bukhu lophunzitsira za kangaroo , anafotokoza a namwino. khanda ndi mphatso, lipatseni mwayi mafunso...

24
Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo Nkhani ya Maliya ndi Patuma

Upload: vanduong

Post on 26-Mar-2018

219 views

Category:

Documents


1 download

TRANSCRIPT

Page 1: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo

Nkhani ya Maliya ndi Patuma

Page 2: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

KAGWIRITSIDWE NTCHITOKA BUKHULI

Pa peji iliyonse mupeza mafunso ndimalangizo okuthandizirani mu zokambirana zanu. Khalani omasuka kugwiritsa ntchito mafunso onsewa kapena ena

mwa mafunsowo pokuthandizirani kuyambitsa zokambirana ndi anthu. Muthanso kupanga mafunso anu mokhudzana ndi nkhaniyi, omwe angathe

kukuthandzirani kuti anthu omwe mukukambirana nawo athe kukamba nkhani zawo zokhudzana ndi Kangaroo.

Tsatirani ndondomeko ili m'musiyi pamene mwakumana ndi anthu oti mukambirane nawo:1. Alonjereni omwe mukufuna kukambirana nawo 2. Awuzeni zolinga za zokambirana za tsiku limenelo3. Afunseni anthu omwe mutakambirane nawo za mbiri ya moyo wawo (mwachitsanzo: ali ndi zaka zingati? Ali pa banja? Ali ndi ana angati?)4. Mukamaliza zokambirana, athokozeni anthu ndipo alimbikitsenikuti azakhalepo pa zokambirana zotsatira

Pa peji iliyonse kapena Zokambirana zonse, chitani izi:· Onetsetsani kuti anthu akuona zithunzi ndipo inu mukuwerenga malemba· Funsani okambirana nawo kuti akuuzeni zimene akuona pachithunzipo· Afotokezereni nkhani ya Maliya ndi Patuma yomwe ili pa peji imeneyo· Kambiranani ndi anthu pa zomwe zimachitika m'dera lawo pokhudza nkhaniyo

Page 3: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

Ndondomeko ya Zokambirana

Nkhani ya Maliya ndi PatumaAfotokozereni anthu nkhani ya Maliya ndi Patuma mokhudzana ndi chithunzi chomwe akuona tsiku limenelo

Mafunso OtsogoleraMusanayambe kupereka uthenga, mukuyenera kufunsa zomwe anthu akuganiza pankhani ya Maliya ndi Patuma, komanso zomwe anthu akudziwa kapena amachita m'dera lawo. Izi zikuthandizani kuti mudziwe zoyenera kutsindika.

Funsani izi:· Mukuganiza zotani pa nkhaniyi?· Mwakondamo chani mu nkhaniyi? · Mwaphunziramo chani? · Chilipo chomwe mwamva munkhaniyi chomwe mungafune mutadziwa zambiri?

UthengaMukadziwa zomwe anthu akudziwa kapena amachita, perekani uthenga oyenelera pa peji lomwe mukugwiritsa ntchito tsiku limenelo

Kuchitapo KanthuAlimbikitseni anthu kuchitapo kanthu pa uthenga omwe mwakambirana.

Page 4: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

01

Page 5: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

NKHANI YA MALIYA NDI PATUMAMaliya ndi kachiphadzuwa m'mudzi wa Kankhomba ku Machinga. Sanangokhala chiphadzuwa, kusukulunso ndiwanzeru moti tikunena pano akuchita ma phunziro a ukachenjede ku sukulu yaku Zomba. Maliya ali ndi nzake wa pa mtima, Patuma, yemwe anadziwana naye ku sekondale. Atatsiriza maphunziro ake a sekondale, Patuma anapeza mamuna dzina lake Maliko amene anachita naye ukwati woyera, ndipo Maliya anagwirizira nawo ukwatiwo. Pakali pano, Patuma ndi oyembekezera ndipo Maliya wakamuchezera.Mafunso otsogolera zokambirana

· Kodi mayi alandire chisamaliro chanji panthawi ya mimba?

