pamawaya a lamya, ngati inumwakhulupirirandi mtima wanu wonse, pamene atumiki akuyika manjapa inu, ndi okondedwa anu akuyika manja pa inu, ngatiinu mukukhulupirira ndi mtima wanu wonse kuti izozatha, izo zatha. Mzimu Woyera wawukulu, Iye ali panomu kachisi usikuuno. Ine ndinamuwona Iye akusunthirapa anthu, anadzisonyeza Yekha pano pa mbali ya khoma,ndipo anapita mmusi pa mwamuna, anabwera pansi pano ndimmwamba kudutsa mchipinda, kudziwitsa zinsinsi za mmitima,

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI 39

kuzindikiritsidwa kwa Kukhalapo Kwake, kuti asonyeze kutiIye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Iye ali pakatipathu! Iye ndiMulungu,Mulunguwosalephera konse.

164 Ndipo kodi mitima yathu siinatenthe mkati mwathu, ndipokodi iyo siikutentha tsopano, podziwa kuti tiri tsopano muKukhalapo kwa Yesu Khristu wowukitsidwa, kwa Yemwekukhale ulemerero ndi matamando kwanthawizonse; Yemweali mu chifanizo chofotokozera cha Yehova Wamphamvuzonse;Yemwe anayandama pansi mu mawonekedwe a Lawi Lamotomu chisamba choyaka, kuti akope tcheru la mneneri; Yemweanali atatsikira pa phiri, ndipo aliyense ngakhale yemweanalikhudza ilo anali woti aphedwe, kupatula Mose ndi Yoswa.Momwe zinaliri kuti Iye anawatsogolera ana a Israeli kudutsamchipululu, mu ulendo wawo, ngati choimira cha anthuoitanidwa-atuluke lero. Pano Iye ali, mwa kufufuza kwa sayansi,ngakhale kudzizindikiritsa Yekha pamaso pa sayansi. Ndipondizochita Zake zomwe ndi mwa uneneri Wake womwe, zinthuzomwe zinanenedwera za Iye kuti azichite mu tsiku lino,kuti zimupange Iye yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse,wakhala akutsimikiziridwa mwangwiro. Kodi izo si zokwanirakuti zipangitse mitima yathu itenthe mkati mwathu? Mulunguakudalitseni inu.

165 Tsopano ndi mtima umodzi, tiyeni tiime ndi kunena: inetsopano ndikumulandira Yesu Khristu ngati Mpulumutsi ndiMchiritsi. [Osonkhana akuti, “Ine tsopano ndikumulandiraYesu Khristu ngati Mpulumutsi ndi Mchiritsi.”—Mkonzi.]Ndipo mwa chisomo Chake, [“Ndipo mwa chisomo Chake,”]kuyambira ora lino mpakana, [“kuyambira ora lino mpakana,”]O Mulungu, [“O Mulungu,”] musalole kusakhulupirira[“musalole kusakhulupirira”] kulowe konse mu mtima mwanga,[“kulowe konse mu mtima mwanga,”] chifukwa ine ndawona[“chifukwa ine ndawona”] uneneri [“uneneri”] wa tsiku lino[“wa tsiku lino”] ukukwaniritsidwa. [“ukukwaniritsidwa.”] inendikukhulupirira [“ine ndikukhulupirira”] kuti Yesu Khristu[“kuti Yesu Khristu”] ali moyo [“ali moyo”] ndipo ali panotsopano [“ndipo ali pano tsopano”] akutsimikizira MawuAke [“akutsimikizira Mawu Ake”] a ora lino [“a ora lino.”]Mauneneri [“Mauneneri”] amene analembedwa a Iye [“ameneanalembedwa a Iye”] tsopano akwaniritsidwa pakati pathu.[“tsopano akwaniritsidwa pakati pathu.”] Iye ndi Mpulumutsiwanga, [“Iye ndi Mpulumutsi wanga,”] Mulungu wanga,[“Mulungu wanga”] Mfumu yanga, [Mfumu yanga,”] Zonse mu-zonse wanga. [“Zonse-mu-zonse wanga.”]