· Akuyenera kudya zakudya zakasinthasintha zochokera ku magulu 6 azakudya pafupipafupi komanso mokwanira

· Akhale aukhondo pathupi pawo, panyumba pawo komanso pazakudya zonse.

· Apite ku sikelo ya amayi oyembekezera pamodzi ndi mamuna wake kosachepera kanayi kuyambira pamene wazindikira kuti ali ndi mimba kuti

akalandire uphungu ndi chithandizo choyenelera mokwanira ndi mwachangu.

· Ayenera kuyezedwa ngati ali ndi HIV, Malungo, matenda a Chindoko, kuthamanga magazi ndi matenda ena, ndikuthandizidwa moyenera ngati

apezedwa ndi matenda ali onse

· Alandire mankhwala a malungo, a njoka za m’mimba ndi oonjezera magazi.

· Atetezedwe kumatenda a malungo pogona mu net usiku ulionse tsiku lili lonse

· Azikhala ndi nthawi yopuma yokwanira (Adzipumula mokwanira kosachepera ola limodzi masana komanso maola 6 kapena 8 usiku)

· Apewe ntchito zolemetsa monga kunyamula katundu wolemera

· Adzimwa madzi a ukhondo pafupi pafupi

· Kukonzekera za kubadwa kwa mwana komanso vuto lililonse lomwe lingadze.

· Ndizofunikira bwanji kukonzekera kubereka?

· Kukonzekera kubereka kukuyenera kuyamba liti?

· Kodi mayi akonzekere bwanji pamene akuyembekezera kubereka?Akuyenera:

· Kudziwa zizindikiro zokuti nthawi yobereka yafika ndi zizindikiro zoopsya kwa amayi oyembekezera

· Kusunga ndalama zozagwiritsa ntchito pa ulendo okabereka ku chipatala

· Kukonzekeratu za momwe adzayendere kupita kukachira ku chipatala pa nthawi yake kapenanso ngati zovuta zina zitagwa mwadzidzi

· Kusankha nzawo kapena wachibale amene angadzawathandize kupita ku chipatala, ndi wina amene angadzathandize kusamala ana otsala

kunyumba

· Kukonzekera zokakhala ku chidikiliro nthawi yabwino

· Kupezeratu zovala ndi zofunda za mwana zosamalika bwino

· Kupezeratu lezala la nyuwani la pangozi ndi kulisunga mosamala

· Mabanja kapena achibale akuyenera kuthandiza bwanji amayi oyembekezera kuti akhale ndi thanzi?

· Alimbikitse mayi kupita kusikelo munthawi yoyenera

· Akonzekere kuthandiza mayi ntchito zolemetsa zapakhomo.

· Kukonzekera za kupeza chithandizo chakuchipatala pamene chafunukirapo ngakhale mwadzidzidzi.

· Kuthandizira kukonza zakudya zakasinthasintha kwa mayi oyembekezera.Kupereka zofunikira zonse

01

Page 6: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

02

Page 7: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

Pamene Maliko ndi Patuma anazindikira kuti akuyembekezera, banja lawo linali lokondwa zedi chifukwa izi zinachitika patangopita miyezi yochepa chilowereni m'banja. Maliko anali mamuna wachikondi ndipo anamusamalira Patuma mwachikondi. Maliko amapita limodzi ndi Patuma ku sikelo ya amayi oyembekezera ndikulandilira limodzi uphungu onse oyenera. Ku chipatala a namwino anawalimbikitsa kuti apitilize kukondana, komanso kupitira ku sikelo limodzi chifukwa, “bambo akamapita ndi amai ku sikelo ya amayi oyembekezera, zimathandiza kuti onse adziwe zoyenera kuchita monga madyedwe oyenera, kuyezetsa magazi, kulandira mankhwala oteteza ku Malungo, akatemela oyenera komanso uphungu ofunikira. Wina akaiwala, amakumbutsa mzake”, anafotokoza a namwino.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso otsogolera zokambirana· Maganizo anu ndiotani pa Maliko ndi Patuma?· Inu amuna anu amakupelekezani ku chipatala? Chifukwa chani amakupelekezani/sakupelekezani?· Pali zikhulupiliro zina zilizonse zomwe zimapangitsa kuti abambo asamatenge nawo mbali pa thanzi lamayi ndi mwana pamene amayi ali

oyembekezera? · Tafotokozani ubwino opita kusikelo motsatira ndondomeko pamene amayi ali oyembekezera?

· Mayi amalandira zithandizo zonse moyenera ndi mokwanira bwino ngati atsatira ndondomeko yasikelo komanso kuyamba sikelo m'miyezi itatu yoyamba.

· Thanzi la mayi ndi mwana oyembekezeredwa limapimidwa pafupipafupi.· Mayi amathandizidwa moyenera pavuto lililonse limene ladza kuti mwana obadwayo akhale wathanzi.· Amaphunzitsidwa ndi kulimbikitsidwa kukhala moyo wathanzi poyembekezera mwana · Amakonzekeretsedwa za chisamaliro cha mwana ngakhale mwanayo atabadwa masiku osakwana.· Amalandira makatemera onse mwandondomeko kuti athandizire kupewa matenda kwa mayi ndi mwana obadwayo.

· Pali ubwino wanji oti abambo azipita limodzi ku sikelo ndi amayi? · Bambo ndi mayi amalangizidwa pamodzi zakukhala moyo wathanzi panthawi ya mimba.· Bambo amamvetsetsa za momwe thanzi la mayi limayendera panthawi ya mimba ndipo ndikosavuta kupangira limodzi dongosolo la banja

lawo makamaka pa nkhani zakulera.· Abambo amazindikira za zofunikira za uchembere wabwino ndipo amapereka chithandizo chokwanira kwa mayi ndi mwana obadwayo

· zinthu zofunikira kwambiri kuzidziwa banja likakhala loyembekezera· Kupita ku sikelo mwachangu komanso mwandondomeko ndi kutsatira malangizo onse.· Kuzindikira mavuto adzidzidzi ndi kuchitapo kanthu mwamsanga· Kukonzekera kubadwa kwa mwana moyenera ngakhale mwanayo atabadwa masiku osakwana

02

Page 8: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

03

Page 9: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

Tsiku lina ali m'mwezi wachisanu ndi itatu(8) chiyimireni, Patuma anayamba kumva kudwala. Maliko pokhala mamuna wachikondi, sanachedwe kumutengera mkazi wake kuchipatala kuti akathandizidwe moyenera. Ngakhale kuti ku sikelo ya amai oyembekezera anaphunzira zambiri kuphatikizapo nkhani yakubereka mwana masiku asanakwane, izi sanaziyembekezere kuti zingawachitikire iwo. Atafika kuchipatala, anapititsidwa ku chipinda cha amayi oyembekezera ndipo anauzidwa kuti ali ndi zizindikiro zoti atha kubereka nthawi ina iliyonse. Patapita maola ochepa, Patuma anabereka mwana wamamuna.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni MwayiMafunso Otsogolera Zokambirana

· Kodi zizindikiro zokuti matenda ayamba ndi ziti?

Zizindikiro zokuti matenda ayamba kwa amayi oyembekezera· Kutaya magazi kapena madzi ku maliseche· Kupweteka pansi pa mchombo ndi nsana· Kupotokola kwa m'mimba pafupi pafupi (pa mphindi 20 ziri zonese kapena pamphindi zochepera apo)

Amayi oyembekezera akuyenera kuthamangira ku chipatala akaona zizindikiro zimenezi

Zizindikiro zosonyeza kuti pali vuto linalake ndi mimba· Kuyera lilime ndi zikope· Kumva kutopa ndi kubanika· Kutupikana kwa miyendo, manja ndi nkhope· Mwana osamveka kugunda m'mimba

Zizindikiro zoopsya. Pitani nsanga ku chipatala mukaona zizindikiro izi:· Kumva kupweteka kwambiri mutu kapena kuchita chidima· Kutentha thupi ndi kufooka· Kupuma mofulumira kapena movutikira· Kupweteka m'mimba kwambiri· Kumva kutopa· Kutaya magazi ku maliseche

Ndi zinthu ziti zimene zimapangitsa kuti mayi abereke masiku asanakwane?· Ngakhale popanda chifukwa chirichonse mayi akhoza kubereka masiku asanakwane.· Matenda omwe adza mthupi lamayi omwe amakakhudzanso mwana m'mimba monga Malungo.· Mimba yamapasa chifukwa chakuchepa kwa malo m'chiberekero

Chofunikira kwambiri ndi kuyamba kupita ku sikelo pamene mayi wazindikira kuti ali ndi mimba kuti akapatsidwe uphungu ndi chithandizo choyenera.