166 Wokondedwa Mulungu, mverani umboni wathu. Ndipomupereke kwa ife, tsiku ndi tsiku, Mkate wa Moyo. Ndipoife tikupereka kwa Inu matamando, O Mulungu, kuchokeramu kuya kwa mtima wathu. Ife tikukutamandani Inu, Mmodzi

40 MAWU OLANKHULIDWA

Wamphamvuyo,Mulunguwa aneneri. MuDzina la YesuKhristu.Ameni.

O, mphindi yakeyo, nthawi yakeyo!…khulupirira;Kungokhulupirira, kungokhulupirira,Zonse zitheka, khulupirira.

Tiyeni ife tiyimbe iyo monga chonchi.Tsopano ndikhulupirira, o, tsopanondikhulupirira,

Zonse nzotheka, tsopano ndikhulupirira;Tsopano ndikhulupira, o tsopanondikhulupirira,

Zonse nzotheka, tsopano ndikhulupirira.Kodi uwo ndi umboni wanu? [Osonkhana ati

“Ameni.”—Mkonzi.] Tsopano pamene ife tikuweramitsa mituyathu.

Mpaka tikomane! mpaka tikomane!Mpaka tikomane pa mapazi a Yesu;Mpaka tikomane! Mpaka tikomane!Mulungu akhale nanu mpaka tikomanenso!

[M’bale Branham akuyamba kung’ung’uza Mulungu AkhaleNdi Inu, ndiye iye akulankhulana ndi M’bale Neville—Mkonzi.]Kodi inumukufuna kuti munene chinachake? Vayle.

…pa mapazi a Yesu;Mpaka tikomane! Mpaka tikomane!Mulungu akhale nanu mpaka tikomanenso!

167 Ndi mitu yathu yoweramitsidwa. M’bale Vayle waimapano kuti atibalalitse ife mu pemphero. M’bale Lee Vayle,iye ndi mlembi wa pa kachisi pano, wa zolembedwa ndimabuku, ndi zina zotero. M’bale wofunika kwambiri, iyewakhala ali ndi ine mu misonkhano yokopa anthu yambiri.Ndikukhumba ndikanakhala nawo mwayi womulola mtumikialiyense, kuwaimitsa iwo pano ndi kulankhula kwa iwo.Inu mukumvetsa, ine ndikutsimikiza. Mtumiki aliyense, ndifeokondwa kukhala nanu pano. Amumpingo nonse, anthu amipingo yosiyana, inayonse, ndife okondwa kukhala nanu pano.Ndipo ndi moona ndi pemphero lathu kwa wina ndi mzake,“Mulungu akhale ndi inu mpaka tidzakomane kachiwiri.” Ndimitu yathu yoweramitsidwa, ndi manja athu okwezedwa, tiyenitiziiyimba iyo kachiwirimokoma kwenikweni kwaMulungu.

Mpaka tikomane! Mpaka tikomane!Mpaka tikomane pa mapazi a Yesu!Mpaka tikomane! Mpaka tikomane!Mulungu akhale nanu mpaka tikomanenso!

ZOCHITIKA ZIMAMVEKA BWINO NDI UNENERI CHA65-0801E(Events Made Clear By Prophecy)

Uthenga uwu wa M’bale William Marrion Branham, woperekedwa Lamlunguusiku, Ogasiti, 1, 1965, ku Branham Tabernacle mu Jeffersonville, Indiana,U.S.A., unatengedwa kuchokera pa matepi ojambulidwa ndi maginitonudindidwa mosachotsera mawu ena mu Chingerezi. Kumasulira kwa Chichewauku kunadindidwa ndi kugawidwa ndi Voice Of God Recordings.

CHICHEWA

©2014 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org