03

Page 10: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

04

Page 11: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

Mwana amene anabeleka Patuma anali wamng'ono kwambiri, wasikelo yokwana 1.2kg. Maliko ndi Patuma anali okhumudwa komanso anali ndi nkhawa pa za moyo wa mwana wawo, ngakhale anali ataphunzitsidwa kale kuti izi zikhoza kuchitikira aliyense, komanso kuti ana obadwa masiku osakwana amakula ngati mwana wina aliyense. Anamwino omwe amawasamalira pamodzi ndi mwana wao anawalimbikitsa kuti asadandaule chifukwa chokuti khanda lirilonse ndi mphatso, ndipo akuyenera kukondwa ndikulipatsa chisamaliro. Anamwino anawatsimikizira kuti mwana wao ngakhale wabadwa masiku osakwna, akula bwino bwino akamusamalira mu njira ya Kangaroo. Anawaptsa uphungu wa momwe angasamalire mwanayo mu njira ya Kangaroo, ndipo anawauza kuti, “Mwanayu mudzimuika pa chifuwa panu musanavale Malaya, nayenso asavale kuti khungu lanu ndi lake likhudzane, mukatero n'kumanga nsalu pamwamba bwino lomwe kuti mwana asagwe. Imeneyo ndiye Kangaroo yo! Mwana akuyenera kukhala pa Kangaroo nthawi zonse, kufikira atakwana sikelo yoyenera ya ma kilo awiri ndi theka (2.5kg). Choncho mukuyenera kuthandizana ndi kulandirana kulera mwana wanu. Mukamusamalira mwana wanu mu njira ya Kangaroo, ndiye kuti mwamupatsa Chikondi, chisamliro, komanso tsogolo lowala.”

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Maganizo anu ndi otani pa za Kangaroo? Mukuona ngati mutha kukwanitsa kuthandiza anzanu/abale anu kusamalira mwana mu njira ya

Kangaroo? · Mu nkhaniyi a namwino akuti “Khanda ndi mphatso, lipatsidwe mwayi.” Izi mukuonangati zikutanthauza chani? Mukugwirizan nazo? · Kodi ndi ndani amene angabereke mwana osakwana masiku?

· Mzimayi wina aliyense atha kubereka mwana osakwana masiku. Sizikuthanthauza kuti amene amabeleka mwana osakwana masiku ndi olakwa, zitha kuchitikira wina aliyense.

· Kodi ndi chisamaliro chotani chimene chimaperekedwa kwa ana obadwa masiku asanakwane?· Mwanayu amabadwa ziwalo zonse za thupi lake zisanakhwime ndipo afunika kupatsidwa kutentha, chakudya, chitetezo potsatira njira ya

kangaroo.· Kangaroo ndi chiyani?

· Ndi chisamaliro chomwe chimaperekedwa kwa mwana obadwa masiku osakwana chimene mwana amayikidwa pa chifuwa pakholo lake kuti alandire kutentha, chakudya, chitetezo kuti ziwalo zake zikhwime.

· Tafotokozani ndondomeko ya kangaroo kuchokera pomwe mwana wabadwa kufikira pomwe mwana akhoza kuchoka pa kangaroo· Mwana akangobadwa amayikidwa pachifuwa cha kholo lake kuti thupi lawo likhudzane ndikugawana kutentha.· Kumuthandizira mwana kuyamwa mkaka wa m'mawere.· Kumuyang'anira ndi kumuyeza pafupipafupi. · Kukonzekeretsa ndi kulimbikitsa kholo kusamala mwana ngakhale kunyumba.

04

Page 12: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

05

Page 13: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

05

Maliya atamva kuti Patuma wabereka mwana osakwana masiku, anapita pamodzi ndi mayi ake kukamuona. Maliya anali ndi mafunso ambiri ndipo anamumvera mzakeyo chisoni kwinakunso akumunyogodola koma mosaonetsera. Anamupeza Patuma atamuika mwana wake pachifuwa kunjaku atavala malaya koma mkatimo khungu la mwana litakhudzana ndi khungu la mai wake. “Tsopano chikatere?” anafunsa Maliya. “Imeneyi ndi njira ya Kangaroo, mphatso ya pamwamba kwa mwana wanga obadwa masiku osakwana”, anayankha motero Patuma. “Imathandiza chiyani Kangaroo yo?” anafunsa Maliya. Mai a Maliya anayankhira ndikufotokoza kuti, “Ubwino wa Kangaroo ndi oti mwana amakula msanga, amatetezedwa kumatenda, bongo wake umakhwima msanga nkukhala wa nzeru, kumuyamwitsa mwana kumaphweka, mwana amamva kutenthela kwa kholo lake komanso Kangaroo imalimbikitsa chikondi pakati pa kholo ndi mwana.” Maliya anazizwa ndi mmene alaongosolera mai ake.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Mutamva nkhaniyi, maganizo anu ndi otani pa ana omwe amabadwa masiku asanakwane?· Nanga maganizo anu ndi otani pa Kangaroo?· Fotokozani ubwino wogwiritsa ntchito njira ya kangaroo kwa mwana obadwa masiku osakwana.

· Mwana amalandira chifundizi chokwanira nthawi zonse.· Mwana amadyetsedwa mokwanira.· Imalimbikitsa Chikondi cha kholo ndi mwana.· Mwana amatetezedwa kumatenda ndi mavuto osiyanasiyana.· Amatulutsidwa msanga kuchipatala chifukwa mwana amakwaniritsa msanga zifukwa zotulutsidwira mwachangu choncho amatha

kusamalira zina zapakhomo.

Page 14: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

06

Page 15: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

06

Patuma anawayalira mphasa Maliya ndi mayi ake. Mayi a Maliya anamulandira Patuma mwana ndikumunyamula motsatira ndondomeko ya Kangaroo, izi zinawadabwitsa atsikana awiriwa. Mayi a Maliya anawauza atsikanawa kuti ntchito yolera mwana mu njira ya Kangaroo ndiyothandizana. China chomwe Chinamudabwitsa Maliya ndi choti Maliko ankamuthandiza mkazi wake ntchito za pakhomo. Patuma anamufotokozera Maliya kuti Maliko anali m'nyamata wachikondi chifukwa amalandirana kufungatira mwana komanso ntchito zina za pakhomo.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana�· Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?· Udindo wa abambo ndi otani pamene mwana wabadwa masiku osakwana?

· Kupereka chilimbikitso · Kupereka zonse zofunika posamalira mwanayo· Kuthandizira ntchito zapakhomo.· Kuyika mwana pachifuwa (kangaroo)· Kuthandizira kubweleranso kuchipatala motsatira ndondomeko.

· Kodi abale ndi anthu ena a m'mudzi angachitepo chiyani pothandiza kusamalira mwana osakwana masiku?· Kupereka chilimbikitso kwa banjali· Kuthandiza ntchito zapakhomo· Kuthandizira kubweleranso kuchipatala motsatira ndondomeko.· Kuthandizira zofunikira pa moyo wa mwana.· Kuthandizira kusamalira mwana pomuyika pa kangaroo. Ndizofunikira kwambiri kuonetsetsa kuti munthu wina aliyense yemwe

akuthandiza kunyamula mwana pa Kangaroo akhale waukhondo pa thupi ndi khungu lake, komanso akhale kuti alibe matenda ena ali onse optsairana monga chimfine, chifuwa, mphere ndi matenda ena a pathupi chifukwa izi zitha kumuyika mwanayo pa chiopsyezo chotengera matendawo.

· Kodi pa chikhalidwe chathu pali zomwe zimalepheretsa kuti abambo agwire ntchito zosamalira mwana kuti akule ndi moyo wa thanzi?

Page 16: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

07

Page 17: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

07

Maliya amagwirizana ndi mayi ake kwambiri chimodzimodzi ndi bambo ake. Pamene anali kwa Patuma, amaona kuchedwa kuti anyamuke, ndipo atangonyamuka, anayamba kumunyogodola mwana wa Patuma chifukwa anali wamng'ono kwambiri. Atangoyamba kubwebwetuka, mayi ake anamuuza kuti, “shiiii! Khala chete”. Maliya anapitilizabe kunena kuti zoti kakhala ndi moyo wakaika, olo katati kakhale ndi moyo mwina kadzakhala kamuthu kakang'ono kopanda nzeru. “komanso ndiye kuti mwina samayenda bwino mmodzi wa iwowo? Kapena ndi chilango amayi?” anafunsa. Mayi a Maliya anamuuza kuti asiye kubwebwetuka zimenezo chifukwa kubereka mwana osakwana masiku sichilango. Anapitiriza kufotokoza kuti khanda lingachepe bwanji, ndi mphatso; lofunika kulipatsa mwayi okhala ndi moyo wathanzi komanso tsogolo lowala polisamalira. Atafika kunyumba, mayi a Maliya anamukhazika pansi nkumuuza kuti “Mwana wa Patumayo ndi mwana ndithu ndipo akula ndikudzakhala mwana osilirika. Zina umafunsa zija ndi nkhambakamwa zomwe anthu osazindikira amakamba”. Maliya anadabwa ndi momwe amayankhulira mayi ake. Mayi ake anamuuza kuti, “mwa ana 4 amene ndinakuberekaninu, m'modzi anabadwa osakwana masiku koma nonse muli moyo ndipo nonse ndinu osilirika chimodzi modzi”.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Maganizo anu ndi otanipa pa nkhaniyi?· Kodi inu munakakhala munkhaniyi, munakamuuza chiyani Maliya?· Ndizotheka bwanji mwana kubadwa masiku osakwana koma n'kukulampaka kudzakhala ndi tsogolo lowala?· Ndi nkhambakamwa ziti zomwe anthu amakamba mwana akabadwa osakwana masiku?· Kodi tingachitepo chiyani kuthetsa nkhambakamwa zimenezi?

Page 18: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

08

Page 19: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

08

Maliya anafunitsitsa kuti amve zinakhala bwanji kuti mayi ake abereke mwana osakwana masiku ndipo ndi ndani mwa abale ake atatuwo poti onse amaoneka alunga lunga ndipo ndi a nzeru. Mayi a Maliya anafotokoza kuti atangoyamba mwezi wachisanu ndi chiwiri (7) wa pathupi pa mwana ameneyu, iwo anayamba kumva ngati matenda ayamba. Mwayi wake bambo aMaliya anali munthu okhulupilira chipatala kwambiri. Anathamangira ku chipatala asakuyembekeza kuti nkokabereka. Koma atafika uko anabereka kamwana kolemera 1 kilo (1kg).“ Makolofe tinakhumudwa, koma achipatala anatitsimikizira kuti ndizabwinobwino,tinangofunika kumusamalira mwanayo mu njira ya kangaroo. Sizinali zophweka chifukwa anthu ambiri anayamba kutinyogodola, zokamba zinali mbwe! M'mene ukuchitira iwemu pa za mwana wa Patuma, koma bambo ako ndi achibale anandithandiza kwambiri”, anafotokoza motero

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?· Akuyenera kusamalira mwana osakwana masiku mu njira ya Kangaroo ndi ndani?

· Mayi· Makolo ndi ena onse a pakhomo· Anthu a m'mudzi atha kuthandiza kusamalira mwana obadwa osakwana masiku

· Ndimavuto ati omwe anthu omwe abereka mwana osakwana masiku amakumana nawo?· Nanga tingathandize bwanji mayi oti akukumana ndi mavuto mwatchulawa?

Page 20: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

09

Page 21: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

09

Mayi a Maliya anamufotokozera kuti ntchito yosamalira mwana osakwana masiku, maziko ake ndi chikondi chozama chomwe makolo amakhala nacho pa mwana. “Pamodzi ndi bambo ako tinachilimika usiku ndi usana kulandizana kufungatira mwanayu chifukwa tinali titauzidwa mokwanira ubwino wa Kangaroo ndipo zomwe ankanena anthu omwe anali mbuli pa za Kangaroo sitinalabade. Ife cholinga chathu chinali chokuti tipulumtse moyo wa mwana wathu wokondedwa, komanso kuti akule wa thanzi ndi wa nzeru. Tinalimbikira kutsata uphungu omwe tinapatsidwa kuchipatala, ndipo sitinafooke kuyendera kuchipatala ndi mwana wathu pamene timamusamala mu njira ya kangaroo”

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Maganizo anu ndi otani pa nkhaniyi?· Pali zikhulupiliro zina zili zonse zomwe zimapangitsa kuti abambo asamatenge nawo mbali posamalira mwana mu njira ya Kangaroo?

· Ndi nthawi ziti zimene mukuyenera kubweleranso kuchipatala pamene mukusamala mwana pa kangaroo kunyumba?

· Pitani kuchipatala tsiku limene madotolo anakulangizani.

· Thamangirani kuchipatala ngati mwaona vuto lirilonse ngakhale tsiku lobweleranso kuchipatala silinafike.

· Ndimavuto ati amene muyenera kuthamangira naye mwana kuchipatala mwachangu?

· Kutentha thupi.

· Kukomoka

· Chikasu

· Kupuma movutikira/mobanika

· Kufooka

· Kukanika kuyamwa

· Kufiira, kutupa ndi mafinya pamchombo

· Kalikonse kovuta komwe kakudabwitsani pa mwana

Page 22: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

10

Page 23: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana

10

“Amayi zikomo kuti m'modzi mwa abale anga atatuwa anabadwa masiku osakwana ndipo munamusamalira bwino mpaka kukula, koma ndi ndani chifukwa palibe amandionekera choncho”, anafunsa Maliya

Mayi a Maliya anamukumbatira mwana wawo ngati mwa Kangaroo kumene, ndikumuyankha funso lake, “Maliya mwana wanga wa pamtima, ndiwe amene unabadwa masiku osakwana. Chikondi cha atate ako ndi ine chinaonekera pa iwe. Patuma tikuyenera kumuthandiza kulera mwana amene uja kuti akule wathanzi ndinso wanzeru”.

Maliya anali odzidzimuka ndi nkhani imeneyi, ndipo anawakumbatira mayi ake ndi chimweme pozindikira Chikondi chomwe anamupatsa. Maliya analonjeza kukamuthandiza Patuma ndi kumulimbikitsa kusamalira mwana wake mu njira ya Kangaroo. Mayi a Maliya anakumbutsa mwana wawo kuti:

· Khanda ndi mphatso, lofunika kulipatsa mwayi okhala ndi moyo wathanzi ndikulisamalira kuti lidzakhale ndi tsogolo lowala.· Khanda lingachepe bwanji, ndi mphatso ndithu; mphatso siyichepa.· Khanda likabadwa masiku osakwana, lileredwe munjira ya Kangaroo· Aliyense akhoza kubereka mwana osakwana masiku.· Palibe chifukwa chenicheni chodziwika chomwe chimapangitsa kuti mwana abadwe masiku osakwana, zimangochitika. Sichilango.· Mamuna wachikondi akuyenera kuthandizana ndi mkazi wake kulera mwana munjira ya Kangaroo· Kulera mwana munjira ya Kangaroo ndi ntchito ya mudzi onse, achibale ndi anthu onse a mmudzi akuyenera kuthandizira kulera mwana obadwa

masiku asanakwane powathandiza makolowo ndi ntchito zina.

Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi

Mafunso Otsogolera Zokambirana· Maganizo anu ndi otanipa nkhaniyi?· Kodi mwana osakwana masiku atha kukula, kukhala munthu wathanzi ndi wanzeru? · Tikuyenera kuchitapo chani kuti khanda losa kwana masiku tilipatse mwayi okula mwa thanzi ndi nzeru?

Page 24: Bukhu Lophunzitsira za Kangaroo , anafotokoza a namwino. Khanda ndi Mphatso, Lipatseni Mwayi Mafunso otsogolera zokambirana